Kodi Zimene Mumakhulupirira pa Nkhaniyi Zimakhudza Moyo Wanu?
Kodi inuyo mumaona kuti moyo uli ndi cholinga? Wasayansi wina dzina lake William B. Provine ananena kuti: “Zimene taphunzira pa nkhani yoti zamoyo zinangokhalapo zokha ndipo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina zimakhudza kwambiri moyo wathu.” Iye anapitiriza kuti: “Ndimaona kuti palibe cholinga chilichonse cha moyo wa anthu komanso zinthu zonse za m’chilengedwechi.”32
Taganizirani zimene mawu amenewa akutanthauza. Ngati moyo ulibe cholinga chilichonse, ndiye kuti chofunika pa moyo n’kumangoyesetsa kuchita zabwino komanso kubereka ana basi. Ndiye kuti munthu akafa, sadzakhalanso ndi moyo mpaka kalekale. Zikutanthauzanso kuti ubongo umene tili nawowu, womwe umatithandiza kuti tiziganizira za moyo wathu panopa komanso m’tsogolo, unangokhalapo mwangozi.
Komatu si zokhazi. Anthu ambiri amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina amanena kuti kulibe Mulungu kapena ngati alipo, alibe nafe ntchito. Ngati zimenezi ndi zoona, ndiye kuti tsogolo lathu lili m’manja mwa atsogoleri andale, achipembedzo komanso anthu ophunzira. Koma m’mbuyo monsemu, anthu ngati amenewa alephera kuthetsa mavuto monga nkhondo, ziwawa komanso chinyengo. Choncho zingatanthauze kuti mavuto amenewa sadzatha. Ngati zimene anthu ena amakhulupirirazi n’zoona, zingakhale bwino kumangoyendera mfundo yoti: “Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.”—1 Akorinto 15:32.
Koma Baibulo limanena kuti: “Inu [Mulungu] ndinu kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9) Kodi mfundo imeneyi ingakhudze bwanji moyo wathu?
Ngati zimene Baibulo limanenazi n’zoona, ndiye kuti moyo wathu uli ndi cholinga. Mlengi wathu wakonza zoti anthu onse amene amachita zinthu mogwirizana ndi cholinga chake adzakhale ndi tsogolo labwino. (Mlaliki 12:13) Anthu oterewa adzakhala ndi moyo wabwino wopanda nkhondo, ziwawa, chinyengo ngakhalenso imfa.—Salimo 37:10, 11; Yesaya 25:6-8.
M’pake kuti anthu ambiri amaona kuti kuphunzira za Mulungu, kumukhulupirira komanso kumumvera kumathandiza kuti tikhale ndi moyo wabwino komanso tsogolo labwino. (Yohane 17:3) Kukhulupirira zimenezi si kukhulupirira za m’maluwa. Pali umboni wonse wotsimikizira kuti zamoyo zinachita kulengedwa.