Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungatulukire Zinthu Zopangidwa Mochititsa Chidwi M’chilengedwe

Mungatulukire Zinthu Zopangidwa Mochititsa Chidwi M’chilengedwe

Mungatulukire Zinthu Zopangidwa Mochititsa Chidwi M’chilengedwe

TIKAMAPONDAPONDA powongola miyendo, ambirife timatha kuona kuti chilengedwe n’chokongola. Kaya ndi maluŵa enaake, mbalame inayake yotenga mtima, mtengo winawake wokongola, kapena malo enaake ochititsa kaso. Anthu ambiri amaona kuti zinthu zokongolazi zinapangidwa ndi Mlengi Wamkulu.

Mwina inuyo mumaganiza kuti ndi asayansi okha amene angatulukire zinthu zopangidwa mochititsa chidwi zimenezi za m’chilengedwe. Ayi ndithu si choncho. Kuti muone kukongola kwa chilengedwe si zolira kuti mukhale ndi zida zinazake zapamwamba za sayansi. M’pongofunika kuchita kuikirapo mtima basi, kuziganizira kaye ndiponso kuchita nazo chidwi. M’pofunikanso kuyamba kuchita chidwi ndi zinthu zodziŵika bwino zimene mwina simuima n’kuziyang’anitsitsa.

Mpangidwe umodzi wa zinthu wodziŵika bwino kwambiri ndiwo wangati nkhata. Anthu amapanga zinthu zambiri zodziŵika bwino zampangidwe umenewu monga zingwe zopota ndiponso msomali wa mazinga. Koma pali zinthu zina zokongola kwambiri zopangidwa motere monga zikamba za nkhono zam’nyanja zikuluzikulu ndiponso zibalobalo za mtengo wa paini. Ndipo mukayang’anitsitsa pakati pa duŵa la mpendadzuŵa mumaonapo mpangidwe wangati nkhatawu. Pali zinthu zinanso zonkira komweku monga pakatikati pa maluŵa enaake ndiponso nyumba ya kangaude.

Mukayang’anitsitsa nyumba ya kangaude, muona kuti kangaude amamanga ulusi wa maziko mouyala ngati mmene masipokosi amakhalira kulimu la njinga. Kenaka amapita pakati pamene ulusi wonsewu ukuchokera n’kulumikiza ulusi wonsewo pogwiritsira ntchito ulusi wina wolimba bwino. Ndiye akatero amayamba kuzunguliza ulusiwu mpaka kumaliza nyumba yake yonseyo. Ulusi umene amaluka mozungulizawu ndi umene umadzaoneka ngati kankhatankhata chonchi.

Mpangidwe wina wochititsa chidwi wachilengedwe ndi wa madontho ooneka ngati diso. Madontho ooneka ngati diso amapezeka pazinthu zoti simungaziganizire n’komwe, monga panthenga za mbalame, mapiko a gulugufe, ngakhalenso pamamba a nsomba. Asayansi amanena kuti madontho ooneka ngati disoŵa amathandiza nyamazo pokopana yaimuna ndi yaikazi, popusitsa adani, kapena poopseza nyama zina. Mbalame yotchedwa peacock n’chitsanzo chodziŵika bwino kwambiri pa zinthu zamadontho otere, ndipo zimene tambala wake amachita ndi mapiko ake akamatchetcherera yaikazi n’zodabwitsa kwambiri m’chilengedwe. Alesandro Wamkulu anagoma kwambiri ndi kukongola kwa mbalameyi mwakuti analamula kuti isamaphedwe mu ufumu wake wonse.

Mpangidwe winanso wodziŵika bwino ndiwo mpangidwe wozungulira ndiponso wobulungira. Dzuŵa likamaloŵa limakhala lobulungira komanso lapsuu ndiponso mwezi ukawala umakhala wobulungira ndipotu zonsezi zimatichititsa chidwi kwambiri. Maluŵa ambiri ooneka ngati mpendadzuŵa amaoneka ngati dzuŵa, ndipo pakati pawo pamakhala payelo ndipo m’mphepete mwakemo mumakhala mwa mitundu yonyezimira yosiyanasiyana. Pakati pofiirira pa maluŵa opezeka kulikonseŵa pamakhala timadzi totsekemera timene timakopa agulugufe monga mmene azungu ena amakopekera ndi nyanja.

Popeza kuti n’zotheka kulonga zinthu zambirimbiri m’chinthu cha mpangidwe wobulungira, nthaŵi zambiri zipatso zazikulu ndiponso zamaonekedwe osiyanasiyana zimakhala za mpangidwe umenewu. Mitundu yawo yonyezimira imakopa mbalame, zimene zimadzadya zipatso zake n’kufalitsira nthangala zake kutali.

Inde mpangidwe wangati nkhata, wa dontho langati diso ndiponso wozungulira ndi ina chabe mwa mipangidwe yambirimbiri imene ili m’chilengedwe. Ina mwa mipangidweyi imakhala ndi ntchito yake, koma ina njongokongoletsa kapena kubisa chinthucho. Mulimonsemo, zioneni zinthuzi ndipo muchite nazo chidwi.

[Chithunzi chachikulu patsamba 23]