PHUNZIRO 11
N’chifukwa Chiyani Timakhala ndi Misonkhano Ikuluikulu?
N’chifukwa chiyani anthu awa akuoneka achimwemwe? N’chifukwa chakuti ali pamsonkhano wina waukulu umene timakhala nawo. Mofanana ndi atumiki akale a Mulungu, amene anauzidwa kuti azichita misonkhano itatu pachaka, ifenso timachita misonkhano ikuluikulu. (Deuteronomo 16:16) Chaka chilichonse timachita misonkhano ikuluikulu itatu: Misonkhano iwiri yadera yomwe imachitika tsiku limodzilimodzi, ndiponso msonkhano wachigawo wamasiku atatu. Kodi timapindula bwanji ndi misonkhano imeneyi?
Imathandiza kuti ubale wathu wachikhristu ukhale wolimba. Mofanana ndi Aisiraeli amene ankasangalala potamanda Yehova “pamsonkhano,” ifenso timasangalala kusonkhana pamodzi n’kumamulambira pamisonkhano ikuluikulu. (Salimo 26:12; 111:1) Misonkhano imeneyi imatipatsa mwayi wokumana komanso kucheza ndi abale ndi alongo athu a m’mipingo ina kapenanso ochokera m’mayiko ena. Masana timasangalala kudyera limodzi chakudya pamalo a msonkhano omwewo, zomwe zimatipatsa mpata wocheza ndi Akhristu anzathu. (Machitidwe 2:42) Pamisonkhano imeneyi timaona umboni wa chikondi chimene chimagwirizanitsa “gulu lonse la abale” padziko lapansi.—1 Petulo 2:17.
Imatithandiza kukula mwauzimu. Aisiraeli ankapindulanso chifukwa chakuti ‘ankamvetsa bwino mawu’ a m’Malemba amene ankafotokozedwa momveka bwino. (Nehemiya 8:8, 12) Ifenso timayamikira malangizo a m’Baibulo amene timalandira pamisonkhano yathu. Msonkhano uliwonse umakhala ndi mutu wochokera m’Malemba. Pamisonkhano imeneyi pamakhala nkhani zosiyanasiyana zosangalatsa komanso zitsanzo zomwe zimatithandiza kuchita zimene Mulungu amafuna pa moyo wathu. Timalimbikitsidwa kwambiri anthu ena akamafotokoza zimene achita kuti apirire mavuto amene akumana nawo pa moyo wachikhristu m’nthawi yovuta ino. Pamisonkhano yachigawo pamakhala masewero amene amatithandiza kumvetsa nkhani inayake ya m’Baibulo komanso kuona zimene tikuphunzirapo, ndipo ochita masewerowa amavala ngati mmene anthu akale ankavalira. Pamsonkhano uliwonse pamakhala ubatizo, ndipo anthu amene akufuna kusonyeza kuti anadzipereka kwa Mulungu, amabatizidwa.
-
N’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu amasangalala akakhala pamsonkhano waukulu?
-
Kodi mungapindule motani ngati mutapezeka pamsonkhano waukulu?