Ekisodo 36:1-38

  • Anabweretsa zopereka zochuluka kuposa zimene zinkafunika (1-7)

  • Kumangidwa kwa chihema (8-38)

36  “Bezaleli adzagwire ntchito limodzi ndi Oholiabu komanso mwamuna aliyense waluso* amene Yehova wamupatsa nzeru ndi kuzindikira kuti adziwe mmene angagwirire ntchito zonse zopatulika mogwirizana ndi zimene Yehova walamula.”+ 2  Kenako Mose anaitana Bezaleli, Oholiabu ndi mwamuna aliyense waluso amene Yehova anaika nzeru mumtima mwake.+ Anaitana aliyense amene anadzipereka mofunitsitsa kugwira ntchitoyo.+ 3  Ndipo iwo anatenga kwa Mose zopereka zonse+ zimene Aisiraeli anabweretsa kuti azigwiritse ntchito pa utumiki wopatulika. Koma Aisiraeliwo anapitirizabe kubweretsa kwa Mose nsembe zaufulu mʼmawa uliwonse. 4  Ndiye ntchito yopatulika itayambika, anthu onse aluso anayamba kubwera mmodzimmodzi. 5  Iwo ankauza Mose kuti: “Anthu akubweretsa zinthu zambiri kuposa zimene zikufunikira pa ntchito imene Yehova walamula kuti ichitike.” 6  Choncho Mose analamula kuti alengeze mumsasa wonsewo, kuti: “Amayi ndi abambo, musabweretsenso zinthu zina kuti chikhale chopereka chopatulika.” Ndi mawu amenewa anthuwo anasiya kubweretsa zinthuzo. 7  Zinthuzo zinali zokwanira pa ntchito yonse imene ankafuna kuti ichitike ndipo zinali zambiri kuposa zimene zinkafunika. 8  Choncho anthu onse aluso+ anapanga chihema.+ Anachipanga ndi nsalu 10 zopangira tenti zopangidwa ndi ulusi wopota wabwino kwambiri, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo ndi ulusi wofiira kwambiri. Iye* anapeta akerubi pa nsaluzo.+ 9  Nsalu iliyonse inali mamita 13* mulitali ndipo mulifupi inali mamita awiri. Nsalu zonse muyezo wake unali wofanana. 10  Kenako analumikiza nsalu 5 pamodzi ndipo analumikizanso nsalu zina 5 zija pamodzi. 11  Atatero anapanga zingwe zopota zabuluu zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu imodzi pamene nsalu ziwirizo zidzalumikizane. Anachitanso chimodzimodzi mʼmphepete mwa nsalu yakumapeto kwenikweni, pamene nsaluzo zidzalumikizane. 12  Anaika zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe pansalu imodzi, ndipo anaikanso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu inayo kuti zikhale moyangʼanizana pamalo olumikizirana. 13  Pomaliza anapanga ngowe 50 zagolide nʼkulumikiza nsalu za tenti ndi ngowezo moti nsaluzo zinakhala chinsalu chimodzi chopangira chihema. 14  Ndiyeno anapanga nsalu za ubweya wa mbuzi zoyala pachihema. Anapanga nsalu 11.+ 15  Nsalu iliyonse inali mamita 13 mulitali ndipo mulifupi inali mamita awiri. Nsalu zonse 11 muyezo wake unali wofanana. 16  Kenako analumikiza nsalu 5 pamodzi komanso analumikiza nsalu zina 6 pamodzi. 17  Atatero anaika zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu yakumapeto kwenikweni, polumikizirana nsalu ziwirizi. Anaikanso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu inayo, pamalo amene nsalu ziwirizi zinalumikizana. 18  Atatero anapanga ngowe 50 zakopa zolumikizira nsaluzo kuti zikhale chinsalu chimodzi. 19  Anapanga chophimba chihemacho cha zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira ndi chophimba chinanso pamwamba pake cha zikopa za akatumbu.+ 20  Kenako anapanga mafelemu oimika+ a chihema amatabwa a mthethe.+ 21  Felemu lililonse linali mamita 4 mulitali ndipo mulifupi linali masentimita 70. 22  Felemu lililonse linali ndi zolumikizira ziwiri zoyandikana. Mafelemu onse a chihema anawapanga choncho. 23  Iwo anapanga mafelemu 20 a mbali yakumʼmwera ya chihemacho. 24  Kenako anapanga zitsulo 40 zasiliva zokhazikapo mafelemu 20 aja. Zitsulo ziwiri anaziika pansi pa felemu lililonse ndipo munalowa zolumikizira ziwiri.+ 25  Kumbali ina ya chihemacho, mbali yakumpoto anaikako mafelemu 20, 26  ndi zitsulo zake 40 zasiliva zokhazikapo mafelemuwo. Zitsulo ziwiri zinali pansi pa felemu lililonse. 27  Anapanga mafelemu 6 nʼkuwaika kumbuyo kwa chihemacho, mbali yakumadzulo.+ 28  Anapanga mafelemu awiri kuti akhale ochirikiza mʼmakona awiri akumbuyo kwa chihemacho. 29  Mafelemu amenewo anali ndi matabwa awiri ophatikiza kuyambira pansi mpaka pamwamba, pamene pali mphete yoyamba. Izi nʼzimene anachita ndi mafelemu onse ochirikiza mʼmakona. 30  Choncho anapanga mafelemu 8 ndi zitsulo 16 zasiliva zokhazikapo mafelemuwo. Zitsulo ziwiri zinali pansi pa felemu lililonse. 31  Ndiyeno anapanga ndodo zamtengo wa mthethe, ndodo 5 za mafelemu a mbali imodzi ya chihema,+ 32  ndi ndodo zinanso 5 za mafelemu a mbali ina ya chihema. Anapanganso ndodo zina 5 za mafelemu akumbuyo kwa chihema, mbali yakumadzulo. 33  Kenako anapanga ndodo yodutsa pakati pa mafelemu onse kuchokera koyambirira mpaka kumapeto. 34  Ndiyeno anakuta mafelemuwo ndi golide ndipo anapanga mphete zake zagolide zolowetsamo ndodo. Ndodozo anazikuta ndi golide.+ 35  Kenako anapanga katani+ ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Pakataniyo anapetapo+ akerubi.+ 36  Ndiyeno katani imeneyi anaipangira zipilala 4 za mtengo wa mthethe ndipo anazikuta ndi golide. Anapanganso tizitsulo tagolide tokolowekapo katani komanso zitsulo 4 zasiliva zokhazikapo zipilalazo. 37  Atatero anawomba nsalu yotchinga khomo la chihema. Nsaluyo inali ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ 38  Anapanganso zipilala zake 5 ndi tizitsulo take tokolowekapo nsalu yotchingayo. Pamwamba pa zipilalazo anakutapo ndi golide komanso tizitsulo take tolumikizira anatikuta ndi golide. Koma zitsulo zake 5 zokhazikapo zipilalazo zinali zakopa.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mwamuna aliyense wamtima wanzeru.”
Zikuoneka kuti akunena Bezaleli.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 28.” Onani Zakumapeto B14.