Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Sandikonda?

Kodi N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Sandikonda?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi N’chifukwa Chiyani Makolo Anga Sandikonda?

“Bambo anga asanasudzule mayi anga, tinkapitira pamodzi kunyanja, tinkadya kumalesitilanti ndiponso tinkapita kumalo osiyanasiyana pagalimoto yawo. Kenaka zonsezi zinatha. Bambo anga anasinthiratu. Mwina tingati anakhala ngati asudzula ndi ine ndemwe.”—Anatero Karen. *

PALI achinyamata ambiri amene amadandaula motero. Iwo, monga Karen amaona kuti m’modzi mwa makolo awo anasiya kuwakonda kapenanso sanawakondepo n’komwe. Pano sitikunena za kuipidwa kumene kumachitika kwakanthaŵi chabe achinyamata akasiyana maganizo ndi makolo awo ndiponso sitikunena za kukwiya chifukwa chodzudzulidwa ndi makolo. Koma kwenikweni tikunena zimene zimachitika nthaŵi zina makolo akamanyalanyazadi ana awo posawasamalira ndiponso posawapatsa malangizo. Nthaŵi zinanso makolowo amakonda kuzunza anawo kwadzaoneni mwina powanenera mawu a chipongwe kapena kuwamenya kumene.

Kusakondedwa ndi makolo ako n’chinthu chopweteka kwambiri. Karen anati: “Ndinkaona kuti ndine wopanda ntchito kwa iwowo ndiponso kuti sandiganizira n’komwe.” Ngati munakumanapo ndi vuto lotere, taganizirani za mfundo izi zimene zingakuthandizeni kuti musavutike maganizo. Dziŵani kuti ngakhale makolo anu atapanda kumakulimbikitsani zinthu zingakuyenderenibe bwino.

Kuwamvetsa Makolo Anuwo

Mfundo yoyamba n’njakuti muyeneradi kumafuna kuti makolo anu azikukondani. Kholo liyenera kukonda mwana wake mwachibadwa ndiponso mosalekeza monga limachitira dzuŵa posaleka kutuluka tsiku ndi tsiku. Chikondi chotere n’chimene Mulungu amafuna kuti makolo azikhala nacho. (Akolose 3:21; Tito 2:4) Nangano n’chiyani makamaka chimachititsa makolo nthaŵi zina kuti azinyalanyaza, asamaganizire, kapenanso kuti azizunza ana awo?

Chifukwa chimodzi ndicho mmene iwowo anakulira. Tadzifunseni kuti, ‘Kodi makolo anga anaphunzirira kuti zolera ana?’ Nthaŵi zambiri makolo amangotengera zimene makolo awo ankawachitira ali ana. Ndipo nthaŵi zambiri zimenezi zimakhala zoipa chifukwa m’masiku athu ovuta ano, anthu ambiri ndi “opanda chikondi chachibadwidwe.” (2 Timoteo 3:1-5) Nthaŵi zina mapeto ake vutoli limakhala longopatsiranapatsirana, kuchokera kwa makolo amene ankazunzidwa ndi makolo awo n’kumapita kwa ana awo.

Ndiponso nthaŵi zina makolo amakhala osasangalala pazifukwa zosiyanasiyana. Ena amadzipanikiza ndi ntchito, kumwa moŵa mwauchidakwa, kapena kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo pofuna kuiwalako mavuto awo ndiponso zinthu zina zokhumudwitsa. Mwachitsanzo William ndi Joan analeredwa ndi bambo womwa moŵa mwauchidakwa. Joan anati, “Bambo sanali munthu woti angakuyamikire munthu ukachita chinachake chabwino. Koma vuto lawo lalikulu kwambiri linali lakuti atayamba kumwa moŵa ankakonda kwambiri kukalipa. Nthaŵi zina ankangokhalira kukalipira mayi madzulo onse. Nthaŵi zambiri ndinkagwidwa mantha.” Ngakhale makolo otere atapanda kuchita nkhanza moonetsera, mphamvu zawo zimangothera n’kutukwanizanako basi mwakuti sangathenso kuchita zinthu zosonyeza kuti amakonda ndiponso amaganiziradi ana awo.

