Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mungatetezere Pathupi Panu

Mmene Mungatetezere Pathupi Panu

Mmene Mungatetezere Pathupi Panu

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU MEXICO

MALINGA ndi zimene linanena Bungwe la United Nations loona za uchembere wabwino, akuti chaka ndi chaka amayi oposa 500,000 amamwalira ndi mavuto okhudzana ndi pathupi. Kuwonjezera pamenepo, bungwe loona za ana la UNICEF linanena kuti chaka chilichonse amayi oposa 60 miliyoni amakumana ndi mavuto oopsa okhudzana ndi pathupi ndipo pafupifupi 20 miliyoni mwa amayi ameneŵa amakhalira kudandaula m’thupi kwa moyo wawo wonse. Amayi ambiri m’mayiko osauka amangotenga mimba n’kumangoberekabereka komanso sadzisamalira, motero amatheratu komanso amakhala odwaladwala. Inde, kukhala ndi pathupi kungakhale koopsa mwinanso kungathe kupha kumene. Koma kodi pali chilichonse chomwe mayi angachite kuti asavutike ndi pathupi pake?

Kukhala Wathanzi Musanatenge Pathupi

Kukonzekera. M’pofunika kuti amayi ndi abambo azikambirana kuchuluka kwa ana amene akufuna kubereka. M’mayiko osauka, sizachilendo kuona amayi akutumbiza mwana wamng’ono. Kukonzekera bwino ndiponso kuganizirana kungathandize kuti mayi akabereka pazipita nthaŵi asanabereke mwana wina, zomwe zingam’patse mpata wopuma, ndipo thanzi lake lingabwereremo panthaŵi imeneyi.

Zakudya. Malinga ndi zimene linanena bungwe lina la ku America lothandiza kutukula miyoyo ya amayi la Coalition for Positive Outcomes in Pregnancy, akuti mayi asanatenge pathupi amafunika kutha miyezi yosachepera inayi osakhudzana ndi zinthu zowononga thanzi, komanso amafunika kuti azidya zamagulu. Mwachitsanzo, khanda lomwe silinabadwe silingagwidwe wamba matenda okhudza msana ngati m’thupi mwa mayiyo muli mavitamini okwanira bwino oteteza msana wa khandalo. Mtsempha wa khanda womwe umapititsa mavitaminiŵa ku msana wa khandalo umatsekeka pakatha masiku 24 kapena 28 mayi atatenga pathupi. Panthaŵiyi amayi ambiri amakhala asanadziŵe n’komwe kuti aima, motero ena omwe akuganiza zobereka amayambiratu kudya zakudya zokhala ndi mavitaminiŵa.

Mavitamini owonjezera magazi amafunikanso kwambiri. Ndipotu mayi akakhala ndi pakati thupi lake limafuna mavitamini a mtunduwu kuŵirikiza kaŵiri. Ngati mavitaminiŵa alipo ochepa m’thupi mwake, mayiyo angadwale matenda osoŵa magazi ndipo zimenezi n’zomwe zimachitikira amayi ambiri a m’mayiko osauka. Vutoli lingakule kwambiri ngati mayi akhala ndi pathupi mobwerezabwereza, popeza kuti sipangakhale nthaŵi yoti mavitaminiŵa abwererenso m’thupi mwake. *

Zaka. Atsikana oyembekezera omwe sanakwanitse zaka 16 angathe kufa mosavuta kusiyana ndi omwe akwanitsa zaka 20. Komanso, amayi omwe apitirira zaka 35 kaŵirikaŵiri amabereka ana ozerezeka. Amayi omwe atenga pathupi ali aang’ono kwambiri kapena atapitirira msinkhu woberekera angathe kukhala ndi vuto la kusayenda bwino kwa magazi m’thupi mwawo. Munthu amadziŵika kuti ali ndi vutoli ngati akuthamanga kwambiri magazi patatha milungu 20 kuchokera pamene anatenga pathupi, komanso akamatupa, ndiponso akamakodza mkodzo wotuwira. Vutoli lingathe kupha mwanayo komanso mayiyo.

Matenda. Munthu akakhala ndi pakati, matenda a m’chikhodzodzo, m’chiberekero, ndiponso m’mimba angakule ndipo angapangitse kuti mwana abadwe masiku ake asanakwane komanso angapangitse kuti magazi asamayende bwino m’thupi. Ngati muli ndi matenda ena alionse ndi bwino kulandiriratu chithandizo musanatenge pathupi.

Kukhala Wathanzi Panthaŵi Yomwe Muli ndi Pathupi

Kulandira chithandizo panthaŵi yoyembekezera. Kupita kuchipatala kaŵirikaŵiri panthaŵi yonse yomwe mayi ali woyembekezera kumachepetsa imfa za amayi apakati. Ngakhale m’mayiko omwe n’kovuta kupita kaŵirikaŵiri kuchipatala, mungathe kupezeka azamba ophunzitsidwa bwino ntchito yawo.

