Salimo 36:1-12
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova.
36 Uchimo umalankhula mumtima mwa munthu woipa, nʼkumuuza zochita.Maso ake saona chifukwa choopera Mulungu.+
2 Iye amadziona kuti ndi wofunika kwambiri,Moti sazindikira zolakwa zake nʼkudana nazo.+
3 Mawu apakamwa pake ndi opweteka komanso achinyengo.Iye amasonyeza kuti alibe nzeru zomuthandiza kuchita zinthu zabwino.
4 Ngakhale ali pabedi lake, amakonza chiwembu kuti apweteke anzake.
Amayenda panjira yoipa,Ndipo sapewa kuchita zinthu zoipa.
5 Inu Yehova, chikondi chanu chokhulupirika chafika kumwamba.+Kukhulupirika kwanu kwafika mpaka mʼmitambo.
6 Chilungamo chanu chili ngati mapiri akuluakulu.*+Ziweruzo zanu zili ngati madzi ambiri ozama.+
Inu Yehova, mumapulumutsa munthu ndiponso nyama.+
7 Inu Mulungu, chikondi chanu chokhulupirika ndi chamtengo wapatali!+
Ana a anthu amabisala mumthunzi wa mapiko anu.+
8 Amamwa zakumwa zabwino* zamʼnyumba yanu nʼkukhuta.+Ndipo mumawachititsa kuti amwe zinthu zanu zosangalatsa zimene zimayenda ngati mtsinje.+
9 Inu ndinu kasupe wa moyo.+Chifukwa cha kuwala kochokera kwa inu, timaona kuwala.+
10 Pitirizani kusonyeza chikondi chanu chokhulupirika kwa anthu amene amakudziwani,+Ndiponso chilungamo chanu kwa anthu owongoka mtima.+
11 Musalole kuti phazi la anthu odzikweza lindiponderezeKapena kuti dzanja la anthu oipa lindithamangitse.
12 Onani, anthu ochita zoipa agwa.Awagwetsera pansi ndipo sangathenso kudzuka.+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chili ngati mapiri a Mulungu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “zamafuta.”