Salimo 3:1-8
Nyimbo ya Davide pamene ankathawa mwana wake Abisalomu.+
3 Inu Yehova, nʼchifukwa chiyani adani anga achuluka chonchi?+
Nʼchifukwa chiyani anthu ambiri akundiukira?+
2 Anthu ambiri akunena za ine* kuti:
“Mulungu samupulumutsa ameneyu.”+ (Selah)*
3 Koma inu Yehova, mumanditeteza mbali zonse+ ngati chishango,Ndinu ulemerero wanga+ komanso ndinu amene mumatukula mutu wanga.+
4 Ndidzaitana Yehova mokweza,Ndipo iye adzandiyankha mʼphiri lake loyera.+ (Selah)
5 Ine ndidzagona pansi nʼkupeza tulo,Ndipo ndidzadzuka ndili wotetezeka,Chifukwa Yehova akupitiriza kundithandiza.+
6 Sindikuopa anthu masauzandemasauzandeAmene andizungulira kumbali zonse kuti andiukire.+
7 Nyamukani, inu Yehova! Ndipulumutseni+ inu Mulungu wanga!
Mudzamenya adani anga onse pachibwano.Mudzaphwanya mano a anthu oipa.+
8 Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.+
Madalitso anu ali pa anthu anu. (Selah)