Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kukhulupirika Kumagwirizana ndi Zimene Timaganiza

Kukhulupirika Kumagwirizana ndi Zimene Timaganiza

Timasonyeza kuti ndife okhulupirika, osati chifukwa cha zochita kapena zolankhula zathu zokha, koma chifukwa cha zimenenso timaganiza. (Sl 19:14) N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziganizira zinthu zilizonse zoona, zofunika kwambiri, zolungama, zoyera, zachikondi, zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika. (Afi 4:8) N’zoona kuti nthawi zina sitingapeweretu kuganiza zinthu zoipa. Komabe kudziletsa kungatithandize kuti tichotse maganizo oipawo n’kuyamba kuganizira zinthu zabwino. Kukhalabe okhulupirika pa zimene timaganiza kungatithandize kuti tizichita zinthu mokhulupirika.—Mko 7:​21-23.

M’munsi mwa lemba lililonse, lembani maganizo amene muyenera kupewa:

Aro 12:3

Lu 12:15

Mt 5:28

Afi 3:13