Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Lipoti la Milandu la 2016

Lipoti la Milandu la 2016

Abale ndi alongo amasonyeza kuti ndi okhulupirika kwa Yehova akakumana ndi mavuto komanso akamaimbidwa milandu. Chitsanzo chawo chabwino chingatithandize kuti nafenso tikhale ndi chikhulupiriro cholimba podziwa kuti Yehova amasamalira “wokhulupirika wake” mwanjira yapadera.Sal. 4:3.

ARGENTINA | Ufulu Wophunzitsa Ana Nkhani za Chipembedzo

Mlongo wina dzina lake Ruth anakulira m’banja la Mboni koma kenako anasiya kusonkhana. Patapita nthawi, anayamba chibwenzi ndi mnyamata wina ndipo anabereka mwana wamkazi. Mlongo Ruth ankakhala mumzinda wa La Plata ndipo tsiku lina anaona a Mboni za Yehova akulalikira pogwiritsa ntchito kashelefu kamatayala. Ruth anakumbukira kuti poyamba anali wa Mboni. Izi zinachititsa kuti ayambirenso kusonkhana komanso anayamba kuphunzitsa mwana wake za Yehova. Koma bambo a mwanayo sanagwirizane nazo moti anakasuma nkhaniyi kukhoti n’cholinga choti Ruth asamaphunzitse mwanayo komanso asamapite naye kukasonkhana.

Loya wa Ruth ananena kuti makolo onse ali ndi ufulu wophunzitsa mwanayo zimene amakhulupirira. Ananenanso kuti a khoti sangachotse ufulu umenewu pokhapokha ngati pali umboni woti zimene kholo likuphunzitsa mwanayo zingamusokoneze. Khoti linagamula kuti makolowo ayenera kulemekeza ufulu wa mwanayo wokhudza chipembedzo ngakhale kuti mwanayo anali ndi zaka 4 zokha. Bambo a mwanayo atapanga apilo za nkhaniyi, khoti la apilolo linanena kuti mwanayo ndi wamng’ono kwambiri moti sangasankhe yekha chipembedzo chimene akufuna. Choncho makolo onse awiri anali ndi ufulu wofanana wophunzitsa mwanayo zokhudza chipembedzo.

Panopa mwana wa Mlongo Ruth amawerenga Baibulo tsiku lililonse komanso amapita kumisonkhano ndi mayi ake. Mwanayo anati akufunitsitsa kudzapita kukaona ofesi ya nthambi ya ku Buenos Aires.

AZERBAIJAN | Ufulu Wouza Ena Zimene Umakhulupirira

Mtumwi Paulo ananena kuti anthu omwe ali mumpingo wachikhristu amakhala ngati ziwalo za thupi moti “chiwalo chimodzi chikavutika, ziwalo zina zonse zimavutikira nacho limodzi.” (1 Akor. 12:26) Mwachitsanzo, pamene Mlongo Irina Zakharchenko ndi Mlongo Valida Jabrayilova, omwe amakhala ku Azerbaijan anamangidwa, a Mboni za Yehova padziko lonse anadandaula kwambiri. Mu February 2015, akuluakulu a boma ananena kuti alongo awiriwa ali ndi mlandu wochita zinthu zoletsedwa zokhudza chipembedzo. Khoti linagamula kuti alongowa amangidwe podikirira kuti mlandu wawo uweruzidwe. Koma mlanduwo unkangolephereka moti alongowa anakhala m’ndende pafupifupi chaka ndipo ankazunzidwa komanso ankawaphera ufulu osiyanasiyana.

Azerbaijan: Mlongo Valida Jabrayilova ndi Mlongo Irina Zakharchenko

Mlandu wawo utaweruzidwa mu January 2016, anawapeza olakwa. Koma ananena kuti sapatsidwa chilango chifukwa anali atakhala kale m’ndende kwa nthawi yaitali. Koma khoti lomwe linaweruza mlanduwu linakana kumva madandaulo awo oti zimene ankachita sizinkaphwanya malamulo. Choncho alongowo anakachita apilo kukhoti lalikulu la m’dzikolo. Iwo anakasumanso ku Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu, chifukwa boma linali litaphwanya ufulu wawo wouza ena zimene amakhulupirira komanso chifukwa anachitidwa nkhanza.

Panopa zinthu zayambanso kuwayendera bwino alongowa. Iwo akuthokoza kwambiri abale ndi alongo chifukwa chowapempherera komanso kuwalimbikitsa pa nthawi imene anali m’ndende. Mlongo Jabrayilova analembera Bungwe Lolamulira kuti: “Mapemphero anu anatithandiza kuti tipirire. Sindidzaiwala chikondi chimene Yehova anandisonyeza kudzera mwa inuyo komanso abale ndi alongo padziko lonse.”

