Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 13

Timoteyo Ankafuna Kuthandiza Anthu

Timoteyo Ankafuna Kuthandiza Anthu

Timoteyo anali mnyamata yemwe ankakonda kuthandiza anthu. Iye anayenda malo ambirimbiri kuti azithandiza anthu ndipo zimenezi zinapangitsa kuti azikhala moyo wosangalala. Kodi ungakonde kudziwa zimene ankachita?—

Agogo komanso amayi ake a Timoteyo ankamuphunzitsa za Yehova

Timoteyo anakulira mumzinda wina, dzina lake Lusitara. Ali mwana, agogo ake, omwe dzina lawo linali Loisi, ndi mayi ake, omwe dzina lawo linali Yunike, ankamuphunzitsa za Yehova. Timoteyo atakula ankafuna kuthandiza anthu ena kuti nawonso adziwe za Yehova.

Timoteyo adakali mnyamata, Paulo anamupempha kuti aziyenda naye limodzi pokalalikira kumadera ena ndipo anavomera. Iye anali wokonzeka kupita kulikonse kuti akathandize anthu.

Timoteyo anapita ndi Paulo ku mzinda wina, dzina lake Tesalonika, womwe unali ku Makedoniya. Pa ulendowu, anafunika kuyenda pansi mtunda wautali kenako n’kukwera bwato. Atafika kumeneko, anathandiza anthu ambiri kudziwa za Yehova. Koma anthu ena anawakwiyira ndipo ankafuna kuwamenya. Choncho Paulo ndi Timoteyo anachoka n’kumakalalikira kwina.

Timoteyo ankakhala mosangalala

Pambuyo pa miyezi ingapo, Paulo anamupempha Timoteyo kuti abwerere ku Tesalonika kukaona mmene abale akumeneko alili. Timoteyo anafunika kulimba mtima kuti apitenso kumzinda woopsawo. Koma Timoteyo anapitabe chifukwa ankadera nkhawa abale a mumzindawo. Pamene ankabwerera kwa Paulo anabwera ndi uthenga wabwino. Anamuuza kuti abale a ku Tesalonika ali bwino komanso zinthu zikuwayendera bwino mwauzimu.

Timoteyo anagwira ntchito limodzi ndi Paulo kwa zaka zambiri. Pa nthawi ina Paulo analemba kuti panalibe munthu wina wabwino kuposa Timoteyo, amene angamutumize kukalimbikitsa mipingo. Timoteyo ankakonda Yehova komanso anthu.

Kodi iweyo umakonda anthu ndipo umafuna kuwathandiza kudziwa za Yehova?— Ngati umatero udzakhala wosangalala kwambiri ngati Timoteyo.