Salimo 92:1-15
Nyimbo ndi Salimo la pa tsiku la Sabata.
92 Ndi bwino kuyamika inu Yehova,+Ndiponso kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, inu Wamʼmwambamwamba.
2 Ndi bwino kulengeza chikondi chanu chokhulupirika+ mʼmawa,Ndi kukhulupirika kwanu usiku,
3 Pogwiritsa ntchito choimbira cha zingwe 10 ndi choimbira cha zingwe zitatu,Komanso nyimbo zosangalatsa zoimbidwa ndi zeze.+
4 Inu Yehova mwachititsa kuti ndisangalale chifukwa cha zochita zanu.Ndimafuula mosangalala chifukwa cha ntchito za manja anu.
5 Ntchito zanu ndi zazikulu kwambiri inu Yehova!+
Maganizo anu ndi ozama kwambiri.+
6 Munthu wopanda nzeru sangadziwe zimenezi,Ndipo munthu wopusa sangamvetse izi:+
7 Anthu oipa akaphuka ngati msipuNdipo anthu onse ochita zoipa zinthu zikamawayendera bwino,Zimatero kuti awonongedwe kwamuyaya.+
8 Koma inu Yehova, ndinu wokwezeka mpaka kalekale.
9 Onani adani anu atagonjetsedwa, inu Yehova,Onani mmene adani anu adzathere,Onse ochita zoipa adzamwazikana.+
10 Koma inu mudzawonjezera mphamvu* zanga kuti zikhale ngati za ngʼombe yamphongo yamʼtchire.Khungu langa ndidzalidzoza mafuta abwino kwambiri.+
11 Maso anga adzaona adani anga atagonja.+Makutu anga adzamva za kugwa kwa anthu oipa amene amandiukira.
12 Koma olungama zinthu zidzawayendera bwino ngati mtengo wa kanjedzaNdipo adzakula kwambiri ngati mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni.+
13 Iwo anadzalidwa mʼnyumba ya Yehova,Zinthu zikuwayendera bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu.+
14 Ngakhale atakalamba* zinthu zidzapitirizabe kuwayendera bwino.+Adzakhalabe amphamvu* ndi athanzi,+
15 Ndipo adzalengeza kuti Yehova ndi wolungama.
Iye ndi Thanthwe langa,+ ndipo sachita zosalungama.
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”
^ Kapena kuti, “atachita imvi.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “onenepa.”