William amamvetsa chifukwa chimene bambo ake analili munthu wovuta chonchi. Iye analongosola kuti: “Bambo anga anakulira mumzinda wa Berlin, ku Germany m’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse. Ali mwana anakumana ndi mavuto osaneneka ndipo anaona anthu ambiri ophedwa. Tsiku ndi tsiku ankakumana ndi mikwingwirima pofuna kungopeza chakudya chenichenichi. Motero ine ndimaona kuti zimenezi zinawasokoneza mutu kwambiri.” N’zoona kuti Baibulo limavomereza kuti anthu akasautsidwa kwambiri amatha kuchita zinthu mosaganiza bwino.—Mlaliki 7:7.

Kodi William ndi Joan amaona kuti bambo awo anayenera kumavuta pakuti nawonso anavutika ali mwana? William anayankha kuti: “Ayi si choncho. Si kuti popeza anavutika ali mwana ndiye kuti ayenera kumwa moŵa mwauchidakwa ndiponso kuchita zinthu zosayenera. Komabe podziŵa zimenezi ndimawamvetsa bambo angaŵa akamachita zinazake.”

Kuzindikira kuti makolo anu nawonso ndi anthu ndipo amatha kulakwa komanso kudziŵa mmene anakulira kungakuthandizeni kwambiri kuti muwamvetse. Miyambo 19:11 amati: “Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo.”

Zimenezi Zisakuvutitseni Maganizo

Mungathe kuvutika maganizo chifukwa cha mmene zinthu zilili kunyumba kwanu. Mwachitsanzo Patricia ankadziona kuti ndi “wopanda ntchito ndiponso wosati munthu n’kumukonda” chifukwa chakuti makolo ake onse sankamusamalira n’komwe. LaNeisha zinkamuvuta kwambiri kukhulupirira anthu aliwonse aamuna pamene bambo ake anasiya mayi ake iye ali ndi zaka zisanu ndi zitatu zokha. Ndipo chifukwa chosoŵa chikondi cha mayi ake amene “ankangokhalira kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo,” Shayla ankangofuna kuti azikondedwa ndi munthu aliyense amene wakumana naye.

Vuto lina lingakhale ukali komanso nsanje. Karen ataona kuti bambo ake atakwatiranso anayamba kukonda kwambiri ana owapeza kuposa iyeyo, zinam’chititsa kuti akhale ndi “nsanje kwambiri nthaŵi inayake.” Nthaŵi zina Leilani ankaona kuti makolo ake ankamuipira kwambiri. Iye anati: “Ndinkangokangana nawo nthaŵi zonse.”

Zonsezi n’zomveka ndithu malingana ndi mmene zinthu zimakhalira m’mabanja otere. Koma kodi mungatani kuti zimenezi zisamakuvutitseni maganizo? Taonani malingaliro otsatiraŵa.

Yandikirani kwa Yehova Mulungu. (Yakobo 4:8) Mungatero poŵerenga Baibulo panokha komanso posonkhana nthaŵi zonse ndi anthu a Yehova. Mukamaona mmene Yehova amachitira ndi anthu ena, mudzazindikira kuti iye sataya wake. Ndithu mungamukhulupirire. Yehova anafunsa Aisrayeli kuti: “Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wom’bala iye?” Ndiyeno anawalonjeza kuti: “Inde aŵa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.” (Yesaya 49:15) Motero pempherani nthaŵi zonse kwa Mulungu. Mukamapemphera musamavutike kwambiri n’kuganiza mawu oyenerera kwambiri. Iye amakumvetsani. (Aroma 8:26) Muzidziŵa kuti Yehova amakukondani ngakhale zikamaoneka kuti palibe aliyense amene akukukondani.—Salmo 27:10.

Uzaniko munthu wina wachikulire wokhulupirika. Pezani anzanu amene ali okhwima mwauzimu. Auzeni mwatchutchutchu mmene mukumvera komanso zimene zikukudetsani nkhaŵa. Mumpingo wa Mboni za Yehova womwe ndi wachikristu, mungathe kupeza bambo anu ndi mayi anu auzimu. (Marko 10:29, 30) Komabe inuyo ndi amene muyenera kuwatsegulira khomo powauza zakukhosi kwanu. Anthu sangadziŵe mmene mukumvera mutapanda kuwauza. Mudzaona kuti mtima wanu udzabwerera m’malo mwake mukadzauza wina chimene chikukupwetekani.—1 Samueli 1:12-18.

