Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 13

Kusonyeza Kuti Nkhaniyo Ndi Yothandiza

Kusonyeza Kuti Nkhaniyo Ndi Yothandiza

Miyambo 3:21

MFUNDO YAIKULU: Thandizani anthu kudziwa mmene mfundo zimene mukuphunzitsa zingawathandizire ndiponso zimene angachite potsatira zimene mukuphunzitsazo.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muziganizira anthu. Muzidzifunsa kuti, Kodi nkhani yangayi ingathandize bwanji anthuwa, nanga mbali zimene zingawathandize kwambiri ndi ziti?

  • Munkhani yanu yonse, muzithandiza anthu kudziwa zoyenera kuchita. Mukangoyamba nkhani yanu, aliyense azizindikira kuti, ‘Nkhaniyitu indithandiza.’ Mukatchula mfundo yaikulu iliyonse, muziwasonyeza mmene angaigwiritsire ntchito. Muzipewa kukamba nkhani mongolambalala popanda kusonyeza zoyenera kuchita.