Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 94

Kupemphera Komanso Kudzichepetsa Ndi Zinthu Ziwiri Zofunika Kwambiri

Kupemphera Komanso Kudzichepetsa Ndi Zinthu Ziwiri Zofunika Kwambiri

LUKA 18:1-14

  • FANIZO LA MKAZI WAMASIYE YEMWE ANALI WAKHAMA

  • FANIZO LA MFARISI NDI WOKHOMETSA MSONKHO

Yesu anali atauza kale ophunzira ake fanizo lowathandiza kumvetsa kufunika kolimbikira kupemphera. (Luka 11:5-13) Pa nthawiyi Yesu ayenera kuti anali ku Samariya kapena ku Galileya ndipo anafotokozanso za kufunika kosasiya kupemphera. Iye anachita zimenezi powauza fanizo kuti:

“Mumzinda winawake munali woweruza wina amene anali wosaopa Mulungu ndiponso wosasamala za munthu. Koma mumzindawo munali mkazi wina wamasiye ndipo anali kupitapita kwa woweruza uja kukamupempha kuti, ‘Ndiweruzireni mlandu wanga ndi munthu amene akutsutsana nane, kuti pachitike chilungamo.’ Kwa kanthawi ndithu woweruzayo sankafuna, koma pambuyo pake ananena mumtima mwake kuti, ‘Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kusamala za munthu, ndionetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa mkazi wamasiyeyu. Ndichita zimenezi kuti asapitirize kumangobwera ndi kundisautsa kwambiri, chifukwa mkazi ameneyu akundivutitsa mosalekeza.’”—Luka 18:2-5.

Pofotokoza tanthauzo la fanizoli, Yesu ananena kuti: “Mwamvatu zimene woweruzayo ananena ngakhale kuti anali wosalungama! Ndithu, ngakhale kuti Mulungu amalezera mtima osankhidwa ake, kodi sadzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iwo, amene amafuulira kwa iye usana ndi usiku?” (Luka 18:6, 7) Kodi pamenepa Yesu anasonyeza kuti Atate ake ndi otani?

Yesu sankatanthauza kuti Yehova Mulungu ndi wofanana ndi woweruza wosalungama uja. Mfundo ya Yesu inali yakuti: Ngati woweruza wosalungama anavomera kuthandiza munthu yemwe ankamuchonderera, ndiye kuti Mulungu adzathandiza aliyense womuchonderera. Yehova ndi wolungama komanso wabwino ndipo adzayankha mapemphero a anthu ake ngati anthuwo sangasiye kupemphera. Tikutero chifukwa cha zimene kenako Yesu ananenanso kuti: “Ndithu ndikukuuzani, [Mulungu] adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iwo mwamsanga.”—Luka 18:8.

Nthawi zambiri anthu sachitira chilungamo anthu osauka ndiponso anthu wamba koma amakondera anthu amene ali ndi udindo komanso olemera. Koma Mulungu sachita zimenezi. Nthawi yoweruza ikadzakwana, Mulungu adzachita zinthu mwachilungamo poonetsetsa kuti anthu oipa alangidwa ndipo atumiki ake alandira moyo wosatha.

Kodi ndi ndani masiku ano amene ali ndi chikhulupiriro ngati mkazi wamasiye uja? Kodi ndi anthu angati amene amakhulupirira kuti Mulungu “adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iwo mwamsanga”? Yesu atamaliza kunena fanizo lofotokoza za kufunika kolimbikira kupemphera, anauzanso ophunzira akewo kufunika kokhala ndi chikhulupiriro popemphera. Iye anawafunsa kuti: “Mwana wa munthu akadzafika, kodi adzapezadi chikhulupiriro padziko lapansi?” (Luka 18:8) Yesu ananena zimenezi pofuna kusonyeza kuti nthawi imene adzabwere mwina anthu ambiri sadzakhala ndi chikhulupiriro.

Anthu ena amene ankamvetsera Yesu ankadziona kuti ali ndi chikhulupiriro. Ankakhulupirira kuti iwowo ndi olungama kuposa anthu ena. Anthu amene anali ndi maganizo amenewa Yesu anawauza fanizo lakuti:

“Anthu awiri anapita m’kachisi kukapemphera. Mmodzi anali Mfarisi, winayo anali wokhometsa msonkho. Mfarisi uja anaimirira ndi kuyamba kupemphera mumtima mwake. Iye anati, ‘Mulungu wanga, ndikukuyamikani chifukwa ine sindili ngati anthu enawa ayi. Iwo ndi olanda, osalungama ndi achigololo. Sindilinso ngati wokhometsa msonkho uyu. Ine ndimasala kudya kawiri pa mlungu ndipo ndimapereka chakhumi pa zinthu zonse zimene ndimapeza.’”—Luka 18:10-12.

Afarisi ankadziwika ndi khalidwe lodzionetsera kuti ndi olungama ndipo ankachita zimenezi kuti azigometsa anthu ena. Nthawi zambiri ankakonda kusala kudya Lolemba ndi Lachinayi, omwe anali masiku a msika, ndipo ankachita zimenezi n’cholinga choti anthu ambiri aziwaona. Afarisiwa ankaonetsetsanso kuti apereka chakhumi cha timbewu ting’onoting’ono. (Luka 11:42) Miyezi ingapo m’mbuyomo, Afarisiwa ananena mawu omwe anasonyeza kuti ankanyansidwa ndi anthu wamba. Iwo anati: “Koma khamu lonseli la anthu osadziwa Chilamulo [malinga ndi mmene Afarisiwo ankawaonera] ndi lotembereredwa.”—Yohane 7:49.

Yesu anapitiriza kufotokoza fanizoli kuti: “Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Anali kungodziguguda pachifuwa ndi kunena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima munthu wochimwa ine.’” Wokhometsa msonkhoyo anavomereza machimo ake moti Yesu anamaliza ndi kunena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Munthu ameneyu anapita kwawo ataonedwa kukhala wolungama kwambiri kusiyana ndi wina uja, chifukwa aliyense wodzikweza adzam’nyazitsa, koma wodzichepetsa adzamukweza.”—Luka 18:13, 14.

Pamenepa Yesu anasonyeza kufunika kokhala wodzichepetsa. Zimene Yesu ananenazi zinali zothandiza kwambiri kwa ophunzira ake chifukwa ophunzirawo anakulira m’dera limene munali Afarisi omwe ankadziona kuti ndi olungama komanso omwe ankalimbikitsa kuti kukhala ndi udindo n’kofunika kwambiri. Ndipotu malangizo amenewa ndi othandiza kwa otsatira onse a Yesu.