ERITREA | Anamangidwa Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Pofika mu July 2016, boma la Eritrea lamanga abale 55 chifukwa cha zimene amakhulupirira. Abale atatu omwe ndi a Paulos Eyassu, a Isaac Mogos komanso a Negede Teklemariam akhala m’ndende kuyambira mu September 1994. Abale enanso 9 akhala m’ndende kwa zaka 10 tsopano.

Koma mu January 2016 panachitika zinthu zosangalatsa pamene khoti linaganiza zoweruza mlandu wa a Mboni a ku Asmara. A Mboniwa anamangidwa mu April 2014 pamene ankachita Chikumbutso. Imeneyi inali nthawi yoyamba kuti boma liweruze mlandu wa a Mboni komanso kuwapatsa mwayi wodziteteza. Mlanduwo utaweruzidwa, abale ndi alongo anauzidwa kuti ankachita mwambo woletsedwa, choncho anawapeza olakwa. Ena anauzidwa kuti apereke chindapusa kenako anamasulidwa. Komabe, mlongo wina dzina lake Saron Gebru, anakana kulipira chindapusa chifukwa cha mlanduwu. Zimenezi zinachititsa kuti akakhale kundende miyezi 6. Mlongo Gebru ankaloledwa kulandira alendo kamodzi pa mlungu ndipo anati sankamuchitira nkhanza. Mlongoyu komanso a Mboni 54 omwe ali m’ndende, akuyamikira kwambiri chifukwa chowapempherera komanso ‘kuwakumbukira pamene ali m’ndende ngati tamangidwa nawo limodzi.’Aheb. 13:3.

GERMANY | Analandira Ufulu Wambiri Wachipembedzo

Pa 21 December, 2015 chigawo cha Bremen chomwe chili kumpoto chakumadzulo kwa dziko la Germany, chinapereka ufulu wambiri wachipembedzo kwa a Mboni za Yehova kuposa umene anali nawo poyamba. Abale anakhala akuyesetsa kuti zimenezi zitheke kwa zaka 4 m’makhoti osiyanasiyana. Zigawo 16 za ku Germany zinali zitapereka kale ufulu woterewu kwa a Mboni za Yehova potsatira zimene khoti lalikulu linagamula ku Berlin. Koma akuluakulu a chigawo cha Bremen anakana kupereka ufuluwu kwa a Mboni chifukwa anthu ena anawauza zabodza zokhudza a Mboniwo.

Komabe mu 2015, khoti loona za ufulu wa anthu ku Germany linagamula kuti zimene akuluakulu a ku Bremen anachitazi kunali kuphwanya ufulu wachipembedzo wa a Mboni za Yehova. Khotili linati a Mboni akapatsidwa ufulu wambiri wachipembedzo, ndiye kuti azikhalanso ndi ufulu wochita zinthu zina zokhudza chipembedzo chawo. Poyamba mipingo ya m’chigawo cha Bremen inkayenera kupereka misonkho komanso inalibe mwayi wopeza zinthu zina zimene zipembedzo zikuluzikulu ku Germany zimapeza. Koma atapatsidwa ufulu wambiri wachipembedzowo, mavuto onsewa anatha.

KYRGYZSTAN | Ufulu Wouza Ena Zomwe Umakhulupirira

Mu March 2013, akuluakulu a m’tauni ya Osh ku Kyrgyzstan, anatengera kukhoti Mlongo Oksana Koriakina ndi mayi awo a Nadezhda Sergienko. Akuluakuluwo ankaimba alongowa mlandu woti ankabera anthu akamawalalikira uthenga wa m’Baibulo. Woweruza mlanduwu anauza alongowa kuti asamachoke panyumba podikira tsiku la mlandu wawo. Mu October 2014, khoti linapeza kuti umboni wa akuluakulu a boma unali wabodza ndiponso sanatsatire dongosolo loyenera. Khotilo linagamula kuti alongowo ndi osalakwa. Akuluakuluwo anachita apilo mlanduwu koma mu October 2015 khoti la apilolo linagwirizana ndi zimene khoti loyamba lija linagamula.

Komabe, akuluakulu a m’tauni ya Osh anakasumanso nkhaniyi kukhoti lalikulu la ku Kyrgyzstan. Khotili linachotsa zonse zimene makhoti ena aja anagamula ndipo linanena kuti liweruzanso mlanduwu. Pa tsiku la mlanduwu mu April 2016, loya yemwe ankaimira alongowa anapempha woweruza kuti athetse mlanduwo chifukwa masiku ake anali atatha. Panalibenso chimene woweruzayo akanachita moti anathetsadi mlanduwo.

