Wolembedwa ndi Yohane 21:1-25
21 Zimenezi zitatha, Yesu anaonekeranso kwa ophunzirawo kunyanja ya Tiberiyo.* Kuonekera kwakeko kunali motere.
2 Simoni Petulo, Tomasi (amene ankatchulidwa kuti Didimo),+ Natanayeli+ wa ku Kana wa ku Galileya, ana a Zebedayo+ ndi ophunzira ake ena awiri onsewa anali pamodzi.
3 Ndiyeno Simoni Petulo anati: “Ine ndikupita kukapha nsomba.” Enawonso anati: “Ifenso tipita nawe.” Iwo anapitadi nʼkukwera ngalawa, koma mkati mwa usiku umenewo sanaphe kanthu.+
4 Koma pamene kunkacha, Yesu anaimirira mʼmbali mwa nyanja, koma ophunzirawo sanazindikire kuti anali Yesu.+
5 Kenako Yesu anati: “Ana inu, kodi muli ndi chakudya chilichonse?”* Iwo anamuyankha kuti, “Ayi!”
6 Iye anawauza kuti: “Ponyani ukonde kumbali yakudzanja lamanja kwa ngalawayo ndipo mupeza kenakake.” Choncho anaponyadi ukondewo, koma sanathenso kuukokera mungalawa chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba.+
7 Zitatero, wophunzira amene Yesu ankamukonda kwambiri uja+ anauza Petulo kuti: “Ndi Ambuye!” Simoni Petulo atamva kuti ndi Ambuye, anavala malaya ake akunja, chifukwa anali maliseche,* ndipo analumphira mʼnyanja.
8 Koma ophunzira enawo anabwera mʼngalawa yaingʼono akukoka ukonde wodzaza ndi nsomba, chifukwa sanali patali kwenikweni ndi kumtunda. Anali pa mtunda wa mamita pafupifupi 90 okha.*
9 Atafika kumtunda anaona moto wamakala ndipo panali nsomba komanso anaona mkate.
10 Yesu anawauza kuti: “Bweretsani kuno zina mwa nsomba zimene mwaphazo.”
11 Choncho Simoni Petulo analowa mʼngalawamo nʼkukokera kumtunda ukonde wodzaza nsomba zikuluzikulu zokwana 153. Koma ngakhale kuti munali nsomba zochuluka choncho, ukondewo sunangʼambike.
12 Yesu anawauza kuti: “Bwerani mudzadye chakudya chamʼmawa.” Panalibe ngakhale mmodzi mwa ophunzirawo amene analimba mtima kumufunsa kuti: “Ndinu ndani?” chifukwa ankadziwa kuti ndi Ambuye.
13 Yesu anapita kukatenga mkate nʼkuwagawira, ndipo anachitanso chimodzimodzi ndi nsomba.
14 Kameneka kanali kachitatu+ kuti Yesu aonekere kwa ophunzira akewo pambuyo poti waukitsidwa kwa akufa.
15 Atamaliza kudya chakudya chamʼmawacho, Yesu anafunsa Simoni Petulo kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine kuposa izi?” Iye anamuyankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambiri.” Iye anamuuza kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga.”+
16 Kenako anamufunsa kachiwiri kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi ine umandikonda?” Iye anamuyankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambiri.” Pamenepo anati: “Weta ana a nkhosa anga.”+
17 Anamufunsanso kachitatu kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi ine umandikonda kwambiri?” Petulo anamva chisoni kuti akumufunsa kachitatu kuti: “Kodi ine umandikonda kwambiri?” Choncho iye anati: “Ambuye, inu mumadziwa zinthu zonse. Mukudziwanso bwino kuti ndimakukondani kwambiri.” Yesu anamuuza kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga.+
18 Ndithudi ndikukuuza iwe, pamene unali mnyamata, unkavala wekha nʼkupita kumene ukufuna. Koma ukadzakalamba, udzatambasula manja ako ndipo munthu wina adzakuveka ndipo adzakunyamula nʼkupita nawe kumene iwe sukufuna.”
19 Ananena zimenezi pofuna kusonyeza mtundu wa imfa imene adzalemekeze nayo Mulungu. Atanena zimenezi, anamuuza kuti: “Pitiriza kunditsatira.”+
20 Petulo anatembenuka nʼkuona wophunzira amene Yesu ankamukonda uja+ akuwatsatira. Wophunzira ameneyu ndi amene pa chakudya chamadzulo chija anatsamira pachifuwa cha Yesu nʼkumufunsa kuti: “Ambuye, ndi ndani amene akufuna kukuperekani?”
21 Choncho atamuona, Petulo anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, nanga uyu adzachita chiyani?”
22 Yesu anati: “Ngati ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka ndidzabwere, kodi iweyo zikukukhudza bwanji? Iweyo ungopitiriza kunditsatira.”
23 Choncho zinamveka pakati pa abale kuti wophunzira ameneyu sadzamwalira. Komabe Yesu sanamuuze kuti sadzamwalira, koma ananena kuti: “Ngati ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka ndidzabwere, kodi iweyo zikukukhudza bwanji?”
24 Wophunzira ameneyu+ ndi amene akuchitira umboni zinthu zimenezi. Iyeyu ndi amenenso analemba zinthu zimenezi ndipo tikudziwa kuti umboni umene akupereka ndi woona.
25 Pali zinthu zinanso zambiri zimene Yesu anachita. Zikanakhala kuti zonse zinalembedwa mwatsatanetsatane, ndikuganiza kuti mipukutu yolembedwayo sikanakwana mʼdzikoli.+
Mawu a M'munsi
^ MʼBaibulo, “nyanja ya Tiberiyo” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Genesareti komanso nyanja ya Galileya.
^ Kapena kuti, “kodi muli ndi nsomba iliyonse.”
^ Kapena kuti, “chifukwa sanavale mokwanira.”
^ Onani Zakumapeto B14.