Chifukwa Chimene Muyenera Kupeŵera Kukhulupirira Mizimu
Chifukwa Chimene Muyenera Kupeŵera Kukhulupirira Mizimu
NGATI inu anakuphunzitsani kuti mitundu ina ya kukhulupirira mizimu ndizo njira zolankhulirana ndi mizimu yabwino, zingakudabwitseni kudziŵa zimene Baibulo limanena za kukhulupirira mizimu. Mwachitsanzo, ilo limati: ‘Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nawo.’—Levitiko 19:31; 20:6, 27.
Komanso, Baibulo limafotokoza za munthu amene amakhulupirira mizimu kuti “Yehova anyansidwa naye.” (Deuteronomo 18:11, 12) Chifukwa chiyani? Kupenda mosamalitsa zimene Baibulo limanena zokhudza mbali imodzi yaikulu ya kukhulupirira mizimu, yotchedwa kulankhula ndi akufa, kudzayankha funso limeneli.
Kodi Akufa Ali ndi Moyo?
Mosiyana ndi zimene anthu ambiri amaganiza, Mawu a Mulungu, Baibulo, amaphunzitsa kuti n’kosatheka kuti anthu alankhulane ndi okondedwa awo akufa. Chifukwa chiyani
kuli kosatheka? Eya, ngati munthu angalankhule ndi akufa, ndiye kuti akufawo ayenera kukhala ndi moyo. Payenera kukhala mbali inayake ya thupi lawo imene imapulumuka imfa. Ena amati mzimu umakhalabe ndi moyo thupi likafa. Kodi zimenezo n’zoona?Nkhani ya m’Baibulo ya chilengedwe cha munthu imati: ‘Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.’ (Genesis 2:7) Kodi zimenezi sizikuvumbula kuti munthuyo ndiye moyo ndi kuti iye alibe mzimu wosafa umene umakhalabe ndi moyo thupi likafa? Ndiponso, Malemba amanena kuti: “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” (Ezekieli 18:4) “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, . . . pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda.”—Mlaliki 9:5, 10.
Choncho malinga ndi zimene Baibulo limanena, mzimu si chinthu chinachake chimene sichimafa pa imfa ya thupi kotero kuti anthu pambuyo pake n’kumalankhula nacho. Nazi zitsanzo ziŵiri za akatswiri ophunzira Baibulo amene afikira ponena kuti moyo umafa. Katswiri wa zaumulungu wa ku Canada Clark H. Pinnock anati: “Lingaliro limeneli [lakuti mzimu wa munthu sumafa] lasonkhezera maphunziro azaumulungu kwanthaŵi yaitali, koma si kuti ndi la m’Baibulo. Baibulo siliphunzitsa za kusafa mwa chibadwa kwa mzimu.” Mofananamo, katswiri wina wamaphunziro wa ku Britain John W. Stott ananena kuti: “Kusafa ndi kusakhoza kuwonongeka kwa mzimu n’chiphunzitso chachigiriki osati cha m’Baibulo ayi.”
Komabe, anthu amalandiradi mauthenga ndiponso kumva mawu amene amamveka ngati akuchokera kwa womwalira uja. Nangano, amalankhulayo ndani?
Kodi Amalankhula ndi Yani?
Baibulo limasimba kuti munthu wauzimu wosaoneka anagwiritsa ntchito njoka, monga momwe katswiri wolankhulitsa chidole amachitira, kuti alankhulane ndi mkazi woyamba, Hava, zomwe zinam’chititsa kuti apandukire Mulungu. (Genesis 3:1-5) Baibulo limatcha munthu wauzimu kapena mngelo ameneyu kuti “njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse.” (Chivumbulutso 12:9) Satanayo, anapambana pa kunyengerera angelo ena kuti apanduke. (Yuda 6) Angelo oipa ameneŵa amatchedwa ziŵanda ndipo ndi adani a Mulungu.
Baibulo limasonyeza kuti ziŵanda zili ndi mphamvu yosonkhezera anthu. (Luka 8:26-34) N’chifukwa chaketu n’zosadabwitsa kuti Chilamulo cha Mulungu chimati: “Asapezeke mwa inu munthu . . . wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.” (Deuteronomo 18:10-12) Kodi kuipa kwa kunyalanyaza lamuloli n’kotani?
Zochitika zenizeni m’moyo wa Mfumu Sauli ya Israyeli wakale zimayankha funso limenelo. Chifukwa choopa adani ake, Mfumu Sauli anafunafuna wobwebweta. Iye anapempha mkazi wobwebwetayo kuti alankhulane ndi mneneri Samueli yemwe anali atafa. Sauli pomva mmene wobwebwetayo analongosolera za mwamuna wokalamba, iye anakhulupirira kuti maonekedwe ofotokozedwawo analidi a Samueli. Kodi uthenga umene Sauli analandira unali wotani? Israyeli anali kudzaperekedwa m’manja mwa adani, ndipo Sauli ndi ana ake akakhala ndi “Samueli,” kusonyeza kuti iwo adzafa. (1 Samueli 28:4-19) Kodi Mulungu anachitapo chiyani pa zomwe Sauli anachita kukafunsira kwa wobwebweta? Malemba amatiuza kuti: “Sauli anafa, chifukwa cha kulakwa kwake . . . ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta.” (1 Mbiri 10:13) Zinalidi zopweteka bwanji!