Pa nthawi yonse imene mlanduwu unkaweruzidwa, alongo athuwa sanafooke. Mlongo Sergienko anati: “Anthu ambiri amakwiya akakhala kuti akuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo. Koma ife sitinachite zimenezi chifukwa tinkadziwa kuti sitili tokha. Tinkaona kuti Yehova amatikonda komanso akutisamalira pogwiritsa ntchito abale ndi alongo.” Alongowa anaona kuti Yehova anakwaniritsa mawu ake a pa Yesaya 41:10 akuti: “Usachite mantha, . . . Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.”

KYRGYZSTAN | Ufulu Wachipembedzo

Pa 9 August, 2015, apolisi 10 anafika pamalo ena pamene abale ndi alongo okwana 40 ankachita misonkhano yampingo mumzinda wa Osh ku Kyrgyzstan. Apolisiwo analamula abalewo kuti aimitse msonkhanowo chifukwa ndi woletsedwa ndipo anawopseza kuti awombera abale ndi alongowo. Kenako anagwira abale 10 n’kupita nawo kupolisi. Kumeneko anamenya abale 9 komanso kuwachitira nkhanza zosiyanasiyana kenako anawatulutsa. Patatha masiku awiri, apolisiwo anatsekera M’bale Nurlan Usupbaev, mmodzi mwa abale amene anamenyedwa aja, ndipo anamutsegulira mlandu wochititsa msonkhano woletsedwa.

Nkhani ya m’baleyu itapita kukhoti mumzinda wa Osh, woweruza anapeza kuti mlanduwo ulibe umboni choncho anangouthetsa. Koma woimira boma pa mlanduwu anachita apilo kukhoti lalikulu. Kumenekunso anagamula kuti m’baleyu ndi wosalakwa chifukwa chipembedzo cha Mboni za Yehova chinalembetsedwa mwalamulo m’dzikolo.

Woimira bomayo sanagwirizanebe ndi chigamulochi, choncho anapanganso apilo kukhoti lina lalikulu kwambiri. Koma n’zosangalatsa kuti mu March 2016 khotili linagwirizana ndi zimene makhoti awiri aja anagamula. Nalonso linanena kuti a Mboni za Yehova ali ndi ufulu wochita misonkhano yawo ku Kyrgyzstan. A Mboni enanso anakadandaula kukhoti chifukwa choti apolisi anawachitira nkhanza ndipo akudikira tsiku la mlandu wawo.

RUSSIA | Ufulu Wachipembedzo

Boma la Russia likupitirizabe kulimbana ndi a Mboni za Yehova ngakhale kuti bungwe loona za ufulu wa anthu a m’dzikoli linawauza kuti akuwaphwanyira ufulu. Chaposachedwapa, akuluakulu a boma analengeza kuti zinthu zokwana 88 zimene gulu lathu limatulutsa ndi zoletsedwa chifukwa zikuopseza chitetezo cha dzikolo. Linalengezanso kuti laletsa webusaiti ya Mboni za Yehova ya jw.org. Komanso mu 2015, akuluakulu oona za zinthu zolowa m’dzikolo analetsa kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lisalowe m’dzikoli. Panopa nkhani yokhudza kuletsedwa kwa Baibuloli ili kukhoti mumzinda wa Vyborg. Mu March 2016, a ku ofesi yoimira boma pamilandu anaopseza kuti atseka maofesi a Mboni za Yehova omwe ali ku Solnechnoye ponena kuti zimene akuchita zikupereka chiopsezo ku dziko la Russia.

Ngakhale kuti akuluakulu a boma akuyesetsa kulimbana ndi Mboni za Yehova m’dzikoli, pali zinthu zina zosangalatsa zomwe zinachitika. Mwachitsanzo, mu October 2015, woimira boma pamilandu anakasuma kukhoti kuti boma litseke bungwe la chipembedzo cha Mboni za Yehova lomwe lili ku Tyumen pamtunda wa makilomita 2,100 kum’mawa kwa mzinda wa Moscow. Ngakhale kuti zinadziwika kuti apolisi anapereka umboni wabodza, khoti la mumzinda wa Tyumen linagamula kuti bungwe la chipembedzo cha Mbonilo litsekedwedi. Komabe pa 15 April, 2016, khoti lalikulu la ku Russia linatsutsa zimene khoti lija linagamula. Linanena kuti “palibe chifukwa chomveka chotsekera bungwe lachipembedzo cha Mboni za Yehova mumzinda wa Tyumen.” Pamene woweruza ankalengeza chigamulochi, abale ndi alongo okwana 60 omwe anali m’khotilo anaimirira uku akuwomba m’manja kwambiri chifukwa chosangalala.

