Mlaliki 8:1-17
8 Ndi ndani angafanane ndi munthu wanzeru? Ndipo ndi ndani akudziwa njira yothetsera vuto?* Nzeru za munthu zimachititsa nkhope yake kuwala ndipo nkhope yake yokwiya imasintha nʼkumaoneka bwino.
2 Ndikunena kuti: “Uzimvera malamulo a mfumu+ polemekeza lumbiro limene unachita kwa Mulungu.+
3 Usafulumire kuchoka pamaso pake,+ ndipo usayambe kuchita nawo zinthu zoipa.+ Chifukwa mfumuyo ikhoza kuchita chilichonse chimene ikufuna kuchita,
4 popeza mfumu ili ndi mphamvu yolamula.+ Ndipo ndi ndani angaifunse kuti, ‘Kodi mukuchita chiyani?’”
5 Munthu amene amatsatira malamulo sadzakumana ndi mavuto,+ ndipo munthu wa mtima wanzeru amadziwa nthawi yoyenera komanso njira yoyenera yochitira zinthu.+
6 Chifukwa mavuto a anthu ndi ambiri, zinthu zonse zizichitidwa mʼnjira yoyenera komanso pa nthawi yoyenera.+
7 Popeza palibe aliyense akudziwa zimene zidzachitike, ndiye ndi ndani angamuuze mmene zidzachitikire?
8 Palibe munthu amene ali ndi mphamvu pa mzimu* kapena amene angaletse mzimuwo kuti usachoke. Mofanana ndi zimenezi palibenso amene ali ndi mphamvu pa tsiku la imfa.+ Palibe amene amaloledwa kuchoka kunkhondo ndipo mofanana ndi zimenezi, anthu amene amachita zoipa, kuipako sikudzawalola kuti athawe.*
9 Zonsezi ndaziona ndipo mtima wanga unaganizira za ntchito iliyonse imene yachitidwa padziko lapansi pano, pa nthawi imene munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.+
10 Ndaona anthu oipa akuikidwa mʼmanda, amene ankalowa ndi kutuluka mʼmalo oyera, koma sanachedwe kuiwalika mumzinda umene ankachitiramo zinthu zoipa.+ Izinso nʼzachabechabe.
11 Chifukwa anthu ochita zoipa sanalangidwe mwamsanga,+ anthu atsimikiza mtima kuchita zoipa.+
12 Ngakhale woipa atachita zoipa maulendo 100 nʼkukhalabe ndi moyo wautali, ine ndikudziwa kuti anthu amene amaopa Mulungu woona zidzawayendera bwino, chifukwa chakuti amamuopa.+
13 Koma woipayo sizidzamuyendera bwino+ ndipo sadzatalikitsa moyo wake umene uli ngati mthunzi,+ chifukwa saopa Mulungu.
14 Pali chinthu china chachabechabe* chimene chimachitika padziko lapansi: Pali anthu olungama amene amachitiridwa zinthu ngati kuti achita zoipa,+ ndipo pali anthu oipa amene amachitiridwa zinthu ngati kuti achita zachilungamo.+ Ndikunena kuti zimenezinso nʼzachabechabe.
15 Choncho ndinauza anthu kuti ndi bwino kusangalala+ chifukwa palibe chabwino kwa munthu padziko lapansi pano kuposa kudya, kumwa ndi kusangalala. Azichita zimenezi pamene akugwira ntchito mwakhama masiku onse a moyo wake,+ amene Mulungu woona wamupatsa padziko lapansi pano.
16 Ndinatsimikiza mumtima mwanga kuti ndipeze nzeru ndiponso kuti ndione zinthu zonse* zimene zikuchitika padziko lapansi,+ mpaka kufika pomasala tulo masana ndi usiku.*
17 Ndiyeno ndinaganizira ntchito yonse ya Mulungu woona, ndipo ndinazindikira kuti anthu sangamvetse zimene zimachitika padziko lapansi pano.+ Ngakhale anthu atayesetsa bwanji sangathe kuzimvetsa. Ngakhale atanena kuti ndi anzeru kwambiri ndipo zonsezi akuzidziwa, sangathebe kuzimvetsa.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “njira yomasulirira zinthu.”
^ Kapena kuti, “mpweya; mphepo.”
^ Mabaibulo ena amati, “kuipa kwawoko sikudzawapulumutsa.”
^ Kapena kuti, “chokhumudwitsa.”
^ Kapena kuti, “ndione ntchito zonse.”
^ Mabaibulo ena amati, “anthu sagona tulo masana ndi usiku.”