MUTU 125
Atamugwira Anapita Naye kwa Anasi Kenako kwa Kayafa
MATEYU 26:57-68 MALIKO 14:53-65 LUKA 22:54, 63-65 YOHANE 18:13, 14, 19-24
-
ANAPITA NDI YESU KWA ANASI AMENE KALE ANALI MKULU WA ANSEMBE
-
KHOTI LA SANIHEDIRINI LINAIMBA MLANDU YESU MOPANDA CHILUNGAMO
Anthu amene anagwira Yesu, anamumanga ngati chigawenga ndipo anapita naye kwa Anasi yemwe anakhalapo mkulu wa ansembe m’mbuyomu. Anasi anali pa udindowu pa nthawi imene Yesu anadabwitsa anthu omwe ankaphunzitsa m’kachisi Yesuyo ali wamng’ono. (Luka 2:42, 47) Patapita nthawi ana ena a Anasi anakhala akulu a ansembe koma pa nthawiyi Kayafa yemwe anali mpongozi wake ndi amene anali mkulu wa ansembe.
Pamene Yesu anali kunyumba kwa Anasi, Kayafa anasonkhanitsa oweruza a m’khoti la Sanihedirini. Khoti la Sanihedirini linkapangidwa ndi oweruza 71 ndipo ena mwa oweruzawa anali mkulu wa ansembe komanso anthu ena omwe anakhalapo pa udindowu m’mbuyomu.
Anasi anafunsa Yesu “za ophunzira ake ndi za chiphunzitso chake.” Yesu anayankha kuti: “Ndalankhula poyera ku dzikoli. Nthawi zonse ndinali kuphunzitsa m’masunagoge ndi m’kachisi, kumene Ayuda onse anali kusonkhana, ndipo sindinalankhule kanthu mseri. N’chifukwa chiyani mukufunsa ine? Funsani amene anamva zimene ndinali kunena kwa iwo.”—Yohane 18:19-21.
Ndiyeno mmodzi wa alonda amene anaimirira chapafupi anamenya Yesu mbama n’kunena kuti: “Ungamuyankhe choncho wansembe wamkulu?” Yesu ankadziwa kuti sanalakwe chilichonse ndiye anayankha kuti: “Ngati ndalankhula molakwika, pereka umboni wa cholakwikacho. Koma ngati ndalankhula moyenera, n’chifukwa chiyani ukundimenya?” (Yohane 18:22, 23) Kenako Anasi analamula kuti Yesu apite naye kwa mpongozi wake Kayafa.
Pamene Yesu ankafika ndi gulu la anthulo n’kuti mkulu wa ansembe, akulu komanso alembi omwe
ankapanga khoti la Sanihedirini atasonkhana kale. Anthuwa anakumana kunyumba kwa Kayafa. Malamulo sankalola kuti munthu aziimbidwa mlandu usiku wa tsiku limene ankachita mwambo wa Pasika. Ngakhale kuti anthuwa ankadziwa zimenezi, anaimbabe Yesu mlandu kuti akwaniritse zolinga zawo zoipa.Gululi linaonetseratu kuti linali lokondera. Tikutero chifukwa nthawi ina m’mbuyomo Yesu ataukitsa Lazaro, khoti la Sanihedirini linapangana kuti liphe Yesu. (Yohane 11:47-53) Ndipo pofika tsiku la Pasikali n’kuti patapita masiku angapo kuchokera pamene atsogoleri achipembedzo anapangana kuti agwire Yesu n’kumupha. (Mateyu 26:3, 4) Moti asanayambe kumuzenga mlanduwu, anthuwo anali ataweruza kale m’maganizo mwawo kuti Yesu ndi wolakwa ndipo ayenera kuphedwa.
Kuwonjezera pa kukumana pa tsiku lomwe kunkachitika mwambo wa Pasika, ansembe aakulu komanso anthu ena omwe ankapanga khoti la Sanihedirini sanatsatirenso malamulo chifukwa anapangana zoti apeze anthu oti akapereke umboni wabodza n’cholinga choti aimbe Yesu mlandu. Anapeza anthu ambiri koma anthuwo ankapereka maumboni osiyana. Kenako panabwera anthu awiri omwe ananena kuti: “Ife tinamva iyeyu akunena kuti, ‘Ine ndidzagwetsa kachisi uyu amene anamangidwa ndi manja, ndipo m’masiku atatu okha ndidzamanga wina osati womangidwa ndi manja.’” (Maliko 14:58) Komabe umboni umene anthu awiriwa anapereka sunkagwirizana.
Kenako Kayafa anafunsa Yesu kuti: “Sukuyankha chilichonse? Kodi n’zoona zimene awa akukunenezazi?” (Maliko 14:60) Yesu sanayankhe chilichonse pa zinthu zabodza zimene mboni ziwiri zija zinanena. Ataona kuti sakuyankha, Kayafa yemwe anali mkulu wa ansembe anagwiritsanso ntchito njira ina n’cholinga choti Yesu alankhule.
Kayafa ankadziwa kuti Ayuda ankakwiya kwambiri akamva munthu aliyense akunena kuti ndi Mwana wa Mulungu. Nthawi ina m’mbuyomu Yesu atanena kuti Mulungu ndi Atate wake, Ayuda ankafuna kumupha chifukwa iwo ankaona kuti Yesu ‘akudziyesa wofanana ndi Mulungu.’ (Yohane 5:17, 18; 10:31-39) Chifukwa chodziwa zimenezi, Kayafa anafunsa Yesu mochenjera kuti: “Ndikukulumbiritsa pali Mulungu wamoyo, utiuze ngati ndiwedi Khristu Mwana wa Mulungu!” (Mateyu 26:63) N’zoona kuti Yesu anadzitchula kuti ndi Mwana wa Mulungu. (Yohane 3:18; 5:25; 11:4) Ngati Yesu akanakana zikanaoneka ngati akukana zoti ndi Mwana wa Mulungu komanso kuti ndi Khristu. Choncho anayankha kuti: “Inde ndinedi, ndipo anthu inu mudzaona Mwana wa munthu atakhala kudzanja lamanja lamphamvu. Mudzamuonanso akubwera ndi mitambo yakumwamba.”—Maliko 14:62.
Yesu atangonena zimenezi, Kayafa anang’amba malaya ake n’kunena mokwiya kuti: “Wanyoza Mulungu! Nanga n’kufunanso mboni zina pamenepa? Pano mwadzimvera nokha mmene akunyozera Mulungu. Tsopano inu mukuona bwanji pamenepa?” A khoti la Sanihedirini anagwirizana ndi zimene Kayafa ananena moti anayankha kuti: “Ayenera kuphedwa basi.”—Mateyu 26:65, 66.
Kenako anthu anayamba kunyoza Yesu, kumumenya nkhonya ndipo ena anamumenya mbama komanso kumulavulira. Anamuphimba kumaso ndi kumumenya mbama, kenako anayamba kulankhula monyoza kuti: “Losera. Wakumenya ndani?” (Luka 22:64) Usiku umenewu Mwana wa Mulungu anazunzidwa kwambiri komanso anamuweruza mopanda chilungamo pa mlandu womwe anaweruza mosatsatira malamulo.