Khalani otanganidwa pothandiza anthu ena. Kuti musadwale maganizo chifukwa chodzimvera chisoni, yesetsani kuiwalako mavuto anu. M’malo mwake muziganizira zinthu zabwino zimene muli nazo. Zinthu zambiri zingakuyendereni bwino ‘posapenyerera zanu za inu nokha, koma popenyereranso za anzanu.’ (Afilipi 2:4) Khalani ndi zolinga zauzimu, ndipo kenako yesetsani kuzikwaniritsa mosakayikira. Kuthandiza ena muutumiki wachikristu ndi njira yabwino kwambiri yoganizira ena osati kumangoganizira za inu nokha.

Pitirizani kulemekeza makolo anu. Nthaŵi zonse kumbukirani kutsatira mfundo za m’Baibulo ndiponso makhalidwe ake abwino. Kulemekeza makolo anu kuli m’gulu la zinthu zimenezi. (Aefeso 6:1, 2) Kuti muwalemekezedi m’njira imeneyi simuyenera kumaipidwa nawo n’kumalakalaka kuwakhaulitsa. Kumbukirani kuti makolo anu ngakhale ataoneka kuti akulakwa motani si ndiye kuti inuyo mungakhoze pochita zinazake zoipa. Motero ingosiyani nkhaniyo m’manja mwa Yehova. (Aroma 12:17-21) Iye “akonda chiweruzo” ndipo ana amawaganizira kwambiri pofuna kuwateteza. (Salmo 37:28; Eksodo 22:22-24) Pitirizani kulemekeza makolo anu mwa kuyesetsa kukhala ndi chipatso cha mzimu wa Mulungu makamaka chikondi.—Agalatiya 5:22, 23.

Zinthu Zingathe Kukuyenderani Bwino

Ndithudi kusakondedwa ndi makolo n’kopweteka kwambiri. Koma musadziwonongere tsogolo lanu chifukwa cha kulephera kwa makolo anu. Mutafuna mungathe kudzakhala ndi tsogolo labwino kwambiri pogwiritsira ntchito mfundo za m’Baibulo tazitchulazi.

William, amene mawu ake tawatchula aja, ndi mtumiki wa nthaŵi zonse pa ofesi ya nthambi ina ya Mboni za Yehova. Iye anati: “Yehova watipatsa zinthu zambiri zotithandiza kuthana ndi mavuto ngati ameneŵa. Ndithu, kukhala ndi Atate wakumwamba wotereyu n’chimwayi chosaneneka.” Mlongo wake, Joan amatumikira nthaŵi zonse monga mpainiya wotumikira kumene kulibe ofalitsa okwanira. Iye anati: “Tili ana tinkatha bwinobwino ‘kuzindikira pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosam’tumikira.’” (Malaki 3:18) “Zimene tinakumana nazo m’moyo wathu zinatilimbikitsa kwambiri kutsatira choonadi n’kumachitenga ngati chathuchathu.”

Nanunso mungachite chimodzimodzi. Baibulo limati, “Akudzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera.” (Salmo 126:5) Kodi lemba limeneli lingakuthandizeni motani pankhaniyi? Lingakuthandizeni m’njira yakuti mukamalimbikira kugwiritsira ntchito mfundo zoyenera pa nthaŵi zovuta, misozi yanu idzasanduka chimwemwe chifukwa Mulungu adzakudalitsani.

Choncho yesetsani kugwirizana kwambiri ndi Yehova Mulungu. (Ahebri 6:10; 11:6) Ngakhale ngati mwavutika kwa zaka zambiri chifukwa cha nkhaŵa, kukhumudwa, ndiponso kudziona ngati wolakwa mungathe kuiwalako zonsezi ndipo m’malo mwake mungathe kukhala ndi “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse.”—Afilipi 4:6, 7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina ena tawasintha.

[Bokosi patsamba 14]

Kodi Mumaona Kuti . . .

• Ndinu wopanda ntchito kwenikweni?

• Kukhulupirira anthu ena n’kopweteketsa ndiponso n’kusaganiza bwino?

• Nthaŵi zonse pochita zinthu mumafuna kuti wina azikulimbikitsani?

• Muli ndi mtima wapachala komanso ndinu wansanje yadzaoneni?

Ngati zimenezi zimakuchitikirani, kambiranani mwamsanga ndi kholo lanu limene mumalikhulupirira, kapena mkulu, kapenanso mnzanu wachikulire mwauzimu.

[Zithunzi patsamba 15]

Chitani zinthu zokuthandizani kuti musamasoŵe mtendere chifukwa cha maganizo