PHUNZIRO 12
Kodi Mungatani Kuti Muyandikire Mulungu?
1. Kodi Mulungu amamvetsera mapemphero onse?
Mulungu akuuza anthu amitundu yonse kuti amuyandikire kudzera m’pemphero. (Salimo 65:2) Komabe sikuti iye amamvetsera kapena kuyankha mapemphero onse. Mwachitsanzo, mapemphero a mwamuna amene amachitira nkhanza mkazi wake angatsekerezedwe. (1 Petulo 3:7) Komanso pamene Aisiraeli ankapitirizabe kuchita zinthu zoipa, Mulungu anakana kumva mapemphero awo. Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kwambiri kulankhula ndi Mulungu m’pemphero. Ndipotu Mulungu amamva mapemphero, ngakhale a munthu amene wachita tchimo lalikulu, ngati munthuyo walapa.—Werengani Yesaya 1:15; 55:7.
Onerani vidiyo yakuti Kodi Mulungu Amamvetsera Mapemphero Onse?
2. Kodi tiyenera kupemphera motani?
Pemphero ndi mbali ya kulambira kwathu. Choncho tiyenera kupemphera kwa Yehova yekha, yemwe ndi Mlengi wathu. (Mateyu 4:10; 6:9) Komanso tikudziwa kuti ndife opanda ungwiro, choncho tiyenera kupemphera m’dzina la Yesu popeza kuti iye anatifera chifukwa cha machimo athu. (Yohane 14:6) Yehova safuna kuti tizingobwereza mapemphero amene tinawaloweza kapena amene analembedwa penapake. Iye amafuna kuti tizipemphera kuchokera pansi pa mtima.—Werengani Mateyu 6:7; Afilipi 4:6, 7.
Mlengi wathu amamva ngakhale mapemphero a mumtima. (1 Samueli 1:12, 13) Iye amafuna kuti tizipemphera nthawi zonse. Mwachitsanzo, tingapemphere pogona, podzuka, tisanayambe kudya chakudya, kapena pamene takumana ndi mavuto.—Werengani Salimo 55:22; Mateyu 15:36.
3. N’chifukwa chiyani Akhristu amasonkhana pamodzi?
Kuyandikira Mulungu si chinthu chophweka chifukwa choti m’dziko limene tikukhalamoli muli anthu omwe sakhulupirira Mulungu ndipo amanyoza lonjezo lake loti padziko lapansi padzakhala mtendere. (2 Timoteyo 3:1, 4; 2 Petulo 3:3, 13) Choncho timafunika kusonkhana ndi abale athu kuti tizilimbikitsana.—Werengani Aheberi 10:24, 25.
Kucheza ndi anthu okonda Mulungu kumatithandiza kuti timuyandikire. Misonkhano ya Mboni za Yehova imatipatsa mwayi woti tilimbikitsidwe ndi chikhulupiriro chimene anzathu ali nacho.—Werengani Aroma 1:11, 12.
4. Kodi mungatani kuti muyandikire Mulungu?
Kuganizira mozama zimene mwaphunzira kuchokera m’Mawu a Mulungu kungakuthandizeni kuti muyandikire Yehova. Muyenera kuganiziranso zimene iye wachita, malangizo amene wapereka komanso malonjezo ake. Kupemphera komanso kuganizira zimenezi mozama, kungakuthandizeni kuti muziyamikira kuchokera pansi pa mtima chikondi cha Mulungu komanso nzeru zake.—Werengani Yoswa 1:8; Salimo 1:1-3.
Munthu angayandikire Mulungu pokhapokha ngati amamudalira komanso kumukhulupirira. Komabe chikhulupiriro chimafunika kuchilimbitsa nthawi zonse. Choncho muzichilimbitsa nthawi zonse poganizira zifukwa zimene zimakuchititsani kuvomereza zimene mumaphunzira.—Werengani Mateyu 4:4; Aheberi 11:1, 6.
5. Kodi kuyandikira Mulungu kungakuthandizeni bwanji?
Yehova amakonda anthu omwe amamukonda. Iye angawateteze ku chinthu chilichonse chomwe chingawononge chikhulupiriro chawo komanso chiyembekezo chawo cha moyo wosatha. (Salimo 91:1, 2, 7-10) Komanso amatichenjeza kuti tisamachite zinthu zomwe zingawononge thanzi lathu komanso zomwe zingatibweretsere mavuto. Yehova amatiphunzitsa kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu.—Werengani Salimo 73:27, 28; Yakobo 4:4, 8.