Salimo 56:1-13

  • Pemphero loperekedwa pa nthawi yozunzidwa

    • “Ine ndimadalira Mulungu” (4)

    • “Misozi yanga mʼthumba lanu lachikopa” (8)

    • “Kodi munthu wamba angandichite chiyani?” (4,11)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira nyimbo ya “Nkhunda Imene Sinena Kanthu Ndipo Imakhala Kutali.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene Afilisiti anamugwira ku Gati.+ 56  Ndikomereni mtima inu Mulungu, chifukwa anthu akundiukira.* Tsiku lonse amamenyana nane ndi kundipondereza.  2  Tsiku lonse adani anga amafuna kundiwakha ndi pakamwa pawo.Anthu ambiri akumenyana nane modzikuza.  3  Ndikamachita mantha,+ ndimadalira inu.+  4  Ndimadalira Mulungu, ndimamutamanda chifukwa cha mawu ake.Ine ndimadalira Mulungu, sindikuopa. Kodi munthu wamba angandichite chiyani?+  5  Tsiku lonse amasokoneza zolinga zanga.Nthawi zonse amaganiza zondivulaza.+  6  Iwo amandibisalira kuti andiukire,Nthawi zonse amaonetsetsa mmene ndikuyendera,+Pofuna kuchotsa moyo wanga.+  7  Alangeni chifukwa cha zochita zawo zoipa. Inu Mulungu, gwetsani mitundu ya anthu mutakwiya.+  8  Inu mukudziwa bwino za kuthawathawa kwanga.+ Sungani misozi yanga mʼthumba lanu lachikopa.+ Kodi misozi yanga sinalembedwe mʼbuku lanu?+  9  Pa tsiku limene ndidzapemphe kuti mundithandize, adani anga adzathawa.+ Mulungu ali kumbali yanga. Sindikukaikira zimenezi.+ 10  Ndimadalira Mulungu, ndimamutamanda chifukwa cha mawu ake.Ndimadalira Yehova, ndimamutamanda chifukwa cha mawu ake. 11  Ine ndimadalira Mulungu. Sindikuopa.+ Kodi munthu wamba angandichite chiyani?+ 12  Inu Mulungu, ine ndikuyenera kukwaniritsa zimene ndinakulonjezani.+Ndidzapereka kwa inu nsembe zoyamikira.+ 13  Chifukwa inu mwandipulumutsa* ku imfa.+Ndipo mwateteza phazi langa kuti lisapunthwe,+Kuti ndiyende pamaso pa Mulungu mʼkuwala kumene kumaunikira anthu amoyo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “akufuna kundiwakha ndi pakamwa.”
Kapena kuti, “mwapulumutsa moyo wanga.”