Salimo 147:1-20
147 Tamandani Ya!*
Kuimbira Mulungu wathu nyimbo zomutamanda nʼkwabwino,Kumutamanda nʼkosangalatsa komanso koyenera.+
2 Yehova akumanga Yerusalemu.+Akusonkhanitsa pamodzi Aisiraeli amene anapita ku ukapolo.+
3 Iye amachiritsa anthu osweka mtima,Ndipo amamanga mabala awo.
4 Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi zonse,Ndipo iliyonse amaitchula dzina lake.+
5 Ambuye wathu ndi wamkulu ndipo ali ndi mphamvu zochuluka.+Nzeru zake zilibe malire.+
6 Yehova amakweza anthu ofatsa,+Koma anthu oipa amawagwetsera pansi.
7 Imbirani Yehova nyimbo moyamikira.Imbirani Mulungu wathu nyimbo zomutamanda pogwiritsa ntchito zeze.
8 Imbirani amene amaphimba mapiri ndi mitambo,Amene amapereka mvula padziko lapansi,+Amenenso amameretsa udzu+ mʼmapiri.
9 Iye amapereka chakudya kwa zinyama,+Amapatsa ana a makwangwala chakudya chimene akulirira.+
10 Iye sachita chidwi ndi mphamvu za hatchi,+Kapena miyendo ya munthu yomwe ndi yamphamvu.+
11 Yehova amasangalala ndi anthu amene amamuopa,+Amene amayembekezera chikondi chake chokhulupirika.+
12 Lemekeza Yehova, iwe Yerusalemu.
Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni.
13 Amachititsa kuti mipiringidzo ya mageti ako ikhale yolimba.Ndipo amadalitsa ana ako.
14 Iye amabweretsa mtendere mʼdziko lako.+Ndipo amakupatsa tirigu wabwino* kwambiri.+
15 Amapereka lamulo lake padziko lapansi.Mawu ake amathamanga mofulumira kwambiri.
16 Iye amapereka sinowo* ngati ubweya wa nkhosa.+Amamwaza mame oundana ngati phulusa.+
17 Amaponya matalala ake ngati nyenyeswa za chakudya.+
Ndi ndani angapirire kuzizira kwake?+
18 Amatumiza mawu ake ndipo matalalawo amasungunuka.
Amachititsa mphepo yake kuwomba,+ ndipo madzi amayenda.
19 Yakobo amamuuza mawu ake,Ndipo Isiraeli amamuuza malangizo ake komanso zigamulo zake.+
20 Sanachite zimenezi ndi mtundu wina uliwonse,+Ndipo mitundu inayo sikudziwa zigamulo zake.
Tamandani Ya!*+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amakupatsa mafuta a tirigu.”
^ Kapena kuti, “chipale chofewa.”
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.