Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Amatengeka Mtima Ndi Manambala

Anthu Amatengeka Mtima Ndi Manambala

Anthu Amatengeka Mtima Ndi Manambala

TANGOGANIZIRANI tikanakhala popanda manambala bwenzi ndalama kulibe. Bwenzi malonda akuchitika mongosinthitsana zinthu basi. Nanga maseŵera bwenzi akuyenda bwanji? Popanda manambala, sibwenzi tikutha kuŵerengetsera zigoli komanso sibwenzi tikudziŵa kuti timu iliyonse ili ndi oseŵera angati.

Manambala n’ngothandiza kwambiri, komansotu anthu ena amati ali ndi mphamvu zinazake zodabwitsa. Ichi n’chifukwa chakuti manambala si chinthu choti munthu ungathe kuchiloza ayi. Sitingathe kuwaona, kuwagwira kapena kuwakhudza. Mwachitsanzo: Apulo limakhala ndi mtundu wake, kusalala kwake, kukula kwake, kapangidwe kake, kununkhira kwake ndiponso kakomedwe kake. Mungathe kuona zinthu zimenezi kuti mutsimikizire ngati chinachake chilidi apulo, ndimu, mpira, kapena ngati chili chinthu chinachake. Komatu manambala si mungawatero. Magulu aŵiri osiyana amene onse ali ndi zinthu seveni sangakhale ofanana n’komwe kupatulapo kuti onsewo ali ndi zinthu seveni. Motero mukamvetsa tanthauzo la manambala, mwachitsanzo mukamvetsa kusiyana kwa pakati pa sikisi ndi seveni ndiye kuti mwamvetsa chinthu chovuta kumvetsa kwambiri. Ndipo apa mpamene anthu ena amaloŵetserapo zikhulupiriro zakuti manambala ali ndi mphamvu zinazake zodabwitsa.

Mfundo za Pythagoras Zinasanduka Sayansi Yabodza

Kale anthu ankakonda kutanthauzira manambala m’njira zinazake zapadera. Pythagoras yemwe anali munthu wachigiriki wanzeru kwambiri amene anakhalako cha m’ma 580 mpaka 500 Nyengo Yathu Ino isanakwane, anaphunzitsa anthu kuti zinthu zonse tingathe kuzifotokoza bwinobwino pogwiritsa ntchito manambala. Iyeyu pamodzi ndi anthu otsatira mfundo zake ankanena kuti chilengedwe chonse chimasonyeza dongosolo ndiponso kugwirizana kwa zinthu. Motero kodi sizingathekenso kuti zinthu zonse zimagwirizana m’njira inayake imene tingathe kuiŵerengetsera mwamasamu?

Kuchokera pa nthaŵi ya Pythagoras anthu akhala akutanthauzira manambala polosera zinthu ndi kumasulira maloto komanso kuti asaiwale zinthu. Manambala agwiritsidwa ntchito ndi Agiriki, Asilamu, ndiponso anthu a m’Matchalitchi Achikristu. Pogwiritsa ntchito njira inayake yokhulupirira manambala yotchedwa gematria, Ayuda enaake okhulupirira kuti manambala amanena mauthenga achinsinsi anapatsa zilembo zonse 22 za m’Chihebri nambala yakeyake ndipo potero ananena kuti anapeza matanthauzo amene ali achinsinsi m’Malemba Achihebri.

N’chimodzimodzinso ndi kukhulupirira manambala kwa masiku ano. Nthaŵi zambiri amayambira kuŵerengetsera dzina lanu ndi deti lanu lobadwa. Ndiye chilembo chilichonse cha m’dzina lanu amachipatsa nambala yake. Pophatikiza manambalaŵa komanso manambala a mwezi ndi tsiku limene munabadwa anthu okhulupirira manambala amapeza manambala ofunika kwambiri kwa inuyo. Kenaka amawapatsa matanthauzo enaake manambalawo, ndipo akatero amaganiza kuti apeza zinthu zonse zokhudza inuyo, kuphatikizapo khalidwe lanu, zimene mumalakalaka mumtima mwanu, ndiponso zimene zidzakuchitikireni m’moyo mwanu.

Mwina chimene chimakopa kwambiri anthu kuti azikhulupirira manambala n’chakuti matanthauzo ake amaoneka ngati n’ngolondoladi. Edward Albertson analemba m’buku lake lakuti Prophecy for the Millions kuti: “Anthu ambiri anayamba kukhulupirira manambala chifukwa choona kuti matanthauzo a manambalawo amagwirizanako ndithu ndi eni ake a manambalawo.” Komatu ena amati imeneyi ndi sayansi yabodza. N’chifukwa chiyani amatero? Kodi pali mfundo zimene ziyenera kukupangitsani kukayikira zinthu zimene anthu okhulupirira manambala amanena?

[Bokosi/Zithunzi patsamba 21]

MONGA N’ZOONADI KUTI M’BAIBULO MULI MAUTHENGA ACHINSINSI?

M’buku lake lonena zakuti m’Baibulo muli mauthenga achinsinsi lotchedwa The Bible Code, wolemba nkhani wina dzina lake Michael Drosnin ananena kuti watulukira mauthenga achinsinsi pofufuza mawu a m’Malemba Achihebri pa kompyuta. Iye ananena kuti mauthengawo anali ndi mawu akuti “wachiŵembu amene adzaphe munthu” komanso dzina lakuti Yitzhak Rabin ndipo uthengawu anaupeza kutatsala chaka chimodzi kuti a Rabin amene anali nduna yaikulu ya dziko la Israel aphedwe.

Zinali zosadabwitsa kuona kuti mfundo za m’buku limeneli la The Bible Code anthu ambiri sanagwirizane nazo. Dave Thomas, yemwe ndi katswiri wa masamu komanso sayansi, anasonyeza kuti ngati mutafufuza mawu alionse pakompyuta mungathe kupeza mawu ooneka ngati uthenga wachinsinsi. Atafufuza bwinobwino nkhani yolembedwa ndi Drosnin yemweyo, Thomas anapeza mawu akuti “zachinsinsi,” “zopusa” ndi “zachinyengo.” Thomas anati: “Ngati mutalolera kuwononga nthaŵi yanu ndi mphamvu zanu pofufuza mawu osiyanasiyana mungathe kutulukira uthenga winawake pena paliponse.”

Kompyuta imatha kuŵerengetsera zinthu zambirimbiri motero pophatikiza zilembo zinazake ingathe kupeza mawu enaake amene anthu angaone ngati akulosera zam’tsogolo. Komatu apa zimakhala kuti zinthuzo zangochitika mwangozi ndipo sizitsimikizira kuti m’Baibulo muli mauthenga achinsinsi. *

[Mawu a M’munsi]

[Chithunzi patsamba 20]

Pythagoras anaphunzitsa anthu kuti zinthu zonse zili ndi dongosolo linalake la manambala

[Mawu a Chithunzi]

Mwachilolezo cha National Library of Medicine