Yesaya 58:1-14

  • Kusala kudya koyenera komanso kwachinyengo (1-12)

  • Kusangalala posunga Sabata (13, 14)

58  Iye anandiuza kuti: “Fuula mwamphamvu! Usabweze mawu. Kweza mawu ako ngati lipenga. Uza anthu anga za kupanduka kwawo.+A nyumba ya Yakobo uwauze machimo awo.   Amandifunafuna tsiku lililonse,Ndipo amasonyeza kuti akusangalala kudziwa njira zanga,Ngati kuti unali mtundu umene unkachita zinthu zolungamaNdiponso sunasiye chilungamo cha Mulungu wawo.+ Iwo akundipempha chiweruzo cholungama,Ngati kuti akufunitsitsa kuyandikira kwa Mulungu.+ Akunena kuti:   ‘Nʼchifukwa chiyani simukuona pamene tikusala kudya?+ Ndipo nʼchifukwa chiyani simukuona tikamadzisautsa?’+ Chifukwa chakuti pa tsiku lanu losala kudya mumachita zofuna zanu,*Ndipo mumapondereza antchito anu.+   Mukamasala kudya zotsatira zake zimakhala kukangana komanso ndewu,Ndipo mumamenya anzanu mwankhanza ndi zibakera.* Simungamasale kudya ngati mmene mukuchitira panopa nʼkumayembekezera kuti mawu anu amveka kumwamba.   Kodi kusala kudya kumene ine ndinakulamulani nʼkumeneku?Kodi likhale tsiku loti munthu azidzisautsa,Kuti aziweramitsa mutu wake ngati udzu,Ndiponso kuti aziyala chiguduli pabedi lake nʼkuwazapo phulusa? Kodi kumeneku nʼkumene mumati kusala kudya komanso tsiku losangalatsa kwa Yehova?   Ayi, kusala kudya kumene ine ndimafuna ndi uku: Kuti muchotse maunyolo amene munaika chifukwa cha kuipa mtima kwanu,Kuti mumasule zingwe za goli,+Kuti mumasule anthu oponderezedwa,+Ndiponso kuti goli lililonse mulithyole pakati.   Ndimafunanso kuti muzigawira chakudya chanu anthu anjala,+Kuti muziitanira mʼnyumba zanu anthu osauka ndi osowa pokhala,Kuti mukaona munthu wamaliseche muzimuveka+Ndiponso kuti musamadzibise kwa abale anu.   Mukatero kuwala kwanu kudzaonekera ngati mʼbandakucha,+Ndipo mudzachira mofulumira kwambiri. Chilungamo chanu chizidzayenda patsogolo panu,Ndipo ulemerero wa Yehova uzidzalondera kumbuyo kwanu.+   Pa nthawiyo mudzaitana ndipo Yehova adzayankha.Mudzafuula popempha thandizo ndipo iye adzanena kuti, ‘Ndikumva lankhulani!’ Mukachotsa goli pakati panu,Nʼkusiya kulozana zala ndi kulankhulana zopweteka,+ 10  Mukapatsa munthu wanjala zinthu zimene inuyo mukulakalaka,*+Ndiponso mukapereka zinthu zofunika kwa anthu ovutika,Kuunika kwanu kudzawala ngakhale mumdima,Ndipo mdima wanu waukulu udzakhala ngati masana.+ 11  Yehova azidzakutsogolerani nthawi zonseNdipo adzakupatsani zinthu zofunika ngakhale mʼdziko louma.+Iye adzalimbitsa mafupa anuNdipo inu mudzakhala ngati dimba lothiriridwa bwino,+Ndiponso ngati kasupe amene madzi ake saphwera. 12  Chifukwa cha inu, anthu adzamanganso mabwinja akalekale,+Ndipo mudzabwezeretsa maziko a mibadwo yakale.+ Mudzatchedwa womanga makoma ogumuka,+Ndiponso wokonza misewu kuti anthu azikhala mʼmphepete mwake. 13  Ngati chifukwa cha Sabata mukupewa* kuchita zofuna zanu* pa tsiku langa lopatulika,+Ndipo mukanena kuti Sabata ndi tsiku losangalatsa kwambiri, tsiku lopatulika la Yehova, tsiku loyenera kulemekezedwa,+Ndipo mukalilemekeza mʼmalo mochita zofuna zanu ndiponso mʼmalo molankhula zopanda pake, 14  Mukatero mudzasangalala kwambiri mwa Yehova,Ndipo ine ndidzakuchititsani kuti mukwere mʼmalo apamwamba a dziko lapansi.+ Ndidzakuchititsani kuti mudye* zochokera mʼcholowa cha Yakobo kholo lanu,+Chifukwa pakamwa pa Yehova panena.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “zokusangalatsani.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi zibakera zoipa.”
Kapena kuti, “zimene mtima wanu umalakalaka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mukubweza phazi lanu.”
Kapena kuti, “zokusangalatsani.”
Kapena kuti, “musangalale.”