MUTU 132
“Ndithudi Munthu Uyu Analidi Mwana wa Mulungu”
MATEYU 27:45-56 MALIKO 15:33-41 LUKA 23:44-49 YOHANE 19:25-30
-
YESU ANAFERA PAMTENGO
-
PAMENE YESU ANKAFA PANACHITIKA ZINTHU ZODABWITSA
Tsopano nthawi inali “cha m’ma 12 koloko” masana, ndipo kunagwa mdima womwe unali wodabwitsa “m’dziko lonselo mpaka 3 koloko masana.” (Maliko 15:33) Mdimawu sunachitike chifukwa cha kadamsana. Kadamsana amachitika mwezi ukangoyamba kumene kuoneka koma zimenezi zinachitika pa nthawi imene anthu ankachita mwambo wa Pasika ndipo pa nthawi imeneyi mwezi umaoneka wathunthu. Mdima umenewu unatenga nthawi yaitali poyerekeza ndi nthawi ya mdima wa kadamsana womwe umangotenga maminitsi ochepa. Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu ndi amene anachititsa mdima umenewu.
Kodi anthu omwe ankanyoza Yesu anatani ataona zimenezi? Nthawi imene kunachita mdimawu azimayi 4 anafika pafupi ndi mtengo umene anapachikapo Yesu. Azimayiwa anali Mariya mayi ake a Yesu, Salome, Mariya Mmagadala ndi Mariya yemwe anali mayi a mtumwi Yakobo Wamng’ono.
Mtumwi Yohane anali ndi mayi ake a Yesu omwe ankalira “chapafupi ndi mtengo wozunzikirapo.” Mariya ankangoyang’anitsitsa mwana wake yemwe anamubereka ndi kumulera, atapachikidwa pamtengo komanso akuvutika ndi ululu. Mariya ankangoona ngati kuti “lupanga lalitali” lalasa moyo wake. (Yohane 19:25; Luka 2:35) Ngakhale kuti Yesu ankamva kupweteka kwambiri, ankaganizira za moyo wa mayi ake. Movutikira kwambiri anayang’ana Yohane ndikuuza mayi akewo kuti: “Mayi, kuyambira lero, uyu akhala mwana wanu.” Kenako anayang’ananso Mariya n’kuuza Yohane kuti: “Kuyambira lero awa akhala mayi ako.”—Yohane 19:26, 27.
Yesu anapatsa mtumwi yemwe ankamukonda udindo wosamalira mayi ake, omwe pa nthawiyi anali mkazi wamasiye. Pa nthawiyi Yesu ankadziwa kuti ana ena a Mariya, omwe anali abale ake, anali asanayambe kumukhulupirira. Choncho pamene Yesu ankapereka udindowu kwa Yohane ankatanthauza kuti Yohane ayenera kusamalira Mariya pa zinthu zauzimu komanso pa zinthu zofunika pa moyo wake wa tsiku ndi tsiku. Pamenepatu Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri.
Mdima uja utangotsala pang’ono kutha, Yesu ananena kuti: “Ndikumva ludzu.” Zimenezi zinakwaniritsa ulosi wina womwe unalembedwa kalekale. (Yohane 19:28; Salimo 22:15) Yesu anazindikira kuti Atate ake sankamutetezanso n’cholinga choti asonyeze kuti ndi wokhulupirika mpaka pa mapeto a moyo wake. Kenako Yesu anafuula mwina mu chilankhulo cha Chiaramu chomwe anthu a ku Galileya ankalankhula kuti: “Eli, Eli, lama sabachthani?” Mawuwa amatanthauza kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?” Anthu ena omwe anaima pafupi naye sanamvetse zomwe ananena moti ananena kuti: “Tamverani! Akuitana Eliya.” Ndiyeno munthu wina anathamanga n’kutenga bango lomwe anaikako chinkhupule chomwe kenako anachiviika m’vinyo wowawasa ndipo anapatsa Yesu kuti amwe. Koma anthu ena ananena kuti: “Mulekeni! Tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.”—Maliko 15:34-36.
Kenako Yesu anafuula kuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!” (Yohane 19:30) Yesu anali atakwaniritsadi zimene Atate wake anamutuma kuti adzachite padziko lapansi. Pamapeto pake Yesu ananena kuti: “Atate, ndikuikiza mzimu wanga m’manja mwanu.” (Luka 23:46) Ponena mawu amenewa Yesu anasonyeza kuti ankapereka moyo wake m’manja mwa Yehova ndipo ankakhulupirira kuti amuukitsa. Kenako Yesu anaweramitsa mutu wake n’kutsirizika.
Yesu atangomwalira kunachitika chivomezi champhamvu chomwe chinaswa miyala. Chivomezichi Mateyu 12:11; 27:51-53.
chinali champhamvu moti manda omwe anali kunja kwa mzinda wa Yerusalemu anatseguka ndipo mitembo ya anthu inaponyedwa kunja. Anthu omwe ankadutsa m’mbali mwa mandawo ataona mitemboyo analowa “mumzinda woyera” ndipo anauza anthu zomwe anaona.—Yesu atangomwalira, chinsalu chachikulu chomwe chinkasiyanitsa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa chinang’ambika pakati, kuchokera pamwamba mpaka pansi. Zimene zinachitikazi zinasonyeza kuti Mulungu anakwiyira anthu amene anapha Mwana wake komanso zinatanthauza kuti tsopano anthu anali ndi mwayi wopita kumwamba, komwe ndi Malo Oyera Koposa.—Aheberi 9:2, 3; 10:19, 20.
Anthu amene anaona zimene zinachitika Yesu atamwalira anachita mantha ndipo mpake kuti anachitadi mantha. Kapitawo wa asilikali amene analipo pamene Yesu ankaphedwa ananena kuti: “Ndithudi munthu uyu analidi Mwana wa Mulungu.” (Maliko 15:39) N’kutheka kuti msilikaliyu analipo pa nthawi imene Pilato ankaweruza Yesu pa mlandu woti ndi Mwana wa Mulungu. Koma tsopano anali ndi umboni woti Yesu sanalakwe chilichonse komanso kuti ndi Mwana wa Mulungu.
Anthu ena amene anaona zomwe zinachitikazo anabwerera ku nyumba zawo “akudziguguda pachifuwa” posonyeza kuti ali ndi chisoni komanso manyazi. (Luka 23:48) Ena anthu amene ankaona zochitikazo chapatali anali azimayi amene nthawi zina ankayenda ndi Yesu. Zinthu zodabwitsa zimene zinachitikazo zinawalimbikitsa kwambiri.