Salimo 79:1-13
Nyimbo ya Asafu.+
79 Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowa mʼdziko limene ndi cholowa chanu.+Aipitsa kachisi wanu woyera.+Yerusalemu amusandutsa bwinja.+
2 Apereka mitembo ya atumiki anu kwa mbalame kuti chikhale chakudya chawoNdipo matupi a anthu anu okhulupirika awapereka kwa zilombo zakutchire.+
3 Atsanula magazi awo ngati madzi kuzungulira Yerusalemu,Ndipo palibe aliyense amene watsala kuti awaike mʼmanda.+
4 Anthu oyandikana nafe akutinyoza,+Anthu otizungulira akutiseka komanso kutikuwiza.
5 Inu Yehova, kodi mukhala wokwiya mpaka liti? Kwamuyaya?+
Kodi mkwiyo wanu ukhala ukuyaka ngati moto mpaka liti?+
6 Tsanulirani mkwiyo wanu pa mitundu ya anthu amene sakukudziwaniKomanso pa maufumu amene saitana pa dzina lanu.+
7 Chifukwa iwo awononga mbadwa zonse za YakoboNdipo dziko lawo alisandutsa bwinja.+
8 Musatiimbe mlandu chifukwa cha zolakwa za makolo athu.+
Tisonyezeni chifundo chanu mofulumira,+Chifukwa zativuta kwambiri.
9 Tithandizeni inu Mulungu amene mumatipulumutsa,+Chifukwa cha dzina lanu laulemerero.Tipulumutseni komanso mutikhululukire* machimo athu chifukwa cha dzina lanu.+
10 Musalole kuti anthu a mitundu ina azinena kuti: “Mulungu wawo ali kuti?”+
Anthu a mitundu ina adziwe ife tikuonaKuti mwabwezera magazi a atumiki anu amene anakhetsedwa.+
11 Imvani kuusa moyo kwa mkaidi.+
Gwiritsani ntchito mphamvu zanu zazikulu* kupulumutsa anthu amene aweruzidwa kuti aphedwe.*+
12 Bwezerani anthu oyandikana nafe maulendo 7+Chifukwa choti akunyozani, inu Yehova.+
13 Mukatero, ife anthu anu komanso nkhosa zimene mukuweta,+Tidzakuyamikani mpaka kalekale.Ndipo tidzalengeza kuti inu ndi woyenera kutamandidwa ku mibadwomibadwo.+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “muphimbe.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja lanu lalikulu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kupulumutsa ana aamuna a imfa.”