PHUNZIRO 01
Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?
Tonsefe timadzifunsa mafunso okhudza moyo, kuvutika, imfa komanso tsogolo lathu. Timafunanso titadziwa zimene tingachite kuti tithane ndi mavuto amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku, monga kusapeza ndalama zokwanira ndiponso zimene tingachite kuti tizikhala mosangalala m’banja lathu. Anthu ambiri amaona kuti Baibulo limawathandiza kupeza mayankho a mafunso ofunika komanso amapezamo malangizo odalirika. Kunena zoona, Baibulo likhoza kuthandiza munthu wina aliyense.
1. Kodi ndi mafunso ena ati amene Baibulo limayankha?
Baibulo limayankha mafunso ofunika monga akuti: Kodi moyo unayamba bwanji? Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? N’chifukwa chiyani anthu abwino amavutika? Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira? Popeza aliyense amafuna mtendere, n’chifukwa chiyani padzikoli pamachitika nkhondo? N’chiyani chidzachitikire dzikoli kutsogoloku? Baibulo limatilimbikitsa kuti tizipeza mayankho a mafunso ngati amenewa ndipo anthu mamiliyoni ambiri apeza mayankho ogwira mtima a mafunsowa.
2. Kodi Baibulo lingatithandize bwanji kuti tizisangalala?
M’Baibulo muli malangizo abwino. Mwachitsanzo, limafotokoza zimene mabanja angachite kuti azikhaladi mosangalala. Limaperekanso malangizo othandiza kuti tisamade nkhawa kwambiri komanso kuti tizikonda ntchito yathu. Tikamakambirana zimene zili m’bukuli, muphunzira zimene Baibulo limanena pa nkhani ngati zimenezi ndi zinanso. Mudzafika pomvetsa kuti “Malemba onse [kapena kuti mawu onse amene ali m’Baibulo] . . . ndi opindulitsa.”—2 Timoteyo 3:16.
Bukuli silikulowa m’malo mwa Baibulo. Koma likuthandizani kuti muzifufuza mfundo za m’Baibulo panokha. Choncho tikukulimbikitsani kuti muziwerenga malemba amene aikidwa m’phunziro lililonse, kenako muziwayerekezera ndi zimene mukuphunzira.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani mmene Baibulo lathandizira anthu ena, zimene mungachite kuti muzisangalala poliwerenga ndiponso ubwino wopempha anthu ena kuti akuthandizeni kulimvetsa.
3. Baibulo lingatithandize
Baibulo lili ngati nyale yowala kwambiri. Lingatithandize kuti tizisankha zinthu mwanzeru, komanso limatiuza zimene zichitike m’tsogolo.
Werengani Salimo 119:105, kenako mukambirane mafunso awa:
-
Kodi amene analemba salimoli, ankaliona bwanji Baibulo?
-
Nanga inuyo mumaliona bwanji?
4. Baibulo limayankha mafunso athu
Baibulo linathandiza mayi wina kupeza mayankho a mafunso amene ankamuvutitsa maganizo kwa zaka zambiri. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
-
Kodi muvidiyoyi, mayiyu anali ndi mafunso otani?
-
Nanga kuphunzira Baibulo kunamuthandiza bwanji?
Baibulo limatilimbikitsa kuti tizifunsa mafunso. Werengani Mateyu 7:7, ndipo kenako kambiranani funso ili:
-
Kodi muli ndi mafunso otani amene mukufuna kuti Baibulo likuyankheni?
5. Mukhoza kumasangalala powerenga Baibulo
Anthu ambiri amasangalala powerenga Baibulo ndipo likuwathandiza kwambiri. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
-
Muvidiyoyi, kodi achinyamatawa ankaiona bwanji nkhani yowerenga mabuku?
-
Ngakhale kuti sakonda kuwerenga mabuku, n’chifukwa chiyani amakonda kuwerenga Baibulo?
Baibulo limatipatsa malangizo amene amatitonthoza komanso kutipatsa chiyembekezo. Werengani Aroma 15:4, kenako mukambirane funso ili:
-
Kodi mungakonde kumva uthenga wa m’Baibulo womwe umatitonthoza komanso kutipatsa chiyembekezo?
6. Anthu ena akhoza kutithandiza kulimvetsa bwino Baibulo
Kuwonjezera pa kuwerenga Baibulo paokha, anthu ambiri amaona kuti kukambirana ndi ena kumawathandiza kuti azilimvetsa bwino. Werengani Machitidwe 8:26-31, kenako mukambirane funso ili:
-
Kodi tingatani kuti tizilimvetsa bwino Baibulo?—Onani mavesi 30 ndi 31.
ZIMENE ENA AMANENA: “Kuphunzira Baibulo ndi kutaya nthawi.”
-
Inuyo mukuganiza bwanji? Nanga n’chifukwa chiyani mukutero?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Baibulo limatipatsa malangizo othandiza, limayankha mafunso ofunika kwambiri, komanso limatitonthoza ndi kutipatsa chiyembekezo.
Kubwereza
-
Kodi m’Baibulo mumapezeka malangizo otani?
-
Kodi ndi mafunso ena ati amene Baibulo limayankha?
-
Kodi ndi zinthu ziti zomwe mungakonde kuphunzira m’Baibulo?
ONANI ZINANSO
Onani mmene malangizo a m’Baibulo akuthandizira anthu masiku ano.
“Mfundo za M’Baibulo Sizikalamba” (Nsanja ya Olonda Na. 1 2018)
Onani mmene Baibulo linathandizira munthu wina amene anali ndi vuto lodzikayikira kuyambira ali wamng’ono
Onani malangizo a m’Baibulo othandiza kuti banja liziyenda bwino.
“Mfundo 12 Zothandiza Kuti Banja Liziyenda Bwino” (Galamukani! Na. 2 2018)
Onani zimene Baibulo limanena pa nkhani ya amene akulamulira dzikoli ngakhale kuti anthu ambiri ali ndi maganizo olakwika pa nkhaniyi.
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?—Vidiyo Yathunthu 3:14