Salimo 11:1-7

  • Kuthawira kwa Yehova

    • “Yehova ali mʼkachisi wake wopatulika” (4)

    • Mulungu amadana ndi aliyense wokonda chiwawa (5)

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. 11  Ine ndathawira kwa Yehova.+ Ndiye nʼchifukwa chiyani mukundiuza kuti: “Thawira kuphiri ngati mbalame!  2  Onani mmene anthu oipa akungira uta,Aika mivi yawo pa chingwe cha uta,Kuti alase anthu owongoka mtima kuchokera pamalo amdima.  3  Kodi munthu wolungama angachite chiyaniMaziko achilungamo atagumulidwa?”  4  Yehova ali mʼkachisi wake wopatulika.+ Mpando wachifumu wa Yehova uli kumwamba.+ Maso ake amaona, inde maso ake* amayangʼanitsitsa ana a anthu.+  5  Yehova amayangʼanitsitsa munthu wolungama komanso munthu woipa.+Mulungu amadana ndi aliyense amene amakonda chiwawa.+  6  Oipa, iye adzawagwetsera misampha* ngati mvula.Moto ndi sulufule+ komanso mphepo yotentha zidzakhala chakumwa chawo.  7  Chifukwa Yehova ndi wolungama.+ Iye amakonda ntchito zolungama.+ Anthu owongoka mtima adzaona nkhope yake.*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “maso ake owala.”
Mabaibulo ena amati, “makala amoto.”
Kapena kuti, “adzawakomera mtima.”