Kodi Apolisi Ndi Ofunika Chifukwa Chiyani?
Kodi Apolisi Ndi Ofunika Chifukwa Chiyani?
KODI pakanapanda apolisi bwenzi zinthu zili bwanji? Kodi chinachitika n’chiyani m’chaka cha 1997 pamene apolisi okwana 18,000 ananyanyala ntchito yawo mumzinda wa Recife m’dziko la Brazil, motero anthu akumeneko opitirira miliyoni imodzi n’kukhala opanda apolisi?
Nyuzipepala ya The Washington Post inanena kuti: “Pamasiku asanu achisokonezoŵa kulikulu ladzikoli lomwe lili cha kugombe kwa nyanja, anthu ophedwa tsiku lililonse achuluka kuŵirikiza katatu kuposa kale. M’mabanki asanu ndi atatu munabedwa. Magulu a anthu achiwawa akhala akuwomba mfuti n’kumachita zinthu zachiwawa zosiyanasiyana m’sitolo zikuluzikulu ndiponso m’madera ena okhala anthu olemera. Ndipo palibe amene akutsatira malamulo apamsewu. . . . Nthaŵi yachiwawayi yaphetsa anthu ambiri mwakuti anthu ena ophedwa akuchita kusoŵa powaika poyembekeza kuti achibale awo adzawatenge ndipo kuzipatala kukungokhala kodzaza kwambiri ndipo anthu ena a mabala amfuti komanso obayidwa akungogona pansi m’chipatalamo m’njira imene anthu amadutsamo.” Akuti nduna ya zachilungamo inanena kuti: “Kuphwanya malamulo kotereku sikunachitekepo kuno.”
Tikukhala m’dziko limene lili ndi zinthu zoipa zambiri zimene zimangobisika chifukwa cha chitukukochi. Motero timafunikira chitetezo cha apolisi. Inde, tisakane kuti ambirife tamvapo kuti apolisi ena amachita nkhanza, amalandira ziphuphu, amachita mphwayi, ndiponso kupondereza anthu. Zoterezi zimamveka kwambiri m’mayiko ena kusiyana ndi m’mayiko enanso. Komabe kodi tikanatani kukanapanda apolisi? Monga si zoona kuti nthaŵi zambiri apolisi amagwira ntchito zotithandiza? Olemba Galamukani! anafunsa apolisi ena ochokera m’mayiko angapo chifukwa chake anakonda kukhala apolisi.
Ntchito Yothandiza Anthu Kuti Azikhala Mtima Uli M’malo
Wapolisi wina wa ku Britain dzina lake Ivan ananena kuti: “Ndimakonda kuthandiza anthu. Ntchito zosiyanasiyana zimene apolisi
amachita zinandikopa. Anthu ambiri sadziŵa kuti kulimbana ndi anthu ambanda ndi mbali yaikulu ndithu pa ntchito za apolisi. Ntchito yathuyi ndi yothandiza kwambiri anthu kuti azikhala mtima uli m’malo. Nthaŵi zambiri patsiku limodzi lokha ndikayendayenda monga mwantchito yanga, ndimatha kuthandizapo munthu winawake akamwalira mwadzidzidzi, kukachitika ngozi yapamsewu, pakachitika za umbanda, ndiponso ndimatha kuthandiza agogo amene asokonezeka. Makamaka zimakhala zonyaditsa kupereka mwana wotayika kwa makolo ake kapena kuthandiza munthu amene wachitidwa chipongwe ndi anthu ambanda kuti asataye mtima.”Stephen anali wapolisi kale m’dziko la United States. Iye anati: “Anthu akafika kwa iwe akudandaula kuti uwathandize, monga wapolisi umakhala ndi njira zosiyanasiyana ndiponso nthaŵi yakuti uwathandize mwanjira ina iliyonse imene ungathe. Zimenezi n’zimene zinandikopa kuti ndiyambe ntchitoyi. Ndinafuna kuti ndiziwathandiza pa mavuto awo. Mwanjira inayake, ndimaona kuti ndinathandizapo anthu powateteza kwa anthu ambanda. Pazaka zisanu ndinamanga anthu oposa 1,000. Koma kupeza ana otayika, kuthandiza anthu amatenda osokoneza maganizo omwe ankangoyenda popanda cholinga chenicheni ndiponso kugwira magalimoto obedwa, zonsezi zinandipangitsa kukhala munthu wokhutira pantchito yanga. Komanso nthaŵi zina ndinkafunafuna anthu amene tinkawaganizira kuti ndiwo apalamula mlandu winawake ndipo ndinkasangalala kwambiri ndikawagwira.”
Roberto, yemwe ndi wapolisi ku Bolivia ananena kuti: “Ndinkafuna kuti ndizithandiza anthu zinthu zamwadzidzidzi zikawagwera. Ndili wamng’ono, ndinkakhumbira apolisi chifukwa chakuti ankateteza anthu kuti asakumane ndi zoopsa. Poyambirira nditangoyamba kumene ntchito imeneyi ndinali wamkulu wa apolisi ongoyendayenda wapansi pakati pa mzinda pomwe pali maofesi aboma. Pafupifupi tsiku lililonse tinkakhalira kuyang’anira zionetsero zokhudza ndale. Ntchito yanga inali yosungitsa bata. Ndinaona kuti ndikakhala munthu wochezeka ndiponso womvetsa zimene atsogoleri a zionetserozo ankanena ndimatha kuchititsa kuti pasakhale ziwawa zopweteketsa anthu. Izi zinali zokhutiritsa kwambiri.”
Ntchito zimene apolisi amagwira pothandiza anthu n’zambirimbiri. M’mayiko ena, apolisi athandizapo kungoyambira populumutsa amphaka mumtengo mpaka polanditsa anthu amene agwidwa ndi zigaŵenga ndiponso kulimbana ndi anthu akuba m’mabanki. Komabe, kungoyambira nthaŵi imene apolisi amakono anayamba kupezeka, anthu akhala akulimbitsidwa mitima ndiponso kukayikakayika. Nkhani yotsatira ikukamba chifukwa chake zili choncho.
[Zithunzi pamasamba 2, 3]
Pamasamba 2 ndi 3: Kulozera koti magalimoto aloŵere ku Chengdu ku China; apolisi a ku Greece oletsa chiwawa; apolisi a ku South Africa
[Mawu a Chithunzi]
Linda Enger/Index Stock Photography
[Chithunzi patsamba 3]
Apolisi atanyanyala ntchito mumzinda wa Salvador, ku Brazil m’mwezi wa July 2001, anthu anaba m’sitoloyi
[Mawu a Chithunzi]
Manu Dias/Agência A Tarde
[Chithunzi patsamba 4]
Stephen wa ku America
[Chithunzi patsamba 4]
Roberto wa ku Bolivia