Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mexico: M’bale Ángel ndi a Ismael akuphunzira kuwerenga zilembo za anthu osaona

NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

America

America
  • MAYIKO 57

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 998,254,087

  • OFALITSA 4,154,608

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 4,353,152

“Tiphunzirira Limodzi”

A Ismael, omwe amakhala ku Mexico, anaganiza zowerenga Baibulo lonse moti pamene chaka chinkatha n’kuti ataliwerenga kawiri. Koma kenako anadwala ndipo anasiya kuona. Patatha zaka zingapo, M’bale Ángel, anakumana ndi a Ismael ndipo anawauza malonjezo a m’Baibulo. A Ismael ankafuna kudziwa zambiri, koma anati: “Ine sindingathe kuwerenga Baibulo chifukwa ndine wosaona.”

Koma a Ángel anawauza kuti: “Musadandaule, ndikuphunzitsani kuwerenga zilembo za anthu osaona.”

A Ismael anawafunsa kuti: “Mumatha kuwerenga zilembo za anthu osaona?”

A Ángel anati: “Ayi, tiziphunzirira limodzi.” M’baleyu anadzipereka kuti aphunzire zilembo za anthu osaona n’cholinga choti athandize a Ismael, ndipo a Ismael anadabwa kwambiri ndi zimenezi. M’bale Ángel atapita kunyumba anafufuza zokhudza zilembo za anthu osaona n’cholinga choti adziwe mmene angawerengere zilembozo. Kenako analemba afabeti ya zilembozi papepala. Ndiyeno anapita nazo kwa a Ismael ndipo anayamba kuwaphunzitsa kuwerenga. Pasanapite nthawi a Ismael anaphunzira kuwerenga afabeti ya zilembo za osaona, ankapezeka pamisonkhano komanso anayamba kuwerenga mabuku athu. Panopa M’bale Ángel akuphunzira ndi anthu 4 osaona. M’baleyu ndi maphunziro akewo amakonda kukambirana mmene zinthu zidzakhalire m’Paradaiso, osaona akadzayamba kuona.

Atawaona Sanawazindikire

Mtsikana wina wazaka 14 wa ku United States, dzina lake Viannei, anati: “Tsiku lina m’kalasi, aphunzitsi ena anayamba kukamba za zipembedzo. Kenako anatiuza kuti titchule mayina a zipembedzo ndipo ine ndinatchula cha Mboni za Yehova. Koma ana a m’kalasimo anayamba kuseka. Iwo anati a Mboni za Yehovafe timawavutitsa tikamapita m’makomo mwawo, ndife anthu osowa zochita ndipo tikawapatsa mabuku athu amangowataya. Aphunzitsi aja nawonso analankhula zoipa zokhudza a Mboni.”

“Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kuti ndilimbe mtima kuwalalikira. Ndinawauza kuti timapita m’makomo mwawo, osati n’cholinga chokawavutitsa, koma chifukwa choti Yehova watituma kuti tikawauze malangizo othandiza a m’Baibulo. Ndinawapempha kuti asamataye mabuku athu chifukwa angawathandize kuti asinthe komanso kuti adzapulumuke. Aphunzitsi aja anapepesa ndipo analonjeza kuti a Mboni akadzafika kwawo, adzamvetsera komanso adzawerenga mabuku athu. Ndinkaona ngati akungonama.”

“Ndinakumananso ndi aphunzitsiwa patatha miyezi 4 koma ndinadabwa kuti anali atayamba kuphunzira Baibulo. Patatha miyezi ina 6 anabwera kusukulu kwathu kudzandithokoza chifukwa chowalalikira tsiku lijali. Nditawaona, sindinawazindikire chifukwa n’kuti atameta tsitsi ndi ndevu zawo. Panopa ndi wofalitsa wosabatizidwa.”

Analalikira M’dera la Amazon

Anthu ambiri omwe amakhala m’dera la Amazon ku Brazil anali asanamvepo uthenga wabwino. Chifukwa cha zimenezi, Bungwe Lolamulira linavomereza kuti abale ndi alongo akagwire ntchito yapadera yolakira kuderali kwa chaka chathunthu. Choncho chaka chatha anthu ambiri a m’derali anakhala ndi mwayi womvetsera uthenga wa Ufumu.

Brazil: Ofalitsa akulalikira ku Amazon

Pa nthawiyi, ofesi ya nthambi inasankha matauni 53 amene ali m’mbali mwa mitsinje m’dera la Amazon ndipo inakonza zoti ofalitsa akalalikire kumaderawa. Mmene pankatha miyezi 4 panali ofalitsa oposa 6,500 amene anadzipereka kukagwira ntchitoyi.

