Kodi Ndingatani Anzanga Akamandivutitsa Kusukulu?
Mutu 14
Kodi Ndingatani Anzanga Akamandivutitsa Kusukulu?
Chongani ziganizozi ngati zili zoona kapena zonama:
1. Munthu anganene kuti wavutitsidwa ngati wamenyedwa kapena kuvulazidwa basi.
□ Zoona
□ Zonama
2. Munthu anganene kuti wachitiridwa zachipongwe ngati munthu wina amamugwiragwira basi.
□ Zoona
□ Zonama
3. Atsikananso amavutitsa anzawo ndiponso kuwachitira zachipongwe.
□ Zoona
□ Zonama
4. Palibe chimene mungachite ena akamakuvutitsani kapena kukuchitirani zachipongwe.
□ Zoona
□ Zonama
ACHINYAMATA ambiri amakhala mwamantha chifukwa chovutitsidwa ndi anzawo kusukulu. Mnyamata wina, dzina lake Ryan, anati: “Timapita kusukulu pabasi, ndipo timayenda mphindi 15, koma chifukwa chakuti anzanga amangonditukwana ndiponso kundimenya, ulendowo umakhala wowawa ndiponso wautali.” Komanso achinyamata ena amachitiridwa zachipongwe. Mtsikana wina, dzina lake Anita, anati: “Mnyamata wina wotchuka kusukulu kwathu ananditchingira njira n’kuyamba kundigwiragwira. Ndinamuuza mwaulemu kuti andisiye koma sanamvere chifukwa ankaona ngati zikundisangalatsa.”
Achinyamata ena amachitiridwa zachipongwe ndi anzawo a kusukulu kudzera pa Intaneti. Kodi inuyo anthu amakuchitirani zachipongwe? Kodi mungatani ngati ena akukuchitirani zachipongwe? Pali zambiri zimene mungachite, koma choyamba tiyeni tione ziganizo zimene zili kumayambiriro kwa nkhani ino ngati zili zoona kapena zonama.
1. Zonama. Nthawi zambiri anthu ovutitsa anzawo amangonyoza osati kumenya. Ena amanyoza anzawo powaopseza, kuwatukwana, kuwagemula ndi kuwanena.
2. Zonama. Mawu oyamikira, nthabwala zotukwana, kapena kuyang’ana mokopa zingakhalenso zachipongwe.
3. Zoona. Anyamata ndiponso atsikana angavutitse kapena kuchitira anzawo zachipongwe.
4. Zonama. Pali zimene inuyo mungachite kuti anthu asiye kukuvutitsani. Tiyeni tione mmene mungachitire.
N’zotheka Kugonjetsa Munthu Amene Akukuvutitsani Popanda Kumenyana Naye
Anthu ena angakuvutitseni kuti angoona kuti muchita chiyani. Baibulo limati: “Usakangaze mumtima mwako kukwiya.” (Mlaliki 7:9) Pamenepa mfundo ndi yakuti ‘kubwezera choipa pa choipa’ kumangowonjezera moto ndipo kumayambitsa mavuto ambiri. (Aroma 12:17) Choncho, kodi mungatani kuti mugonjetse munthu amene akukuvutitsani popanda kumenyana naye?
Musafulumire kukwiya. Ngati munthu wina akukugemulani, musafulumire kukwiya. Mnyamata wina dzina lake Eliu anati: “Nthawi zina ndi bwino kungonyalanyaza zimene ena akunena.” Izi zingakhale zoona chifukwa munthu amene akukuvutitsaniyo akaona kuti sizikukukhudzani amangosiya.
Yankhani mofatsa. Baibulo limati: “Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Munthu amene akukuvutitsani sayembekezera kuti mumuyankha mofatsa, choncho ngati mutamuyankha mofatsa, angasiye. Zoona, kudziletsa kuti musayankhe mwaukali ena akamakunenani n’kovuta kwambiri, koma n’kofunika. Lemba la Miyambo 29:11 limati: “Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; koma wanzeru auletsa nautontholetsa.” Kufatsa si kupusa. Munthu wofatsa nthawi zonse amadziwa chimene akuchita, koma wovutitsa anzake nthawi zambiri amachita zinthu m’chimbulimbuli ndiponso zinthu sizimuyendera bwino. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Wosakwiya msanga aposa wamphamvu.”—Miyambo 16:32.
Dzitetezeni. Ngati mukuona kuti zinthu zaipa, ndi bwino kuthawa. Lemba la Miyambo 17:14 limati: “Kupikisana kusanayambe tasiya makani.” Choncho ngati mukuona kuti pachitika zinthu zachiwawa, chokanipo kapena thawani. Ngati simungathe kuthawa, chitani chilichonse kuti mudziteteze.
Kaneneni. Makolo anu ayenera kudziwa zimene zikukuchitikirani. Iwo angakupatseni malangizo othandiza. Mwachitsanzo, angathe kukuuzani kuti mukanene nkhaniyo kwa aphunzitsi. Makolo ndi aphunzitsi angakuthandizeni kuti muthetse nkhaniyo bwinobwino popanda kuyambitsa mavuto ena.
Munthu amene akukuvutitsani sangapitirize ngati akuona kuti inuyo sizikukukhudzani. Choncho, musapse mtima, ndipo gwiritsirani ntchito mfundo zimene takambiranazi.
Kodi Mungatani Ena Akamakuchitirani Zachipongwe?
M’pomveka kupsa mtima ena akamakuchitirani zachipongwe. Koma pali zinthu zambiri zimene mungachite kuti mudziteteze. Onani mfundo zotsatirazi.
