Miyambo 6:1-35

  • Kukhala wosamala pa nkhani yolonjeza kubweza ngongole ya wina (1-5)

  • “Pita kwa nyerere waulesi iwe” (6-11)

  • Munthu wopanda nzeru komanso woipa (12-15)

  • Zinthu 7 zimene Yehova amadana nazo (16-19)

  • Samalani ndi mkazi wamakhalidwe oipa (20-35)

6  Mwana wanga, ngati walonjeza kuti udzapereka ngongole ya mnzako iye akadzalephera kubweza,+Ngati wagwirana dzanja ndi mlendo pochita mgwirizano,+  2  Ngati wakodwa ndi lonjezo limene unapanga,Ngati wagwidwa ndi mawu amʼkamwa mwako,+  3  Uchite izi mwana wanga kuti udzipulumutse,Chifukwa uli mʼmanja mwa mnzako: Pita ukadzichepetse ndipo ukamuchonderere kwambiri mnzakoyo.+  4  Usalole kuti maso ako agone,Kapena kuti zikope zako ziwodzere.  5  Dzipulumutse ngati insa mʼmanja mwa wosaka,Ndiponso ngati mbalame mʼmanja mwa wosaka mbalame.  6  Pita kwa nyerere waulesi iwe,+Ukaone mmene imachitira zinthu kuti ukhale wanzeru.  7  Ngakhale kuti ilibe mtsogoleri, kapitawo, kapena wolamulira,  8  Imakonza chakudya chake mʼchilimwe,+Ndipo imasonkhanitsa chakudya chake pa nthawi yokolola.  9  Kodi waulesi iwe, ugona pamenepo mpaka liti? Kodi udzuka nthawi yanji kutulo tako? 10  Ukapitiriza kugona pangʼono, ukapitiriza katulo pangʼono,Ukapitiriza kupinda manja pangʼono kuti upume,+ 11  Umphawi wako udzabwera ngati wachifwamba,Ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.+ 12  Munthu wopanda pake komanso woipa, amangoyendayenda nʼkumalankhula mabodza.+ 13  Amatsinzinira ena diso lake,+ amachita zizindikiro ndi phazi lake ndiponso amachita zizindikiro ndi zala zake. 14  Popeza mtima wake ndi wachinyengo,Nthawi zonse amakonza ziwembu+ komanso amakhalira kuyambanitsa anthu.+ 15  Choncho tsoka lake lidzabwera mwadzidzidzi.Adzathyoledwa modzidzimutsa moti sadzachira.+ 16  Pali zinthu 6 zimene Yehova amadana nazo.Zilipo zinthu 7 zimene amanyansidwa nazo: 17  Maso odzikweza,+ lilime lonama,+ manja amene amakhetsa magazi a anthu osalakwa,+ 18  Mtima umene umakonza ziwembu,+ mapazi othamangira kukachita zoipa, 19  Mboni yachinyengo imene nthawi zonse imanena mabodza,+Komanso aliyense amene amayambitsa mikangano pakati pa abale.+ 20  Mwana wanga, uzitsatira malamulo a bambo ako,Ndipo usasiye kutsatira malangizo* a mayi ako.+ 21  Uwamange pamtima pako nthawi zonseNdipo uwamange mʼkhosi mwako. 22  Ukamayenda adzakutsogolera.Ukamagona adzakulondera.Ndipo ukadzuka, adzakuuza zochita.* 23  Chifukwa lamulolo ndi nyale,+Ndipo malangizo ndi kuwala,+Komanso kudzudzula kumene kumathandiza munthu kusintha ndi njira yakumoyo.+ 24  Zidzakuteteza kwa mkazi woipa,+Komanso ku lilime lokopa la mkazi wachiwerewere.*+ 25  Usasirire kukongola kwake mumtima mwako.+Kapena kulola kuti ukopeke ndi maso ake achikoka, 26  Munthu amafika potsala ndi mkate umodzi wokha chifukwa cha hule,+Koma mkazi wa mwini amasaka moyo wako wamtengo wapatali. 27  Kodi munthu anganyamule makala a moto pachifuwa pake, zovala zake osapsa?+ 28  Kapena kodi munthu angayende pamakala a moto, mapazi ake osapsa? 29  Nʼchimodzimodzi ndi aliyense wogona ndi mkazi wa mnzake.Aliyense wokhudza mkaziyo adzalangidwa.+ 30  Anthu sanyoza munthu wakubaNgati waba kuti apeze chakudya pamene ali ndi njala. 31  Koma akapezeka, adzabweza zinthuzo kuwirikiza ka 7.Adzapereka zinthu zonse zamtengo wapatali zamʼnyumba mwake.+ 32  Aliyense wochita chigololo ndi mkazi ndi wopanda nzeru.*Amene amachita zimenezi amadzibweretsera mavuto aakulu pa moyo wake.+ 33  Adzangodzivulaza yekha ndipo anthu adzamunyoza,+Moti kunyozeka kwake sikudzafufutika.+ 34  Chifukwa nsanje imachititsa kuti mwamuna wake akwiye kwambiri.Pomubwezera sadzamva chisoni.+ 35  Iye sadzavomera chipukuta misozi chilichonse,*Ndipo sadzapepeseka ngakhale utapereka mphatso yaikulu bwanji.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malamulo.”
Kapena kuti, “adzakupatsa malangizo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”
Kapena kuti, “ali ndi zolinga zoipa.”
Kapena kuti, “sadzavomera dipo lililonse.”