Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndikwaniritse Zolinga Zanga?

Kodi Ndingatani Kuti Ndikwaniritse Zolinga Zanga?

Mutu 39

Kodi Ndingatani Kuti Ndikwaniritse Zolinga Zanga?

Kodi ndi chiti pa zinthu zitatuzi chomwe mumachifuna kwambiri?

□ Kusadzikayikira

□ Kukhala ndi anzanu ambiri

□ Kukhala wosangalala

CHOSANGALATSA n’chakuti mukhoza kukhala ndi zonse zitatu. Zimenezi zikhoza kutheka ngati mutakhala ndi zolinga n’kuyesetsa kuzikwaniritsa. Taganizirani mfundo zotsatirazi:

Kusadzikayikira. Mukakhala ndi zolinga zing’onozing’ono n’kuzikwaniritsa, mumalimba mtima kuti mukhozanso kukwaniritsa zolinga zikuluzikulu. Mumalimbanso mtima polimbana ndi mavuto a tsiku ndi tsiku, monga kunyengereredwa ndi anzanu kuti muzichita zoipa.

Kukhala ndi anzanu ambiri. Anthu amasangalala kucheza komanso kugwira ntchito ndi anthu amene amakhala ndi zolinga pa moyo wawo. Anthu amenewa amakhala kuti akudziwa zimene akufuna ndipo amayesetsa kuti zimene akufunazo zitheke.

Kukhala wosangalala. Kunena zoona, munthu sumva bwino ukamangodikirira kuti tsiku lina zinthu zidzayamba kukuyendera bwino. Koma ngati utakhala ndi zolinga n’kuyesetsa kuzikwaniritsa, umayamba kusangalala. Ngati mukufuna kupeza poyambira, masamba otsatirawa angakuthandizeni. *

✔ 1 KUPEZA ZOLINGAZO

1. Ganizirani zolinga zimene mungakhale nazo. Pochita zimenezi musavutike ndi kuganiza kwambiri, ingolembani zolinga zonse zimene zabwera m’maganizo mwanu. Yesetsani kulemba zolinga zoposa 10.

2. Ganizirani zimene mwalembazo. Ndi zolinga ziti zimene mukuona kuti zingakhale zosangalatsa pozikwaniritsa? Kodi ndi ziti zimene mukuona kuti ndi zovuta kwambiri? Nanga ndi ziti zimene mukuona kuti mungasangalale kwambiri mutazikwaniritsa? Kumbukirani kuti ngati mwasankha zolinga zogwirizana ndi zimene mumakonda simungavutike kuzikwaniritsa.

3. Zisanjeni. Zolingazo ziikeni manambala malinga ndi mmene mukufuna kuzikwaniritsira.

✔ 2 KUPANGA PULANI

Pa cholinga chilichonse chimene mwasankha, chitani zotsatirazi:

Lembani cholingacho.

Kuphunzira chinenero chamanja

Dziikireni malire. N’zosatheka kukwaniritsa cholinga chilichonse ngati simunadziikire tsiku limene mukufuna mudzakhale mutachikwaniritsa.

July 1

Lembani zomwe mungachite pochikwaniritsa.

Zoyenera kuchita

1. Kupeza pepala la afabeti.

2. Kuphunzira masaini 10 mlungu uliwonse.

3. Kusonkhana ndi mpingo wa chinenerochi.

4. Kupempha munthu wina kuti aziona ngati ndikusaina bwino.

Ganizirani mavuto amene mungakumane nawo. Kenako ganizirani mmene mungathetsere mavutowo.

Mavuto amene ndingakumane nawo

Kusapeza munthu amene amalankhula chinenerochi kunoko

Tsimikizani kuti muchitadi. Sainirani komanso kulemba deti posonyeza kuti muyesetsa mmene mungathere kukwaniritsa cholingacho.