A Mboni za Yehova a ku Russia atsimikiza kuti apitirizabe kutumikira Yehova mosaopa “chida chilichonse chimene chidzapangidwe.”Yes. 54:17.

RWANDA | Ufulu Wamaphunziro

Posachedwapa ana a Mboni a ku Rwanda ankachotsedwa sukulu chifukwa chokana kuchita miyambo yachipembedzo komanso zinthu zosonyeza kukonda dziko lawo. Pofuna kuthetsa vutoli, pa 14 December, 2015, boma linakhazikitsa lamulo lothandiza kuti ana asamasalidwe m’masukulu chifukwa cha chipembedzo chawo. Lamuloli linati masukulu onse ayenera kulemekeza ufulu wachipembedzo wa mwana aliyense.

Pa 9 June, 2016, pa jw.org panali nkhani yamutu wakuti, “Dziko la Rwanda Lathetsa Tsankho Limene Limachitika M’masukulu Chifukwa cha Kusiyana kwa Zipembedzo.” N’zochititsa chidwi kuti nyuzipepala ina ya pa intaneti ya m’dzikoli inaikanso nkhaniyi pawebusaiti yawo. Pasanapite nthawi, anthu okwana 3,000 anawerenga nkhaniyi ndipo ambiri analemba zosonyeza kuti akugwirizana ndi zimene boma la Rwanda linanena pa nkhaniyi. A Mboni za Yehova a ku Rwanda akusangalala kwambiri ndi zimene boma linachitazi chifukwa zikuthandiza kuti ana awo aziphunzira popanda kusalidwa chifukwa cha chipembedzo.

Rwanda: Anabwereranso kusukulu

SOUTH KOREA | Ufulu Wokana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Umakhulupirira

Kwa zaka zoposa 60, abale a m’dziko la South Korea, azaka zapakati pa 19 mpaka 35 akhala akukakamizidwa kulowa usilikali. M’dzikoli mulibe lamulo lolola munthu amene wakana kulowa usilikali, kugwira ntchito zina. Zimenezi zachititsa kuti abale akakana kulowa usilikali azimangidwa. M’mabanja ena zimapezeka kuti agogo, bambo komanso ana anamangidwapo pa chifukwa chimenechi.

Khoti lalikulu la m’dzikoli linagamula kuti amuna onse ayenera kulowa usilikali. Koma makhoti ang’onoang’ono komanso anthu ena omwe anaweruzidwa kuti amangidwe chifukwa chokana kulowa usilikali, akumatengeranso nkhanizo kukhoti lomweli kuti azionenso. Choncho pa 9 July, 2015, khotili linavomera kumva mlandu wokhudza anthu amene anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. M’bale Min-hwan Kim, yemwe anakhala m’ndende kwa miyezi 18 chifukwa chokana kuphunzira usilikali, anati: “Ndinaikidwa m’ndende koma panopa ndatuluka. Koma ndikukhulupirira kuti boma lisiya kumanga anthu chifukwa chokana kulowa usilikali. Bomali lingachite bwino kwambiri litamawalola kugwira ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali zomwe zingathandize dziko lathu.” Khoti lalikululi linanena kuti lipereka chigamulo cha nkhaniyi m’tsogolo muno.

TURKMENISTAN | M’bale Bahram Hemdemov

M’bale Hemdemov, yemwe ali ndi zaka 53, ali pa banja ndipo ali ndi ana 4. M’baleyu ndi wakhama komanso anthu a m’dera lawo amamulemekeza kwambiri. Koma mu May 2015, khoti linagamula kuti m’baleyu ndi wolakwa chifukwa ankachititsa msonkhano woletsedwa kunyumba kwake. Choncho anamuuza kuti akakhale m’ndende kwa zaka 4 akugwira ntchito yakalavulagaga. M’baleyu anaikidwa m’ndende ina yoipa kwambiri yomwe ili m’tauni ya Seydi ndipo akuluakulu a boma ankamuchitira nkhanza pomufunsa mafunso komanso kumumenya. Koma m’baleyu ndi banja lake akhalabe okhulupirika kwa Yehova. Mlongo Gulzira, yemwe ndi mkazi wa m’baleyu, amaloledwa kukamuona komanso kukamulimbikitsa mwa apa ndi apo.

Monga taonera, a Mboni za Yehova akupitirizabe kukhala okhulupirika akamayesedwa ndipo timawapempherera. Zitsanzo zawo zimatithandiza kuti nafenso tilimbitse chikhulupiriro chathu. Timadziwa kuti Yehova adzakwaniritsa lonjezo lake la pa Salimo 37:28 lomwe limati: “Sadzasiya anthu ake okhulupirika.”