Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 3:1-23

  • Akorinto ankakondabe zinthu za mʼdziko (1-4)

  • Mulungu ndi amene amakulitsa (5-9)

    • Antchito anzake a Mulungu (9)

  • Kumanga ndi zinthu zosagwira moto (10-15)

  • Ndinu kachisi wa Mulungu (16, 17)

  • Nzeru zamʼdziko ndi zopusa kwa Mulungu (18-23)

3  Choncho abale, sindinathe kulankhula nanu ngati anthu auzimu,+ koma ngati anthu okonda zinthu za mʼdzikoli,* ngati tiana+ mwa Khristu.  Ndinakupatsani mkaka, osati chakudya chotafuna, chifukwa munali musanalimbe mokwanira. Ndipo mpaka pano simunalimbebe,+  chifukwa mukuganizabe ngati anthu amʼdzikoli.*+ Nanga ngati mukuchitirana nsanje ndiponso kukangana nokhanokha, si ndiye kuti ndinu akuthupi+ ndipo mukuyenda ngati anthu a mʼdzikoli?  Ngati wina akunena kuti: “Ine ndine wa Paulo,” ndipo wina akuti: “Ine ndine wa Apolo,”+ si ndiye kuti mukungofanana ndi anthu onse?  Kodi Apolo ndi ndani? Nanga Paulo ndi ndani? Ife tangokhala atumiki+ amene tinakuthandizani kukhala okhulupirira, mogwirizana ndi ntchito imene Ambuye anatipatsa.  Ineyo ndinadzala,+ Apolo anathirira,+ koma Mulungu ndi amene anakulitsa.  Choncho wofunika kwambiri si amene anadzala kapena amene anathirira, koma Mulungu amene amakulitsa.+  Wodzala ndi wothirira amagwira ntchito ali ndi cholinga chimodzi, koma aliyense adzalandira mphoto mogwirizana ndi ntchito yake.+  Chifukwa ndife antchito anzake a Mulungu. Inuyo ndinu munda wa Mulungu umene ukulimidwa, nyumba ya Mulungu.+ 10  Mogwirizana ndi kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu anandisonyeza, ndinayala maziko+ ngati mmene amachitira munthu waluso* pa ntchito zomangamanga. Koma amene akumanga pamaziko amenewo ndi munthu wina. Choncho aliyense asamale mmene akumangirapo. 11  Chifukwa palibe munthu wina amene angayale maziko ena kupatulapo amene anayalidwa kale, omwe ndi Yesu Khristu.+ 12  Ndiye ngati munthu akumanga pamazikowo ndi golide, siliva, miyala yamtengo wapatali, mitengo, udzu ndi ziputu, 13  ntchito ya aliyense idzadziwika kuti ndi yotani. Tsiku lina ntchitoyo idzadziwika mmene ilili, chifukwa moto ndi umene udzaonetsa zimenezo poyera.+ Motowo udzaonetsa kuti ntchito ya munthu aliyense ndi yotani. 14  Ngati zimene munthu wamanga pamazikowo zidzakhalapobe, iye adzalandira mphoto. 15  Ngati zimene wamanga zidzapsa ndi moto, ndiye kuti zake zatayika, komabe iyeyo adzapulumuka. Koma adzakhala ngati wapulumuka pamoto. 16  Kodi inu simukudziwa kuti ndinu kachisi wa Mulungu+ ndipo mzimu wa Mulungu ukukhala mkati mwanu?+ 17  Ngati munthu wina wawononga kachisi wa Mulungu, Mulungu adzamuwononga munthuyo, chifukwa kachisi wa Mulungu ndi woyera, ndipo kachisiyo ndi inuyo.+ 18  Munthu asamadzinamize. Ngati aliyense wa inu akuganiza kuti ndi wanzeru nthawi* ino, akhale wopusa kuti akhale wanzeru. 19  Kwa Mulungu nzeru zamʼdzikoli nʼzopusa, chifukwa Malemba amati: “Iye amachititsa kuti anzeru agwere mʼmisampha yawo.”+ 20  Amanenanso kuti: “Yehova* amadziwa kuti maganizo a anthu anzeru ndi opanda pake.”+ 21  Choncho pasakhale munthu wodzitama chifukwa cha anthu, popeza zinthu zonse ndi zanu, 22  kaya Paulo, Apolo, Kefa,*+ dziko, moyo, imfa, zinthu zimene zilipo kapena zimene zikubwera, zonse ndi zanu. 23  Inuyo ndinu a Khristu+ ndipo Khristu ndi wa Mulungu.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu akuthupi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu akuthupi.”
Kapena kuti, “woyangʼanira wanzeru.”
Amatchedwanso Petulo.