Mofananamo lerolino, anthu amene amakhulupirira mizimu amadziika pangozi yoopsa. Baibulo limachenjeza kuti [“okhulupirira mizimu,” NW] adzafa “imfa yachiŵiri [kapena kuti yosatha].” (Chivumbulutso 21:8; 22:15) Ndiyeno, n’zachionekere kuti, njira yabwino kutsatira ndiponso yopulumutsa moyo ndiyo kupeŵa kukhulupirira mizimu kwa mtundu wina uliwonse.
Mmene Mungapeŵere Mizimu Yoipa
Bwanji nanga ngati munayamba kale kukhulupirira mizimu? Mudzachita bwino kusazengereza kutsatira njira zodzitetezera nokha ndi banja lanu kuti musavulazidwe ndi mizimu yoipa. Njira zotani? Nali fanizo: Kodi munthu amateteza bwanji nyumba yake ku nsikidzi? Pambuyo pa kuzichotsa m’nyumba yakeyo, iye amachotsa zinthu zonse zimene zimaitana nsikidzizo. Amamata ming’alu ndiponso kukonzanso makoma a nyumbayo kuti nsikidzizo zisaloŵenso, ndipo ngati mliri wa nsikidziwo ukupitirizabe, iye angathe kukapempha chithandizo kwa aboma kuti adzathane ndi vutolo.
Kuchita zofananazo kungakuthandizeni kupeŵa mizimu yoipa ndiponso kulekana nayo bwinobwino. Taganizirani chitsanzo cha Akristu a m’zaka za zana loyamba ku Efeso amene anali kukhulupirira mizimu asanakhale Akristu. Ataganiza mofatsa kuti asiye kukhulupirira mizimu, iwo anachita zinthu zitatu pofuna kudziteteza iwo eni kuti mizimu yoipa isawagwire ngati nsikidzi. Kodi iwo anachita zotani?
Choyamba
Baibulo limalongosola kuti: “Ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo, nawatentha pamaso pa onse.” (Machitidwe 19:19) Mwa kutentha mabuku awo onse azamatsenga, Akristu atsopanowo anapereka chitsanzo kwa onse amene akufuna kupeŵa mizimu yoipa lerolino. Tayani zinthu zonse zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu. Izi zingaphatikizepo mabuku, magazini, mabuku azithunzithunzi, mavidiyo, zikwangwani, zinthu zapakompyuta, ndi nyimbo zojambulidwa zimene n’zamizimu, ndiponso zithumwa kapena zinthu zina “zodzitetezera” nazo—Deuteronomo 7:25, 26; 1 Akorinto 10:21.
Munthu wina ku South America amene anali kukhulupirira mizimu zedi kwa zaka zambiri analabadira uphungu wa m’Malemba umenewu. “Tsiku lina,” iye anakumbukira motero, “ndinasonkhanitsa zinthu zamizimu zonse n’kuzitulutsa panja pa nyumba yanga, ndinatenga nkhwangwa, n’kuziduladula.” Kenako anatentha chilichonse kufikira zonse zinatha. Atachita zimenezi anapita patsogolo kwambiri mwauzimu ndipo posapita nthaŵi anakhala mtumiki wakhama mu mpingo wina wa Mboni za Yehova.
Komabe, njira yoyambayo siyokwanira. N’chifukwa chiyani tikutero? Eetu, ngakhale pambuyo pa zaka zingapo Akristu a ku Efeso aja atawononga mabuku awo azamatsenga, mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Kulimbana kwathu tilimbana . . . ndi a uzimu a choipa.’ (Aefeso 6:12) Ziŵanda zinali zisanasiyebe. Zinali kufunafunabe kuti zipezenso mwayi. Kodi n’chiyaninso chimene Akristuwo anafunika kuchita?
Chachiŵiri
Paulo analimbikitsa Aefeso a m’zaka za zana loyambawo kuti: “Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11) Langizo limeneli likugwirabe ntchito lerolino. Mofanana kwambiri ndi munthu amene akuyesetsa kuthana ndi nsikidzi m’nyumba mwake, Mkristu ayenera kulimbitsa chitetezo chake chonga khoma kuti mizimu yoipa isamugwire. Kodi njira yachiŵiriyi imaphatikizapo chiyani?
Paulo anatsindika kuti: ‘Koposa zonse mudzitengerenso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’ (Aefeso 6:16) Ndithudi chikopa chimenechi n’chofunika zedi. Ngati chikhulupiriro chanu n’cholimba, ndiye kuti kukana kwanu mizimu yoipa kudzakhala kwamphamvu.—Mateyu 17:20.