Kulandira chithandizo panthaŵiyi kungapangitse kuti anthu odziŵa ntchitoyi akhale tcheru pa china chilichonse chomwe chingafune chisamaliro chapadera. Izi zikuphatikizapo kuyembekezera mapasa, kuthamanga kwambiri magazi, vuto la mtima ndiponso la impso, komanso matenda a shuga. M’mayiko ena mayi woyembekezera amatha kulandira katemera wa kafumbata pofuna kuteteza khanda lake kuti lisadzadwale kafumbata likabadwa. Mwinanso m’kati mwa miyezi 6 kapena 7 kuchokera pamene anaima, mayiyo angam’pime pofuna kuona ngati ali ndi tizilombo ta matenda monga chibayo. Tizilombo ta matendaŵa, ngati tili m’matumbo a mayiyo, tingadzaloŵe m’thupi la mwanayo panthaŵi imene mayiyo akuchira.

Mayi woyembekezerayo ayenera kukhala wokonzeka kuuza a zachipatala kanthu kalikonse kofunikira kuti adziŵe, kuphatikizapo matenda omwe anadwalapo m’mbuyomo ndiponso mmene anachirira. Ayeneranso kukhala womasuka kufunsa mafunso. M’pofunika kuthamangira kuchipatala ngati mayi woyembekezera akuona zinthu izi: kutaya magazi, kutupa nkhope mwadzidzidzi, kumva litsipa kapena kuphwanya kosalekeza kwa mutu kapena zala, kuchita mdima m’maso mwadzidzidzi, kupotokola m’mimba, kusanzasanza, kuchita chingwangwa, kusintha kwa kutakataka kwa khandalo, kutuluka ukazi, kumva ululu pokodza, kapena kusafuna kukodza.

Mowa ndiponso mankhwala osokoneza ubongo. Mayi akamamwa mowa ndiponso akamagwiritsira ntchito mankhwala osokoneza ubongo (kuphatikizaponso kusuta fodya) m’posavuta kuti ubongo wa khandalo usamadzagwire bwino ntchito, komanso kuti khandalo lidzakhale lopinimbira, kapena lozerezeka. Ana omwe amayi awo ankagwiritsira ntchito kwambiri mankhwala osokoneza ubongo nawonso amakhala ngati anachitapo zimenezi. Ngakhale kuti anthu ena amakhulupirira kuti kumwako mowa mwa apo ndi apo kulibe vuto lililonse, nthaŵi zambiri akatswiri a zaumoyo amanena kuti ndi bwino kusiyiratu mowa panthaŵiyi. Amayi oyembekezera afunikanso kusamala kuti asapume utsi wa fodya amene anthu ena akusuta.

Mankhwala. Mayi woyembekezera asamwe mankhwala ena alionse pokhapokha ngati wapatsidwa ndi dokotala amene akudziŵa za pathupipo ndipo akudziŵa bwino vuto lomwe mankhwalawo angakhale nalo. Mitundu ina ya mankhwala owonjezera mavitamini ingayambitse mavuto ena. Mwachitsanzo, thupi likakhala kuti lili ndi vitamini A wambiri mwanayo angadzabadwe wopunduka.

Kunenepa. Mayi woyembekezera afunika kuyesetsa kuti asakhale wonenepa kapena woonda kwambiri. Malinga ndi zimene linanena buku lina lofotokoza za zakudya lakuti Krause’s Food, Nutrition and Diet Therapy, akuti makanda omwe amabadwa ali onyentchera angathe kumwalira mosavuta kusiyana ndi amene abadwa ali athanzi. Komanso, kudya ndi malingaliro oti ndikudyera anthu aŵiri kumangonenepetsa munthu. Kunenepa kwabwino, komwe kumayamba kuonekera kwambiri kuyambira mwezi wachinayi wa mimba, kumasonyeza kuti mayiyo akudya moyenerera mogwirizana ndi zimene thupi lake likufuna. *

Ukhondo ndiponso zinthu zina zofunika. Munthu angapitirize kusamba monga mwa masiku onse, koma kumasamala ndithu monga mayi woyembekezera. Mayi woyembekezera sayenera kukhudzana ndi munthu aliyense amene ali ndi matenda opatsirana monga chikuku. Komanso pofuna kupeŵa matenda ena ndi ena ogwira ubongo wa makanda, ndi bwino kuyesetsa kusadya nyama yosapsa kapena kusakhudza ndowe za mphaka. Ndi bwino kwambiri kutsatira njira zothandiza paukhondo monga kusamba m’manja ndiponso kutsuka zinthu zomwe timadya zosaphika. Si nthaŵi zonse pamene kugona ndi mwamuna kumabweretsa mavuto, kusiyapo ngati ndi mlungu womalizira wa mimbayo kapena ngati mayi akutaya magazi, kumva kupweteka m’chiuno, kapenanso ngati wapita padera chaposachedwapa.

