Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto 6:1-18
6 Pamene tikugwira naye ntchito limodzi,+ tikukulimbikitsani kuti musalandire kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu nʼkuphonya cholinga cha kukoma mtimako.+
2 Chifukwa iye anati: “Pa nthawi yovomerezedwa ndinakumvera, ndipo pa tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza.”+ Ndithudi, inoyo ndi nthawi yeniyeni yovomerezedwa. Lero ndi tsiku lachipulumutso.
3 Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa, kuti anthu asapezere chifukwa utumiki wathu.+
4 Koma tikusonyeza mʼnjira iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu.+ Tikuchita zimenezi popirira zinthu zambiri, pokumana ndi mavuto, pokhala opanda zinthu zofunika, pokumana ndi zinthu zovuta,+
5 pomenyedwa, kuikidwa mʼndende,+ zipolowe, pogwira ntchito mwakhama, kusagona tulo ndiponso kukhala osadya.+
6 Tikusonyezanso zimenezi pokhala oyera, odziwa zinthu, oleza mtima,+ okoma mtima,+ potsogoleredwa ndi mzimu woyera, posonyeza chikondi chopanda chinyengo,+
7 polankhula zoona ndiponso pokhala ndi mphamvu ya Mulungu.+ Komanso tikuchita zimenezi ponyamula zida za chilungamo+ kudzanja lamanja* ndi lamanzere,*
8 popatsidwa ulemerero ndi kunyozedwa ndiponso poneneredwa zoipa ndi zabwino. Tikuonedwa ngati achinyengo koma ndife oona mtima,
9 ngati osadziwika koma ndife odziwika bwino, ngati oti tikufa* koma tikukhalabe ndi moyo,+ ngati olangidwa koma osaperekedwa kuti tikaphedwe,+
10 ngati achisoni koma osangalala nthawi zonse, ngati osauka koma olemeretsa anthu ambiri komanso ngati opanda chilichonse koma okhala ndi zinthu zonse.+
11 Takhala tikulankhula nanu inu Akorinto, ife tatsegula kwambiri* mtima wathu.
12 Ife sitikuumira pa nkhani yokusonyezani chikondi,+ koma inuyo ndi amene mukutikonda moumira.
13 Choncho ndikulankhula nanu ngati ana anga, inunso muzichita zomwezo, tsegulani kwambiri* mitima yanu.+
14 Musamangidwe mʼgoli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana.+ Pali mgwirizano wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo?+ Kapena pali kugwirizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima?+
15 Ndiponso pali mgwirizano wotani pakati pa Khristu ndi Beliyali?*+ Nanga munthu wokhulupirira* ndi wosakhulupirira angafanane pa zinthu ziti?+
16 Ndipo pali kugwirizana kotani pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano?+ Chifukwa ifeyo ndife kachisi wa Mulungu wamoyo,+ ngati mmene Mulungu ananenera kuti: “Ndidzakhala pakati pawo+ ndiponso ndidzayenda pakati pawo. Ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga.”+
17 “‘Choncho chokani pakati pawo ndipo musiyane nawo,’ watero Yehova.* ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa,’”+ “‘ndipo ndidzakulandirani.’”+
18 “‘Ndidzakhala bambo anu+ ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,’+ watero Yehova* Wamphamvuyonse.”
Mawu a M'munsi
^ Mwina zogwiritsa ntchito polimbana ndi mdani.
^ Mwina zodzitetezera.
^ Kapena kuti, “oonedwa ngati oyenera kufa.”
^ Kapena kuti, “ife tafutukula.”
^ Kapena kuti, “futukulani.”
^ Kuchokera ku mawu a Chiheberi otanthauza, “Wopanda Pake,” ndipo akunena za Satana.
^ Kapena kuti, “wokhulupirika.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.