Salimo 73:1-28

  • Munthu woopa Mulungu anayambanso kuona zinthu moyenera

    • “Mapazi anga anangotsala pangʼono kusochera” (2)

    • “Ndinkavutika tsiku lonse” (14)

    • ‘Mpaka pamene ndinalowa mʼmalo opatulika a Mulungu’ (17)

    • Anthu oipa ali pamalo oterera (18)

    • Kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino (28)

Nyimbo ya Asafu.+ 73  Mulungu ndi wabwinodi kwa Isiraeli, kwa anthu oyera mtima.+  2  Koma ine mapazi anga anangotsala pangʼono kusochera,Mapazi anga anangotsala pangʼono kuterereka.+  3  Chifukwa ndinkachitira nsanje anthu onyada*Ndikamaona mtendere wa anthu oipa.+  4  Chifukwa samva ululu umene munthu amamva akamafa.Matupi awo amakhala athanzi.*+  5  Iwo savutika ngati mmene anthu ena amavutikira,+Ndipo sakumana ndi mavuto mofanana ndi anthu ena.+  6  Choncho kudzikuza kuli ngati mkanda mʼkhosi mwawo,+Ndipo avala chiwawa ngati malaya.  7  Maso awo akwiririka chifukwa cha kunenepa kwa nkhope yawo.*Ali ndi zinthu zambiri kuposa zimene ankalakalaka mumtima mwawo.  8  Iwo amanyodola komanso kulankhula zinthu zoipa.+ Amaopseza anthu monyada kuti awapondereza.+  9  Amalankhula ngati kuti ali kumwamba,Ndipo malilime awo akuyendayenda padziko lapansi mwamatama. 10  Choncho anthu a Mulungu amawatsatira,Ndipo amamwa madzi awo omwe ndi ambiri. 11  Iwo amanena kuti: “Mulungu angadziwe bwanji?+ Kodi Wamʼmwambamwamba amadziwa chilichonse?” 12  Ndithudi, izi nʼzimene oipa amachita, amakhala mosatekeseka nthawi zonse.+ Iwo amawonjezera chuma chawo.+ 13  Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe,Ndipo ndasamba mʼmanja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wosalakwa.+ 14  Ndinkavutika tsiku lonse,+Ndipo mʼmawa uliwonse ndinkadzudzulidwa.+ 15  Koma ndikananena zinthu zimenezi,Ndikanachitira chinyengo anthu anu.* 16  Nditayesa kuti ndimvetse zimenezi,Zinali zopweteka kwa ine 17  Mpaka pamene ndinalowa mʼmalo opatulika aulemerero a Mulungu,Ndipo ndinazindikira tsogolo lawo. 18  Ndithudi, mwawaika pamalo oterera.+ Mwawagwetsa kuti awonongeke.+ 19  Iwo awonongedwa mwadzidzidzi.+ Afika pamapeto awo modzidzimutsa ndipo atha momvetsa chisoni! 20  Inu Yehova, mofanana ndi maloto amene amaiwalika munthu akadzuka,Inunso mukadzuka mudzawakana.* 21  Koma mtima wanga unandipweteka,+Ndipo mkati mwanga* ndinamva ululu. 22  Ndinali wopanda nzeru ndipo sindinkamvetsa zinthu.Ndinali ngati nyama yosaganiza pamaso panu. 23  Koma tsopano ine ndili ndi inu nthawi zonse.Mwandigwira dzanja langa lamanja.+ 24  Mumanditsogolera ndi malangizo anu,+Ndipo pambuyo pake mudzandipatsa ulemerero.+ 25  Winanso ndi ndani kumwambako amene angandithandize? Ndipo chifukwa chakuti inu muli ndi ine, palibenso chimene ndimalakalaka padziko lapansi.+ 26  Thupi langa ndi mtima wanga zingalefuke,Koma Mulungu ndi thanthwe la mtima wanga ndiponso cholowa changa mpaka kalekale.+ 27  Ndithudi, anthu amene ali kutali ndi inu adzatheratu. Mudzawononga* aliyense amene akukusiyani pochita chigololo.*+ 28  Koma kwa ine, kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.+ Ndapanga Yehova Ambuye Wamkulu Koposa kukhala malo anga othawirako,Kuti ndilengeze za ntchito zanu zonse.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “odzitukumula.”
Kapena kuti, “Mimba zawo zimakhala zazikulu chifukwa cha kunenepa.”
Kapena kuti, “chifukwa choti zinthu zikuwayendera bwino.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mibadwo ya ana anu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mudzawanyoza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mu impso zanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mudzakhalitsa chete.”
Kapena kuti, “pochita zosakhulupirika.”