Salimo 118:1-29

  • Yamikani Yehova chifukwa wapambana

    • ‘Ndinaitana Ya ndipo anandiyankha’ (5)

    • “Yehova ali kumbali yanga” (6, 7)

    • Mwala wokanidwa wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona (22)

    • “Amene akubwera mʼdzina la Yehova” (26)

118  Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.+Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.  2  Isiraeli anene kuti: “Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”  3  Anthu amʼnyumba ya Aroni tsopano anene kuti: “Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”  4  Anthu amene amaopa Yehova tsopano anene kuti: “Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”  5  Nditavutika ndinaitana Ya.*Ya anandiyankha nʼkundipititsa pamalo otetezeka.*+  6  Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.+ Munthu angandichite chiyani?+  7  Yehova ali kumbali yanga ndipo akundithandiza.+Ndidzayangʼana anthu amene amadana nane atagonja.+  8  Kuthawira kwa Yehova nʼkwabwinoKusiyana ndi kudalira anthu.+  9  Kuthawira kwa Yehova nʼkwabwinoKusiyana ndi kudalira akalonga.+ 10  Mitundu yonse ya anthu inandizungulira,Koma mʼdzina la Yehova,Ndinaithamangitsira kutali.+ 11  Mitunduyo inandizungulira, ndithu inandizungulira kumbali zonse.Koma mʼdzina la YehovaNdinaithamangitsira kutali. 12  Inandizungulira ngati njuchi,Koma inathimitsidwa mwamsanga ngati moto umene uli pakati pa minga. Mʼdzina la Yehova,Ndinaithamangitsira kutali.+ 13  Ndinakankhidwa kwambiri kuti ndigwe,Koma Yehova anandithandiza. 14  Ya ndi malo anga obisalapo komanso mphamvu yanga,Iye wakhala chipulumutso changa.+ 15  Phokoso lachisangalalo komanso chipulumutso*Likumveka mʼmatenti a anthu olungama. Dzanja lamanja la Yehova likusonyeza mphamvu zake.+ 16  Dzanja lamanja la Yehova lakwera mʼmwamba chifukwa wapambana.Dzanja lamanja la Yehova likusonyeza mphamvu zake.+ 17  Sindidzafa, koma ndidzakhala ndi moyo,Kuti ndilengeze ntchito za Ya.+ 18  Ya anandilanga mwamphamvu,+Koma sanalole kuti ndife.+ 19  Nditsegulireni mageti achilungamo.+Ndidzalowa mmenemo ndipo ndidzatamanda Ya. 20  Ili ndi geti la Yehova. Olungama adzalowa pamenepo.+ 21  Ndidzakutamandani, chifukwa munandiyankha+Ndipo munakhala chipulumutso changa. 22  Mwala umene omanga nyumba anaukanaWakhala mwala wapakona* wofunika kwambiri.+ 23  Umenewu wachokera kwa Yehova,+Ndipo ndi wodabwitsa mʼmaso mwathu.+ 24  Ili ndi tsiku limene Yehova wapanga.Tidzakondwera ndi kusangalala pa tsiku limeneli. 25  Yehova tikukupemphani, chonde tipulumutseni. Yehova, chonde tithandizeni kuti tipambane. 26  Wodalitsidwa ndi amene akubwera mʼdzina la Yehova.+Tikupempha kuti Yehova akudalitseni mʼnyumba yake. 27  Yehova ndi Mulungu.Iye amatipatsa kuwala.+ Tiyeni tikhale limodzi ndi gulu la anthu amene akupita kuchikondwerero atanyamula nthambi mʼmanja mwawo,+Mpaka kukafika panyanga za guwa lansembe.+ 28  Inu ndinu Mulungu wanga ndipo ndidzakutamandani.Ndinu Mulungu wanga ndipo ndidzakukwezani.+ 29  Yamikani Yehova,+ chifukwa iye ndi wabwino.Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi

“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Kapena kuti, “pamalo otakasuka.”
Kapena kuti, “kupambana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu wa kona.”