Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 12

Yakobo Analandira Madalitso

Yakobo Analandira Madalitso

Isaki ali ndi zaka 40 anakwatira Rabeka ndipo ankamukonda kwambiri. Patapita nthawi, iwo anabereka ana amuna awiri amapasa.

Wamkulu dzina lake anali Esau ndipo wamng’ono anali Yakobo. Esau ankakonda kupita kutchire n’kumakasaka nyama. Koma Yakobo ankakonda kukhala pakhomo.

Pa nthawiyo bambo akamwalira, mwana wamkulu ndi amene ankapatsidwa malo aakulu komanso ndalama zambiri za banjalo. Zimene ankapatsidwazo zinkatchedwa kuti cholowa. M’banja la Isaki cholowa chimenechi chinkaphatikizapo zinthu zimene Yehova analonjeza Abulahamu. Esau sankaganizira kwambiri za malonjezo amenewa koma Yakobo ankaona kuti malonjezowo ndi ofunika kwambiri.

Tsiku lina Esau anapita kokasaka ndipo anabwerako atatopa kwambiri komanso ali ndi njala. Atafika anapeza Yakobo akuphika mphodza ndipo anamva kununkhira kwa mphodzazo. Iye anauza Yakobo kuti: ‘Ndigawireko pangʼono mphodza zofiira zimene ukuphikazo, njala yandipha kwabasi.’ Yakobo anamuyankha kuti: ‘Ndikugawira, koma undilonjeze kaye kuti ndidzalandira madalitso ako.’ Ndiyeno Esau anati: ‘Inetu za madalitsozo ndilibe nazo ntchito. Tenga madalitsowo. Ine chimene ndikufuna ndi kudya basi.’ Kodi ukuganiza kuti pamenepa Esau anachita bwino? Ayi. Tikutero chifukwa iye anasinthanitsa chinthu chofunika kwambiri ndi mbale ya chakudya.

Isaki atakalamba, inali nthawi yoti apereke madalitso kwa Esau poti ndiye anali wamkulu. Koma Rabeka anathandiza Yakobo, mng’ono wake wa Esau, kuti alandire madalitsowo. Esau atazindikira kuti Yakobo walandira madalitso ake, anakwiya kwambiri ndipo ankafuna kupha m’bale wakeyo. Isaki ndi Rabeka anafuna kuteteza Yakobo choncho anamuuza kuti: ‘Pita ku Harana kwa amalume ako a Labani. Ukakhale komweko mpaka mtima wa Esau utakhala m’malo.’ Yakobo anamvera zimene makolo ake ananenazi ndipo anathawira ku Harana.

“Kodi munthu angapindule chiyani ngati atapeza zinthu zonse zamʼdzikoli koma nʼkutaya moyo wake? Kapena kodi munthu angapereke chiyani choti asinthanitse ndi moyo wake?”​—Maliko 8:36, 37