Ndiyeno, kodi mungalimbitse motani chitetezo chanu? Mwa kupitirizabe kuphunzira kwanu Baibulo. Kodi phunziro la Baibulo likugwirizana bwanji ndi chikhulupiriro? Eya, mofanana ndi mmene kulimba kwa khoma komwe kumadalira pa kulimba kwa maziko ake, chimodzimodzinso kulimba kwa chikhulupiriro cha munthu komwenso kumadalira kwambiri pa maziko ake. Kodi maziko ameneŵa n’chiyani?
Chidziŵitso cholondola cha Mawu a Mulungu. Mtumwi Paulo analongosola kuti: “Chikhulupiriro chidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mawu a Kristu.” (Aroma 10:17) Mukupemphedwa kufunsira phunziro la Baibulo laulere kwa a Mboni za Yehova, panthaŵi ndi malo amene mungafune. Phunziro ngati limeneli lidzalimbitsa chikhulupiriro chanu. (Aroma 1:11, 12; Akolose 2:6, 7) Zotsatira zake n’zotani? Posapita nthaŵi chikhulupiriro chanu chidzakhala linga lolimba lomwe lidzakutchinjirizani ngati chikopa ku mphamvu ya mizimu yoipa.—Salmo 91:4; 1 Yohane 5:5.
Kodi njira yachitatu yomwe Akristu a ku Efeso aja anayenera kutsata n’njotani?
Chachitatu
Mu Efeso wakale okhulupirira atsopanowo anatsatira ndithu njira za kukana mizimu yoipa, koma Akristuwo anali kukhalabe mu mzinda wodzala ndi uchiŵanda. Iwo anafunika chitetezo chowonjezereka. Chotero pamene mtumwi Paulo analembera okhulupirira anzake, iye anawauza chochita kuti: “Mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthaŵi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse.”—Aefeso 6:18.
Ndithudi, kupemphera ndi mtima wonse komanso nthaŵi ndi nthaŵi kaamba ka chitetezo cha Yehova kunali, ndipo kudakali, njira yotsimikizika yomwe n’njofunika zedi kuti mutetezedwe ku mizimu yoipa. Ndipo n’kosangalatsa kudziŵa kuti Yehova adzayankha zopempha zanu zochokera pansi pa mtima mwa kukupatsani chitetezo chake, chomwe chimaphatikizapo chichirikizo cha angelo ake. (Salmo 34:7; 91:2, 3, 11, 14; 145:19) Choncho, n’kofunika kwambiri kuchita khama kupemphera kwa Mulungu kuti, “Mutipulumutse kwa woipayo.”—Mateyu 6:13; 1 Yohane 5:18, 19.
Antônio, yemwe kale anali wobwebweta ku Brazil, anafikira pozindikira kufunika kwa pemphero. Atavomereza phunziro la Baibulo ndi kuphunzira dzina la Mulungu, lakuti Yehova, iye anayamba kupemphera mwamphamvu kwa Yehova Mulungu kuti amasuke ku zikhulupiriro za mizimu. Poganizira zakale, iye anati: “Kupemphera kwa Yehova kwatsimikizira kukhala pothaŵira panga ndiponso pa anthu ena ambiri omwe m’mbuyomu anali muukapolo wa mizimu yoipa.”—Miyambo 18:10.
Mungathe Kupambana
Pambuyo pakuti mwam’dziŵa Yehova, n’kofunika kuti muzim’khulupirira kotheratu, kugonjera ulamuliro wake, ndiponso kumvera malamulo ake. Ngati mutachita zimenezi, ndiye kuti pamene mumuitana kugwiritsa ntchito dzina lake kuti akuthandizeni, iye adzakutetezani. Antônio analandira chitetezo ngati chimenechi. Lero ndi mkulu wachikristu mumpingo wina wa Mboni za Yehova ku São Paulo ndipo akuyamikira kuti anapeza choonadi chimene chinam’masula.—Yohane 8:32.
Mofanana ndi Antônio ndiponso anthu ena zikwizikwi omwe kale anali kukhulupirira mizimu koma tsopano akutumikira Yehova Mulungu, inunso mutha kusiya bwinobwino kukhulupirira mizimu. Choncho, chotsani zinthu zonse zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu, limbitsani chikhulupiriro chanu mwa kuphunzira Baibulo ndiponso pemphererani chitetezo cha Yehova. Tsatirani njira zimenezi, pakuti moyo wanu ukudalira pa izo!
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Malinga ndi zimene Baibulo limanena, anthu amoyo sangalankhule ndi akufa
[Chithunzi patsamba 6]
1. Chotsani zinthu zonse zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu
[Chithunzi patsamba 7]
2. Pitirizani kuphunzira Baibulo
[Chithunzi patsamba 8]
3. Pempherani mwamphamvu ndiponso nthaŵi ndi nthaŵi