Abale ndi alongo 10 anapita m’tauni ina yotchedwa Anamã, ndipo pa nthawiyo n’kuti mulibe wofalitsa aliyense. Iwo analalikira m’tauniyi kwa masiku 11 ndipo anagawira mabuku, magazini ndi zinthu zina zokwana 12,500 komanso anayambitsa maphunziro 200. Pa nthawi imene anali m’tauniyi abalewa ankachitanso misonkhano ya mpingo. Pamsonkhano womaliza, panasonkhana anthu 90. Panopa abale ndi alongowa akuchititsabe maphunziro aja kudzera pa foni. Tikuyembekezera kuti ntchito imene abale ndi alongo anagwira m’madera amenewa ikhala ndi zotsatira zabwino.

Ananena Kuti Webusaiti Yathu ya jw.org Ndi Yothandiza

Jehizel ndi Mariana akhala ali m’kalasi imodzi pasukulu ina ku Venezuela kwa zaka 6. Jehizel ndi wa Mboni za Yehova ndipo Mariana ankamunyoza chifukwa cha zimenezi. Mariana ankaona kuti Jehizel sadziwa kusangalala ndi moyo. Ndiye tsiku lina zitafika pomukwana, Jehizel anauza Mariana kuti: “Mariana, ukatsegule pawebusaiti yathu ya jw.org. Ndiyeno ukapite pamene palembedwa kuti, ‘Mavidiyo Achikhristu’ kenako ukapite pamene alemba kuti, ‘Achinyamata.’”

Madzulo a tsiku limenelo Mariana anaimbira foni Jehizel n’kumuuza kuti: “Tsopano ndadziwa chifukwa chake sumachita nawo zinthu zina.”

Chifukwa chosadziwa zimene ankatanthauza, Jehizel anamufunsa kuti: “Kodi ukufuna uyambenso kundinyoza?”

Koma Mariana anayankha kuti: “Ayi, si choncho. Ndikufuna kukuthokoza. Ndazindikira kuti zinthu zimene ndinkaona ngati kusangalala ndi moyo, ndi zimene zimandibweretsera mavuto.” Panopa Mariana amaphunzira Baibulo ndiponso amapita kumisonkhano yonse ya mpingo.

Anafunsa M’busa wa Kutchalitchi Kwawo

Mayi Gérole ankagwira ntchito yausekilitale patchalitchi china ku Haiti. Iwo anachita chidwi kwambiri ataona kuti a Mboni ayankha mafunso awo onse. Choncho mayiwa ndi mwana wawo wamkazi anavomera kuti aziphunzira Baibulo. Chifukwa choti ankasangalala kwambiri ndi zimene ankaphunzira, anapempha kuti aziphunzira kawiri pa mlungu.

Patatha miyezi itatu, mayiwa anapita kwa m’busa wa kutchalitchi kwawo n’kumufunsa mafunso 4. Anamufunsa kuti: “Kodi Yesu anakhala Mfumu chaka chiti? Kodi anthu abwino amapita kuti akamwalira? Nanga anthu oipa amapita kuti? Kodi Yesu anafera pamtanda kapena pamtengo?” M’busa uja anati angathe kuyankha funso lachiwiri ndi lachitatu basi. Iye anati: “A Mboni za Yehova amati anthu 144,000 okha ndi amene adzapite kumwamba. Koma ineyo ndimaona kuti anthu onse amene amachita chifuniro cha Mulungu adzapita kumwamba. Pamene anthu oipa adzapita kumoto kukawotchedwa.” Mayiyo atafunsa m’busayu kuti amuonetse umboni wa m’Malemba wa zimenezi, analephera kutchula lemba lililonse. Mayi Gérole anakhumudwa kwambiri ndi zimene m’busayu anayankha. Komabe izi zinapangitsa kuti apitirize kuphunzira Baibulo ndi a Mboni. Kenako anasiya tchalitchi chawo ndipo anati zimene anaphunzira ndi a Mboni pa miyezi itatu zinali zambiri kuposa zimene anaphunzira pa zaka 30 zimene anakhala akupita kutchalitchi. Panopa mayiwa komanso mwana wawo uja anabatizidwa ndipo akuphunzira Baibulo ndi anthu 23 m’mudzi wakwawo.

Haiti: Mayi Gérole ndi mwana wawo akuphunzira Baibulo ndi munthu