Kanani mwamphamvu. Ngati simukana mwamphamvu, munthu wokuvutitsaniyo angaone ngati mukungokana koma pansi pa mtima mukufuna. Muuzeni motsimikiza kuti mukufuna asiye zimene akuchitazo. Choncho tsimikizani kuti mukati ayi akhaledi ayi. (Mateyo 5:37) Mukamasekerera kapena kulankhula mwamanyazi, amaona ngati zikukusangalatsani. Choncho muuzeni mwamphamvu kuti simukufuna. Palibenso njira ina yabwino yodzitetezera kuposa imeneyo.
M’chititseni manyazi. Anita tam’tchula kale uja anati:
“Ndinam’kalipira mokweza kuti asiyiretu, ndipo anzake onse anayamba kumuseka. Iye anachita manyazi ndipo anasiya kundilankhula. Koma patapita masiku owerengeka, anandipepesa ndipo nthawi ina ananditeteza munthu wina akundivutitsa.”Ngati sakukusiyani, thawani. Kuthawa ndi njira yabwino. Koma ngati mukuona kuti simungathe kuthawa, dzitetezeni mmene mungathere. (Deuteronomo 22:25-27) Mtsikana wina wachikhristu anati: “Mnyamata wina atandigwira, ndinam’menya mwamphamvu n’kuthawa.”
Uzani munthu wina. Mtsikana wina wazaka 16, dzina lake Adrienne, anati: “Mnyamata wina amene ndinkacheza naye bwinobwino atayamba kundivutitsa, ndinauza makolo anga kuti andithandize maganizo. Iye ankaona ngati palibe vuto ndipo ankalimbikirabe ngakhale kuti ndinkakana. Choncho ndinayenera
kuuza makolo basi.” Makolo a Adrienne anam’patsa malangizo omwe anamuthandiza kuthana ndi vuto lakelo. Nanunso makolo anu angakuthandizeni.Palibe amene angasangalale kuti azivutitsidwa kapena kuchitiridwa zachipongwe. Ndiye muzikumbukira mfundo iyi: Ngakhale kuti ndinu Mkhristu, simuyenera kumangolekerera kuti anzanu azikuvutitsani kapena kukuchitirani zachipongwe. Yesetsani kutsatira malangizo amene tafotokozawa kuti muthane ndi mavuto ngati amenewa.
WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 18
Achinyamata ambiri amafuna kutengera zochita za anzawo. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zoyenera kuchita.
LEMBA LOFUNIKA
“Ngati ndi kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.”—Aroma 12:18.
MFUNDO YOTHANDIZA
Ngati anzanu amakuvutitsani, muziyankha molimba mtima koma osati mwaukali. Uzani mwamphamvu munthu amene akukuvutitsaniyo kuti asiye. Kenako ingochokani mwakachetechete. Ngati akupitirizabe kukuvutitsani, kamunenereni.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Ena angayambe kukuvutitsani ngati mwavala zovala zimene anthu a m’gulu linalake amakonda. Munthu wina amene poyamba anali wovutitsa anati: “Nthawi zambiri tinkavutitsa aliyense yemwe wavala zovala za gulu lathu. Tinkamukakamiza kuti akhale m’gulu lathu ndipo akakana tinkamumenya kwambiri.”
ZOTI NDICHITE
Ngati wina wayamba kundivutitsa, ndiyenera kuchita izi: ․․․․․
Kuti ena asamandivutitse, ndiyenera kuchita izi: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․
MUKUGANIZA BWANJI?
● Kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu wolimba mtima komanso wofatsa kuti anzanu asamakupezerereni?
● Kodi mungatani ngati ena akukuchitirani zachipongwe? (Ganizirani zachipongwe zimene ena angakuchitireni ndiponso zimene mungachite kuti mudziteteze.)
● N’chifukwa chiyani simuyenera kungolekerera ena akamakuchitirani zachipongwe?
[Mawu Otsindika patsamba 123]
“Mukaona kuti ndewu iyambika, musalowerere ndipo ingonyamukani n’kumapita kunyumba. Ena amagwa m’mavuto chifukwa chofuna kuonerera ndewu.”—Anatero Jairo
[Bokosi/Chithunzi pamasamba 125]
kodi mungatani kuti anthu asamakuchitireni zachipongwe?
Musamakope ena. Anthu angakuchitireni zachipongwe ngati mukuchita zinthu mowakopa. Baibulo limati: ‘Kodi mungatenge moto pachifuwa chanu, osatentha zovala?’ (Miyambo 6:27) Apatu mfundo ndi yakuti munthu amene amakopa ena, amakhala akudziitanira mavuto.
Musamangocheza ndi aliyense. Mukamacheza ndi anthu akhalidwe loipa, anthu amaona kuti inunso muli ndi khalidwe loipa. Mtsikana wina dzina lake Carla anati: “Inunso angakuchitireni zachipongwe ngati mumakonda kucheza ndi anthu amene amasangalala kuvutitsa anzawo.”—1 Akorinto 15:33.
Muzivala modzilemekeza. Mukavala mosadzilemekeza, anzanu amaona ngati mukungofuna kukopa anyamata kapena atsikana ndipo amakopekadi n’kukuchitirani zachipongwezo.—Agalatiya 6:7.
Musamabise zoti ndinu Mkhristu. Mukamabisa zoti ndinu Mkhristu, anzanu amafuna kuti muzichita nawo zoipa.—Mateyo 5:15, 16.
[Chithunzi pamasamba 124]
Munthu akamakuvutitsani, si bwino kumupsera mtima chifukwa mukatero mumakhala ngati mukuthira parafini pamoto
[Chithunzi pamasamba 127]
Muuzeni munthu amene akukuvutitsaniyo kuti alekeretu