Mika 3:1-12
3 Ine ndinati: “Tamverani inu atsogoleri a mbadwa za YakoboNdiponso inu olamulira a nyumba ya Isiraeli.+
Kodi simukuyenera kudziwa chilungamo?
2 Koma mumadana ndi zinthu zabwino+ ndipo mumakonda zinthu zoipa.+Mumasenda khungu la anthu anga nʼkuchotsa mnofu pamafupa awo.+
3 Mumadyanso mnofu wa anthu anga,+Ndipo mumasenda khungu lawo.Mumaswa mafupa awo nʼkuwaphwanyaphwanya.+Ngati zinthu zimene zaphikidwa mumphika* komanso ngati nyama imene ili mumphika.
4 Pa nthawiyo adzafuulira Yehova kuti awathandize,Koma sadzawayankha.
Adzawabisira nkhope yake pa nthawi imeneyo,+Chifukwa cha zochita zawo zoipa.+
5 Izi nʼzimene Yehova wanena zomwe zidzachitikire aneneri amene akusocheretsa anthu a mtundu wanga.+Amene amalengeza kuti ‘Mtendere!’+ kwinaku akuluma ndi mano awo.*+Koma munthu akapanda kuika chakudya mʼkamwa mwawo, amakonzekera zokamenyana naye:
6 ‘Usiku udzakufikirani,+ koma simudzaona masomphenya.+Kuzidzakhala mdima, koma inu simudzaloseranso.
Aneneri amenewa dzuwa lidzawalowera.Ndipo mdima udzawagwera masanasana.+
7 Oona masomphenya adzachititsidwa manyazi,+Ndipo olosera adzakhumudwa.
Onsewa adzaphimba ndevu zawo zapamulomo,*Chifukwa Mulungu sadzawayankha.’”
8 Koma ine ndapatsidwa mphamvu ndi mzimu wa Yehova.Ndipo ndine wokonzeka kuchita chilungamo ndiponso kusonyeza mphamvu,Kuti ndiuze mbadwa za Yakobo za kugalukira kwawo, komanso Isiraeli za tchimo lake.
9 Tamverani izi inu atsogoleri a nyumba ya YakoboKomanso inu olamulira a nyumba ya Isiraeli,+Amene mumadana ndi chilungamo ndiponso mumapotoza zinthu zonse zowongoka,+
10 Inu amene mumapha anthu kuti mumange Ziyoni ndiponso mumachita zinthu zopanda chilungamo kuti mumange Yerusalemu.+
11 Atsogoleri amumzindawo saweruza asanalandire ziphuphu,+Ansembe ake amaphunzitsa kuti apeze malipiro,+Ndipo aneneri ake amalosera kuti apeze ndalama.+
Komatu iwo amanena kuti amadalira Yehova ndipo amati:
“Yehovatu ali nafe,+
Ndipo tsoka silidzatigwera.”+
12 Choncho chifukwa cha anthu inu,Ziyoni adzalimidwa ngati munda,Yerusalemu adzakhala mabwinja.+Ndipo phiri la nyumba* ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda zamunkhalango.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mumphika wakukamwa kwakukulu.”
^ Mabaibulo ena amati, “pamene ali ndi choti atafune.”
^ Kapena kuti, “adzaphimba pakamwa pawo.”
^ Kapena kuti, “phiri la kachisi.”