PHUNZIRO 12
Kodi Ntchito Yathu Yolalikira za Ufumu Imachitika Motani?
Yesu atatsala pang’ono kuphedwa ananena kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Koma kodi zingatheke bwanji kulalikira padziko lonse? Zingatheke potsatira chitsanzo chimene Yesu anasonyeza pamene anali padziko lapansi.—Luka 8:1.
Timayesetsa kuyendera anthu kunyumba zawo. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azilalikira uthenga wabwino kunyumba ndi nyumba. (Mateyu 10:11-13; Machitidwe 5:42; 20:20) Otsatirawo anauzidwa dera loti azikalalikira. (Mateyu 10:5, 6; 2 Akorinto 10:13) Mofanana ndi zimenezi, masiku ano ntchito yathu yolalikira imachitika mwadongosolo, ndipo mpingo uliwonse umapatsidwa dera loti uzilalikira. Zimenezi zimatithandiza kutsatira lamulo la Yesu lakuti “tilalikire kwa anthu ndi kupereka umboni wokwanira.”—Machitidwe 10:42.
Timayesetsa kulankhula ndi anthu kulikonse kumene angapezeke. Yesu anatipatsa chitsanzo polalikira kumalo alionse kumene kumapezeka anthu, monga m’mphepete mwa nyanja ndi pachitsime. (Maliko 4:1; Yohane 4:5-15) Ifenso timalankhula ndi anthu nkhani za m’Baibulo m’malo alionse monga mumsewu, m’malo ochitira malonda, m’malo amene anthu amakonda kupita kukacheza ndi patelefoni. Komanso tikakhala ndi mpata wabwino, timalalikira kwa anthu amene tayandikana nawo nyumba, anzathu akuntchito, akusukulu ndiponso achibale athu. Zonsezi zathandiza kuti anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse amve “uthenga wabwino wa chipulumutso.”—Salimo 96:2.
Kodi pali aliyense amene mukufuna kumuuza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi zimene Ufumuwo udzachite m’tsogolo? Yesetsani kuuza ena uthenga wopatsa chiyembekezowu, ndipo chitani zimenezi mwamsanga.
-
Kodi ndi “uthenga wabwino” wotani umene ukuyenera kulengezedwa?
-
Kodi a Mboni za Yehova akutsanzira bwanji Yesu polalikira?