GEORGIA
Munali Kuti Nthawi Yonseyi?
Artur Gerekhelia
-
CHAKA CHOBADWA 1956
-
CHAKA CHOBATIZIDWA 1991
-
MBIRI YAKE Patangotha miyezi 8 atabatizidwa, anachoka kwawo komanso anasiya bizinezi yotentha n’kusamukira kumene kunkafunika olalikira ambiri.
NDINALI nditangobatizidwa kumene pamene abale anandipempha ngati ndingakonde kuwonjezera utumiki wanga. Pa 4 May, 1992, ndinakhala nawo pamsonkhano wapadera wa amene ankafuna kusamukira kudera limene kunkafunika olalikira ambiri. Tsiku lotsatira, ineyo ndi mnzanga amene anandigawira kuti ndizilalikira naye, tinasamukira kudoko la Batumi, lomwe lili m’dera la Ajaria.
Tsiku loyamba limene ndinalalikira ku Batumi, ndinkachita mantha kwambiri. Sindinkadziwa chochita moti ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi ndiwalalikira bwanji anthu amenewa?’ Ndinadabwa kwambiri ndi zimene mayi wina, yemwe anali woyamba kumulalikira kuderali ananena. Mayiyo anati: “Munali kuti nthawi yonseyi?” Mayiyo ankafunitsitsa atadziwa zambiri zokhudza Mboni za Yehova moti tsiku litsatira, tinayamba kuphunzira naye Baibulo.
Tisanapite ku Batumi, tinapatsidwa maadiresi a anthu omwe ankafuna kuphunzira Baibulo. Ndiye popeza mzindawo unali
udakali wachilendo kwa ife, tinkafunsa anthu kuti tisasochere. Ambiri sanatithandize kwenikweni chifukwa misewu yambiri inali itangosinthidwa kumene mayina. Komabe, anthuwa ankamvetsera tikamawalalikira. Pasanapite nthawi, tinayamba kuphunzira Baibulo ndi anthu omwe ankakhala m’magulu a anthu 10 kapena 15.Titangotha miyezi 4 yokha tili m’derali, anthu oposa 40 ankabwera kumisonkhano yathu. Ndiye tinayamba kudzifunsa kuti, ‘Ndani amene angatithandize kusamalira anthu amenewa?’ Kenako asilikali a dziko la Georgia anayamba kumenyana ndi gulu loukira boma ku Abkhazia. Zotsatira zake zinali zoti abale ndi alongo onse omwe anali kumpingo wanga wakale anasamukira ku Batumi. Zimenezi zinachititsa kuti kwa tsiku limodzi lokha, ku Batumi kukhazikitsidwe mpingo wokhala ndi akulu okwanira komanso apainiya.