Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chomera Chopirira Modabwitsa

Chomera Chopirira Modabwitsa

Chomera Chopirira Modabwitsa

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU NAMIBIA

KAMPWEYA kayeziyezi kakuwomba kuno ku chipululu cha Namib, kummwera cha kumadzulo kwa Africa. Kunja kulibe mtambo ndi umodzi omwe. Dzuŵa likukwera ndipo kunja nako kukumka kutentha. Lino ndi dera lokhala ndi milu ya m’chenga younjikanaunjikana ndiponso zigwa zam’chenga wokhawokha zongoti see chifukwa chowombedwa ndi mphepo. Maso athu akuunguza uku ndi uku pochita chidwi ndi derali. Kodi chinthu icho chikuoneka ngati mulu wa masamba obiriŵiracho n’chiyani? Titayang’ana bwinobwino tikuzindikira kuti chinthucho ndi chimodzi mwa zomera zodabwitsa kwambiri padziko lonse ndipo amachitcha kuti Welwitschia mirabilis. Mbali yachiŵiri ya dzina loperekedwa ndi asayansili, ndi Chilatini ndipo limatanthauza kuti “chodabwitsa.”

Kutchire, chomerachi chimapezeka m’madera a zipululu za ku Angola ndi ku Namibia kokha basi. N’chosiyana kwambiri ndi zomera zina moti asayansi amachiika m’gulu lakelake la zomera, lomwe muli chomera chokhachi basi. M’buku lake lotchedwa Welwitschia—Paradox of a Parched Paradise, Chris Bornman analemba kuti: “Pa mitundu 375,000 ya zomera zodziŵika kwa anthu, palibe chomera china chomwe chachititsa chidwi kwambiri akatswiri ofufuza za zomera koposa chomera chimenechi ndipo palibenso chomera china chimene anthu avutikana nacho kwambiri chonchi pofuna kuchipezera gulu la zomera loti achiikemo.”

Zomera zimenezi zimaoneka ngati masamba ambirimbiri angomera pamodzi mongozungulira kamtengo, koma kwenikweni chomerachi chili ndi masamba aŵiri okha. Masambaŵa amalenzeka chifukwa cha mphepo ya m’chipululu. Dzina la chomerachi pa chinenero cha Chiafirikana limatanthauza kuti “wamasamba aŵiri sangafe.” Ndipotu dzinali n’lochiyenera kwambiri! Kuno nthaŵi zina masana kumatentha mpaka kufika pa 40 digiri seshasi ndipo usiku kumatha kuzizira kwambiri, komanso kulibe mitengo yoti ingatchingire mphepo zowononga zakunozi. Chomerachi sichidalira mitsitsi yake potenga madzi kuchokera m’nthaka, monga mmene zimachitira zomera zambiri. Chaka chonse, kuchipululu cha Namib kumagwa mvula yosakwana n’komwe mamilimita 25, ndipo nthaŵi zina sikukhala mvula kwa zaka zambirimbiri! Ngakhale kuti zimatere, chomerachi sichileka kukula ndipo masamba ake amakhalabe obiriŵira. Kwa nthaŵi yaitali, asayansi akhala akudabwa kuti zimenezi zimatheka bwanji. Zikuoneka kuti chinsinsi chake chagona pakuti masamba a chomerachi amamwa mame amene amafika kuchipululuchi m’mamaŵa kudzera m’mphepo yochokera kunyanja.

Masamba a chomerachi safota n’kuyamba kumerera atsopano. Masamba aŵiri oyambirirawo amamka akula kwa moyo wonse wa chomeracho. Tsamba lina lotere atalitambasula, anapeza kuti linali lotalika mamita pafupifupi 9! Tangoganizirani mmene masambaŵa angatalikire ngati atapanda kufa n’kuthothoka! Magazini ya zasayansi yotchedwa Veld & Flora, inati: “Chomerachi chitati chikhale kwa zaka 1500 chikhoza kukhala ndi tsamba lalitali [mamita 225].” Koma kodi chomerachi chingakhaledi kwa zaka zambiri chonchi? Buku la The World Book Multimedia Encyclopedia limati: “Chomerachi sichikula msanga ndipo nthaŵi zambiri chimatha kukhala kwa zaka 1,000 kapena mpaka 2,000.”

Ndithudi, chomerachi n’chopirira modabwitsa. Koma kodi ndani anapangitsa kuti chomerachi chizikhala ndi moyo wautali choncho m’malo a nyengo yoipa, achipululu ngati ameneŵa? Kwenikweni, tiyenera kuthokoza Mmisiri wanzeru zonse, amene ali Mlengi, Yehova Mulungu, yemwe analenga “zitsamba [kuti] achite nazo munthu.”—Salmo 104:14.