Kodi Akristu Ayenera Kuganiza Kuti Mulungu Azingowateteza?
Lingaliro la Baibulo
Kodi Akristu Ayenera Kuganiza Kuti Mulungu Azingowateteza?
Nthaŵi zambiri Baibulo limanena kuti Mulungu amatha kuteteza anthu om’lambira kuti asagwe m’mavuto. Mfumu Davide anati: “Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa.” (Salmo 140:1) Masiku ano anthu ambiri olambira Mulungu amene anakumanapo ndi chiwawa, umbanda, kapena masoka achilengedwe anachita kupulumuka lokumbakumba. Ena akhala akudzifunsa ngati Mulungu ndiye anawateteza mozizwitsa panthaŵi zimenezo, makamaka akamaganiza kuti pali anthu ena oopa Mulungu omwe anagwa m’mavuto aakulu, ngakhale kufa imfa yowawa.
KODI Yehova Mulungu amateteza anthu ena kuti asagwe m’vuto koma ena n’kuwasiya kuti agwe m’vuto? Kodi masiku ano tiyenera kuganiza kuti Mulungu angatilanditse mozizwitsa anthu akafuna kutivulaza kapena pamene tikugwa m’tsoka?
Nkhani za M’Baibulo Zosimba Kutetezedwa Mozizwitsa
Baibulo lili ndi nkhani zambiri zofotokoza mmene Mulungu anathandizira anthu ake om’lambira. (Yesaya 38:1-8; Machitidwe 12:1-11; 16:25, 26) Malemba amalongosolanso kuti nthaŵi zina Yehova sanawalanditse atumiki ake kuti tsoka lisawagwere. (1 Mafumu 21:1-16; Machitidwe 12:1, 2; Ahebri 11:35-38) Motero, n’zachidziŵikire kuti Yehova amachita kufuna kuti ateteze anthu pachifukwa kapena cholinga chinachake iye akakonda kuti zitero. Motero Mkristu wina aliyense atapanda kulanditsidwa paziyeso, asamafulumire kuganiza kuti Mulungu wamuiwala. Tiyenera kuvomereza kuti kunja kuno anthu amakumana ndi zovuta, ngakhale atakhala atumiki okhulupirika a Yehova. Kodi n’chifukwa chiyani zili choncho?
Chifukwa Chimene Atumiki a Mulungu Okhulupirika Amakumana ndi Zovuta
Chifukwa chimodzi n’chakuti tonsefe tinabadwa tili ndi uchimo ndiponso opanda ungwiro kuchokera kwa Adamu ndi Hava. Motero, Aroma 5:12; 6:23) Chifukwa china n’chakuti tikukhala m’masiku otsiriza. Baibulo limati anthu masiku ano ndi “opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino.” (2 Timoteo 3:1-5) Kuchuluka kwa khalidwe la kugwirira akazi, kuba anthu, kuphana, ndi nkhanza zina zotere kukuikira umboni wa zimenezi.
timakumana ndi zowawa, zosautsa, komanso imfa. (Atumiki a Mulungu okhulupirika ambiri amakhala ndiponso kugwira ntchito pamodzi ndi anthu achiwawa ndipo nthaŵi zina anthuŵa amawavutitsa. Tingakhale pangozi yaikulu chifukwa chongoti tapezeka pamalo olakwika ndiponso panthaŵi yolakwika. Komanso timakumana ndi zimene Solomo analongosola kuti ‘nthaŵi ndi zochitika zongotigwera mwadzidzidzi zimatigwera tonsefe.’—Mlaliki 9:11, NW.
Kuphatikizanso pamenepo, mtumwi Paulo ananena kuti Akristu adzazunzidwa chifukwa cholambira Mulungu. Iye anati: “Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.” (2 Timoteo 3:12) M’zaka zaposachedwapa zimenezi zachitikadi m’mayiko angapo.
Motero, anthu oopa Mulungu si kuti sangakhudzidwe ndi mavuto amene amakhalapo chifukwa cha chiwawa, kuphwanya lamulo, masoka achilengedwe, kapena imfa yongochitika mwatsoka. Satana wakhala akuyesa kugwiritsa ntchito mfundo yakuti Yehova amawatchinjiriza anthu ake motero sakumana ndi zovuta zilizonse m’moyo. (Yobu 1:9, 10) Izi si zoona ayi. Komabe sitikukayika kuti ngakhale Yehova atapanda kutipulumutsa mozizwitsa kutsoka, iye amatiteteza ndithu anthu akefe.
Mmene Yehova Amatetezera Anthu Ake Masiku Ano
Yehova amapereka malangizo oteteza anthu ake kudzera m’Mawu ake. Kukonda zinthu zauzimu ndiponso kudziŵa bwino Baibulo kungatipatse nzeru ndiponso maganizo abwino, zimene zingatithandize kuti tipeŵe kulakwitsalakwitsa tikamachita zinthu zilizonse ndiponso kuti tizichita zinthu mwanzeru. (Salmo 38:4; Miyambo 3:21; 22:3) Mwachitsanzo, kumvera malangizo a m’Baibulo pankhani ya chiwerewere, umbombo, ukali, ndi chiwawa kwapulumutsa Akristu ambiri kuti asagwe m’mavuto ochuluka zedi. Komanso posakondana kwambiri ndi anthu oipa, sitingapezeke wamba m’malo amene mungachitike zoopsa, kapena kuti kupezeka pamalo olakwika komanso panthaŵi yolakwika. (Salmo 26:4, 5; Miyambo 4:14) Anthu amene amachita zinthu mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo, moyo amaumva kukoma kwambiri, ndipo nthaŵi zambiri amakhala okhazikika maganizo ndiponso amakhala athanzi labwino.
Cholimbikitsanso kwambiri ndicho kudziŵa kuti ngakhale Mulungu akalola kuti zinthu zoipa zichitike, iye amapatsanso anthu om’lambira mphamvu zokwanira kuti azipirire. Mtumwi Paulo akutitsimikizira kuti: “Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.” (1 Akorinto 10:13) Baibulo limatilonjezanso “mphamvu yoposa yachibadwa” yotithandiza kupirira zovuta.—2 Akorinto 4:7, NW.
Mulungu Amachita Mmene Akufunira
Kodi Akristu ayenera kuganiza kuti nthaŵi zonse Mulungu angawapulumutse mozizwitsa ngati patachitika ngozi? Zimene zinalembedwa m’Baibulo sizisonyeza choncho.
N’zoona kuti Yehova Mulungu angafune kuchitapo kanthu kuti apulumutse atumiki ake. Ndipo ngati winawake amakhulupirira kuti pangozi inayake anapulumutsidwa ndi Mulungu, sitiyenera kum’tsutsa. Koma Yehova akapanda kufuna kutipulumutsa, sitiyenera kuganiza kuti ndiye kuti sakondwera nafe.
Tisakayike n’komwe ngakhale titakhala pachiyeso kapena pavuto lalikulu bwanji, kuti Yehova amateteza atumiki ake okhulupirika, pochotsa vutolo, potipatsa mphamvu zoti tipirire kapena, ngati titafa, adzatiukitsira kumoyo wosatha m’dziko lake latsopano.—Salmo 37:10, 11, 29; Yohane 5:28, 29.