Yesaya 63:1-19
63 Kodi amene akuchokera ku Edomuyu+ ndi ndani,Amene akuchokera ku Bozira+ atavala zovala zowala zamitundu yosiyanasiyana,*Amene zovala zake ndi zaulemelero,Ndiponso amene akuyenda ndi mphamvu zake zochuluka?
“Ndine, amene ndikulankhula mwachilungamo,Amene ndili ndi mphamvu zambiri zotha kupulumutsa.”
2 Nʼchifukwa chiyani zovala zanu zili zofiira,Ndipo nʼchifukwa chiyani zovala zanu zikuoneka ngati za munthu woponda mphesa mʼchoponderamo mphesa?+
3 “Moponderamo mphesa ndapondapondamo ndekha.
Palibe munthu wochokera pakati pa mitundu ya anthu amene anali nane.
Ndinapitiriza kupondaponda adani anga nditakwiya,Ndipo ndinkawapondaponda ndili ndi ukali.+
Magazi awo anawazikira pazovala zanga,Ndipo ndadetsa zovala zanga zonse.
4 Chifukwa tsiku lobwezera lili mumtima mwanga,+Ndipo chaka choti ndiwombole anthu anga chafika.
5 Ndinayangʼana koma panalibe wondithandiza.Ndinadabwa kuti palibe amene anandithandiza.
Choncho dzanja langa linandibweretsera chipulumutso,*+Ndipo mkwiyo wanga ndi umene unandithandiza.
6 Ndinapondaponda mitundu ya anthu nditakwiya,Ndinawaledzeretsa ndi ukali wanga.+Ndipo magazi awo ndinawathira pansi.”
7 Ndidzanena za ntchito za Yehova zosonyeza chikondi chake chokhulupirika,Ntchito zotamandika za Yehova,Chifukwa cha zinthu zonse zimene Yehova watichitira.+Zinthu zabwino zambiri zimene wachitira nyumba ya Isiraeli,Mogwirizana ndi chifundo chake komanso chikondi chake chokhulupirika chomwe ndi chochuluka.
8 Iye anati: “Ndithu awa ndi anthu anga, ana amene sadzachita zosakhulupirika.”*+
Choncho iye anakhala Mpulumutsi wawo.+
9 Pa nthawi yonse imene iwo ankavutika, iye ankavutikanso.+
Ndipo mthenga wake* anawapulumutsa.+
Iye anawawombola chifukwa cha chikondi komanso chifundo chake,+Ndipo nthawi zonse ankawakweza mʼmwamba komanso kuwanyamula.+
10 Koma iwo anapanduka+ nʼkumvetsa chisoni mzimu wake woyera.+
Kenako iye anakhala mdani wawo,+Ndipo anachita nawo nkhondo.+
11 Iwo anakumbukira masiku akale,Masiku a Mose mtumiki wake,
Ndipo anafunsa kuti: “Kodi amene anawatulutsa mʼnyanja+ pamodzi ndi abusa a anthu ake+ uja ali kuti?
Ali kuti amene anaika mzimu wake woyera mwa iye?+
12 Ali kuti amene anachititsa mkono wake waulemerero kuti upite ndi dzanja lamanja la Mose,+Amene anagawanitsa madzi pamaso pawo+Kuti adzipangire dzina lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale,+
13 Amene anawachititsa kuti adutse pamadzi amphamvu*Moti anayenda osapunthwa,Mofanana ndi hatchi mʼchipululu?*
14 Mofanana ndi ziweto zimene zatsetserekera kuchigwa,Mzimu wa Yehova unawachititsa kuti apume.”+
Izi ndi zimene munachita potsogolera anthu anu,Kuti mudzipangire dzina laulemerero.*+
15 Yangʼanani muli kumwamba ndipo muoneKuchokera pamalo anu okhala apamwamba, oyera ndi aulemerero.*
Kodi mtima wanu wodzipereka kwambiri ndiponso mphamvu zanu zili kuti?Kodi chikondi chanu chachikulu*+ ndi chifundo chanu+ zili kuti?
Chifukwa simukundisonyezanso zimenezi.
16 Inutu ndinu Atate wathu.+Ngakhale kuti Abulahamu sankatidziwaNdipo Isiraeli sangatizindikire,Inu Yehova ndinu Atate wathu.
Dzina lanu ndinu Wotiwombola wakalekale.+
17 Nʼchifukwa chiyani inu Yehova mukuchititsa kuti tichoke panjira zanu?
Nʼchifukwa chiyani mukuumitsa mtima wathu kuti tisakuopeni?+
Bwererani chifukwa cha atumiki anu,Mafuko omwe ndi cholowa chanu.+
18 Dzikoli linali la anthu anu oyera kwa kanthawi kochepa.
Koma adani athu apondaponda malo anu opatulika.+
19 Kwa nthawi yaitali, takhala ngati anthu amene simunawalamulirepo,Ngati anthu amene sanadziwikepo ndi dzina lanu.
Mawu a M'munsi
^ Mabaibulo ena amati, “zovala zofiira kwambiri.”
^ Kapena kuti, “linandithandiza kuti ndipambane.”
^ Kapena kuti, “zachinyengo.”
^ Kapena kuti, “mngelo amene amaonekera pamaso pake.”
^ Kapena kuti, “madzi akuya.”
^ Kapena kuti, “mʼchigwa.”
^ Kapena kuti, “lokongola.”
^ Kapena kuti, “okongola.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kubwadamuka kwa mʼmimba mwanu.”