Kalata Yoyamba ya Petulo 1:1-25

  • Moni (1, 2)

  • Kubadwanso mwatsopano nʼkukhala ndi chiyembekezo chodalirika (3-12)

  • Mukhale oyera monga ana omvera (13-25)

1  Ine Petulo mtumwi+ wa Yesu Khristu, ndikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu, amene muli alendo mʼdzikoli, omwe mwamwazikana ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya,+ Asia ndi Bituniya. 2  Ndikulembera inu amene Mulungu Atate+ anadziwiratu za inu. Iye anakupatsani mzimu wake kuti mukhale oyera.+ Anachita zimenezi kuti mukhale omvera komanso kuti akuyeretseni ndi magazi a Yesu Khristu.+ Ndikupempha Mulungu kuti akusonyezeni chifundo chake chachikulu komanso kuti mukhale ndi mtendere. 3  Atamandike Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, yemwenso ndi Atate wake. Mulungu anatisonyeza chifundo chachikulu pamene anachititsa kuti tibadwenso mwatsopano+ nʼkukhala ndi chiyembekezo chodalirika.+ Zimenezi zinatheka chifukwa cha kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.+ 4  Anachititsa kuti tibadwenso mwatsopano kuti tikhale ndi cholowa chosawonongeka, chosadetsedwa ndiponso chosasuluka.+ Cholowa chimenechi anakusungirani kumwamba.+ 5  Anasungira inuyo amene Mulungu akukutetezani ndi mphamvu yake chifukwa muli ndi chikhulupiriro. Mulungu akukutetezani kuti mudzalandire chipulumutso, ndipo chipulumutso chimenechi chidzaonekera mu nthawi yamapeto. 6  Pa chifukwa chimenechi, mukusangalala kwambiri ngakhale kuti panopa nʼkoyenera kuti muvutike kwa kanthawi chifukwa cha mayesero osiyanasiyana+ amene mukukumana nawo. 7  Zimenezi zikukuchitikirani kuti chikhulupiriro chanu chidzachititse kuti mutamandidwe ndiponso kulandira ulemerero ndi ulemu, Yesu Khristu akadzaonekera.*+ Chikhulupiriro chanucho chayesedwa+ ndipo ndi chamtengo wapatali kuposa golide amene amawonongekabe ngakhale kuti anadutsa pamoto. 8  Ngakhale kuti Khristuyo simunamuonepo, mumamukonda. Ngakhale simukumuona panopa, mumamukhulupirira ndipo mukusangalala kwambiri ndi chimwemwe chodzaza tsaya, 9  popeza ndinu otsimikiza kuti chikhulupiriro chanu chidzachititsa kuti mupulumuke.+ 10  Aneneri amene analosera za kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu anakusonyezani, anafufuza za chipulumutso chimenechi mwakhama ndiponso mosamala kwambiri.+ 11  Mzimu woyera unali utaneneratu kuti Khristu+ adzavutika ndipo kenako adzalandira ulemerero. Aneneri ankafufuza zizindikiro zimene mzimu woyera* unawasonyeza zokhudza nthawi yeniyeni komanso nyengo imene zimenezi zidzachitike.+ 12  Mulungu anauza aneneriwo kuti sankadzitumikira okha, koma ankatumikira inuyo. Tsopano zinthu zimenezi zaululidwa ndi anthu omwe akulengeza uthenga wabwino kwa inu mothandizidwa ndi mzimu woyera wochokera kumwamba.+ Angelo amafunitsitsa atamvetsa zinthu zimenezi. 13  Choncho konzekeretsani maganizo anu kuti mugwire ntchito mwamphamvu.+ Mukhalebe oganiza bwino+ ndipo muziyembekezera ndi mtima wonse kukoma mtima kwakukulu kumene adzakusonyezeni, Yesu Khristu akadzaonekera.* 14  Monga ana omvera, siyani kuchita zinthu motsatira zimene munkalakalaka musanadziwe Mulungu. 15  Koma mofanana ndi Woyera amene anakuitanani, inunso khalani oyera mʼmakhalidwe anu onse,+ 16  chifukwa Malemba amati: “Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.”+ 17  Ndiponso ngati mukupempha zinthu kwa Atate, amene amaweruza mopanda tsankho+ mogwirizana ndi zimene aliyense amachita, muzichita zinthu zosonyeza kuti mumaopa Mulungu+ pamene mukukhala mʼdzikoli monga alendo. 18  Mukudziwa inu kuti zinthu zimene zinakumasulani*+ ku moyo wanu wopanda phindu umene munatengera kuchokera kwa makolo anu, sizinali zinthu zotha kuwonongeka monga siliva kapena golide. 19  Koma munamasulidwa ndi magazi amtengo wapatali+ a Khristu,+ omwe ndi ofanana ndi magazi a nkhosa yopanda chilema komanso yopanda mawanga.+ 20  Zoonadi, Mulungu anasankhiratu Khristu anthu asanayambe kuberekana padziko lapansi,+ koma anaonekera pa nthawi yamapeto chifukwa cha inuyo.+ 21  Kudzera mwa iye, mukukhulupirira Mulungu+ amene anamuukitsa kwa akufa+ ndi kumupatsa ulemerero,+ nʼcholinga choti chikhulupiriro ndiponso chiyembekezo chanu zikhale mwa Mulungu. 22  Popeza mwadziyeretsa pokhala omvera choonadi cha mʼMawu a Mulungu ndipo tsopano mumakonda abale mopanda chinyengo,+ muzikondana kwambiri kuchokera mumtima.+ 23  Inuyo mwabadwanso mwatsopano+ kudzera mʼmawu a Mulungu+ wamoyo ndi wamuyaya. Simunabadwe kuchokera mumbewu yoti ikhoza kuwonongeka, koma mumbewu yomwe singawonongeke.+ 24  Pakuti “anthu onse ali ngati udzu, ndipo ulemerero wawo wonse uli ngati duwa lakutchire. Udzu umafota ndipo duwa limathothoka, 25  koma mawu a Yehova* adzakhalapo mpaka kalekale.”+ “Mawu” amenewa ndi uthenga wabwino umene unalengezedwa kwa inu.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “akadzaululika.”
Kapena kuti, “mzimu woyera umene unali mwa iwo.”
Onani mawu amʼmunsi pavesi 7.
Mʼchilankhulo choyambirira, “zinakuwombolani.”