Kuchira Bwinobwino

Mayi amene amadzisamalira panthaŵi yomwe ali ndi pathupi sakumana ndi mavuto ambiri panthaŵi yochira. Nthaŵi zambiri amakonzeratu ngati akufuna kudzachirira panyumba kapena kuchipatala. Amadziŵanso bwino kwambiri zimene zili m’tsogolo mwake ndiponso amamvera malangizo a mzamba kapena dokotala. Ndiyeno mzamba kapena dokotalayo amadziŵa zomwe mayiyo akufuna, ngati pali mwayi wosankha, pankhani monga mmene mayiyo akufuna kudzakhalira panthaŵi yochira, kung’amba kuti mayiyo abereke bwino, ndiponso kugwiritsira ntchito zipangizo zothandizira pobereka, mankhwala othandiza kuchepetsa ululu, ndiponso makina oonera khanda lisanabadwe. M’pofunikanso kugwirizana pankhani zinanso monga izi: Kodi adzapita kuchipatala chiti ngati kuchirira panyumba kukuvuta? N’chiyani kwenikweni chimene chidzachitike atadzataya magazi kwambiri? Popeza kuti pobereka amayi ambiri amamwalira chifukwa chotaya magazi kwambiri, m’pofunika kukonzekereratu pokhala ndi njira zina zoti n’kugwiritsira ntchito m’malo mwa magazi kwa odwala amene salola kuthiridwa magazi. Komanso, m’pofunika kuganiziriratu zodzachita ngati padzafunike kuchita opaleshoni pochira.

Baibulo limanena kuti ana ndi mphatso, kapena kuti “cholandira” chochoka kwa Mulungu. (Salmo 127:3) Mayi akadziŵa zambiri zokhudza pathupi pake, zinthu zimamuyenderanso bwino. Podzisamalira asanatenge pathupi ndiponso panthaŵi yomwe ali ndi pathupi komanso poganizira mozama zinthu zosiyasiyana zomwe zimafunika pochira, ndiye kuti mayi akuchitadi zonse zotheka kuti asadzavutike akadzakhala ndi pathupi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Zina mwa zakudya zimene zili ndi mavitamini olimbitsa mafupa ndiponso owonjezera magazi ndi chiwindi, ndiwo za m’gulu la nyemba, ndiwo za masamba, mtedza, ndiponso phala lotendera. Kuti thupi ligaye bwino zakudya za mavitamini owonjezera magazi ndi bwino kudyanso zipatso.

^ ndime 16 Mayi amene watenga pathupi ali wathanzi amafunika kuti panthaŵi yochira akhale atawonjezera makilogalamu 9 kapena 12. Komabe, atsikana aang’onoang’ono kapena amayi omwe ali ndi vuto la kupereŵera kwa zakudya m’thupi ayenera kuwonjezera makilogalamu 12 kapena 15, pamene amayi omwe ndi onenepa kwambiri ayenera kuwonjezera makilogalamu 7 kapena 9 basi.

[Bokosi patsamba 14]

MALANGIZO KWA AMAYI APAKATI

● Ndi bwino kuti mayi woyembekezera azidya zinthu monga zipatso, ndiwo zamasamba (makamaka zobiriŵira kwambiri, zachikasu, ndiponso zofiirira), nyemba, soya, nandolo, nsawawa, nsima kapena phala la ufa wa mgaiwa, phala makamaka lotendera, nsomba, nyama ya nkhuku, ya ng’ombe, tchizi, ndi mkaka makamaka wopanda mafuta. Ndi bwino kuchepetsa kudya zinthu za mafuta, shuga, ndiponso za mchere wambiri. Imwani madzi ambiri. Musamamwe zakumwa monga khofi ndiponso musamadye zakudya zomwe zili ndi mankhwala oti zikhalitse ndiponso okometsera. Dothi, mwaye, ndiponso zinthu zina zosadya zingathe kungoyambitsa vuto la kupereŵera kwa zakudya m’thupi ndiponso kungoputa mavuto ena.

● Samalani ndi mavuto ena ndi ena omwe angayambe chifukwa cha zinthu zosiyanasiyana, monga kupita kukaunikidwa ku ekesileyi kaŵirikaŵiri ndiponso mankhwala ena oopsa kwambiri. Chepetsani kugwiritsira ntchito maperefyumu ndiponso mankhwala ena ndi ena ogwiritsira ntchito m’nyumba. Musakhalitse kwambiri m’malo otentha ndiponso masachite maseŵera olimbitsa thupi mopitirira muyeso. Musaimirire nthaŵi yaitali komanso musagwire ntchito kwambiri. Muzimanga malamba moyenerera mukakhala m’galimoto.