Zimene ndingachite kuti ndithane ndi vutoli

Kupeza ma DVD a chinenero chamanja kapena kuchita dawunilodi pa www.ps8318.com.

․․․․․ ․․․․․

Siginecha Deti

✔ 3 YAMBANI KUZIKWANIRITSA

Yambani lero lomwe. Dzifunseni kuti, ‘Kodi lerolo ndingachite chiyani kuti ndiyambe kukwaniritsa cholinga changa?’ N’zoona kuti simungadziwiretu zonse zofunika pokwaniritsa cholingacho komabe zimenezi zisakulepheretseni kuyamba kuchikwaniritsa. Paja Baibulo limanena kuti: “Woyang’ana mphepo sadzabzala mbewu, ndipo woyang’ana mitambo sadzakolola.” (Mlaliki 11:4) Pezani chinthu chimene mungachite lerolo ndipo chichiteni, ngakhale chitakhala chaching’ono.

Muzionanso zolingazo tsiku lililonse. Tsiku lililonse muziganizira cholinga chilichonse n’kuona kufunika kwake. Onani zimene mukuchita pokwaniritsa zolingazo ndipo mungaike chizindikiro ichi ✔ (kapena deti) pambali pa zimene mwakwaniritsa.

Ganizirani mmene zidzakhalire m’tsogolo. Ganizirani mmene mungamvere mutakwaniritsa cholingacho. Kenako ganiziraninso zimene muyenera kuchita kuti mukwaniritse zolingazo ndipo musakayikire zoti mungazikwaniritse. Pomaliza, ganizirani mmene mungasangalalire ngati mutakwaniritsa cholinga chanu. Kenako yambanipo kuzikwaniritsa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Mfundo zimene zili m’masamba amenewa zalembedwa pofuna kuthandiza munthu amene ali ndi zolinga zomwe sizingamutengere nthawi yaitali, koma zingagwirenso ntchito pa zolinga zikuluzikulu.

LEMBA

“Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.”​—Miyambo 21:5.

MFUNDO YOTHANDIZA

Musamapanikizike kwambiri pofuna kutsatira ndendende zimene munalemba. Pamene mukuyesetsa kukwaniritsa cholinga chanu, mukhoza kusintha pena ndi pena.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Mukakhala ndi cholinga chachikulu n’kuchikwaniritsa, m’pamenenso mumakhala wosangalala kwambiri.

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi ndi zotheka kukwaniritsa zolinga zambirimbiri nthawi imodzi?​—Afilipi 1:10.

● Kodi kukhala ndi zolinga kukutanthauza kuti muyenera kulemba chilichonse chimene mungachite pa moyo wanu?​—Afilipi 4:5.

[Mawu Otsindika patsamba 283]

“Munthu ukakhala kuti ulibe cholinga chilichonse, moyo sumakusangalatsa. Koma ukakhala ndi zolinga n’kumazikwaniritsa, umakhala wosangalala.”​—Anatero Reed

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 283]

Chitsanzo cha Zolinga Zimene Mungalembe

Anzanga Kukhala ndi mnzanga wamkulu kapena wamng’ono kwa ineyo. Kuyambiranso kucheza ndi mnzanga amene ndinasiya kucheza naye.

Thanzi Kuchita masewera olimbitsa thupi kwa mphindi pafupifupi 90 mlungu uliwonse. Kugona maola 8 tsiku lililonse.

Sukulu Kuyesetsa kuti ndizikhoza bwino masamu. Kukana ngati anzanga akundinyengerera kuti ndichite zoipa.

Moyo wauzimu Kuwerenga Baibulo kwa mphindi 15 tsiku lililonse. Kuuza anzanga a m’kalasi zimene ndimakhulupirira mlungu uliwonse.

[Chithunzi patsamba 284, 285]

Zolinga zili ngati pulani chabe ya nyumba. Kuti mukhale ndi nyumba yeniyeni pamafunika kuchita khama kugwira ntchito