Kanyanja Kokongola Kwambiri
Kanyanja Kokongola Kwambiri
YOLEMBEDWA KU MEXICO
PAKATI pa dziko la Mexico ndi kachilumba ka Baja California, pali kanyanja kokongola kwambiri. Dzina la kanyanjaka ndi Gulf of California koma kale kankatchedwa kuti nyanja ya Cortés. Malo ambiri m’derali ndi chipululu komanso amiyala. Nthambi ya bungwe la United Nations yoona zamaphunziro, sayansi ndi chikhalidwe inanena kuti malo amenewa ali m’gulu la malo a zachilengedwe ofunika kwambiri padziko lonse. N’chifukwa chiyani malowa ali ofunika kwambiri?
Kanyanja kameneka n’kakatali makilomita 1,000, ndipo m’lifupi n’kamakilomita 153. M’kanyanjaka komanso m’dera lozungulira muli zamoyo zosiyanasiyana ndipo m’mokongola kwambiri. Madzi a m’nyanjayi amachita mafunde aatali pafupifupi mamita 9 chakumpoto, ndipo malire a madzi ake amasinthasintha. Dzuwa limawala bwino panyanja imeneyi ndipo madzi ake ali ndi mchere wofunika, choncho mumakhala zomera ndi zamoyo zosiyanasiyana. Ndipo chifukwa cha zimenezi komanso chifukwa chakuti madzi ake ndi oyera, munthu wina woyenda panyanja, dzina lake Jacques-Yves Cousteau, ananena kuti, “kanyanjaka kakusungira zamoyo zambiri zam’madzi za padziko pano.”
M’kanyanjaka muli mitundu 890 ya nsomba. Pamitundu imeneyi, mitundu 90 imapezeka m’nyanja yokhayi basi. Mpake kuti anthu amati nyanjayi ndi malo ophunzirira zamoyo zam’madzi. N’zomvetsa chisoni kuti zamoyo zina monga mtundu wa anangumi ang’onoang’ono otchedwa Vaquita (kutanthauza kang’ombe m’chisipanishi) zikusowa.
Tianangumi tina timakhala totalika masentimita 150. Timakhala totuwa, kapena tofiirira ndipo timakhala ndi madontho akuda kuzungulira maso ake. Timapezeka m’madzi oderapo pafupi ndi malo amene mtsinje wa Colorado umathira m’nyanjayo. Anthu sadziwa zinthu zambiri zokhudza anangumi amenewa. Ndipotu anangumi amenewa anawatulukira posachedwapa mu 1958, pamene anapeza zigaza zitatu m’mphepete mwanyanja ku chilumba cha Baja California.
Anangumi amenewa alipo ochepa ndipo amatetezedwa chifukwa atsala pang’ono kutha. Ngakhale zili choncho, chaka chilichonse anangumi ambiri amakodwa m’maukonde a asodzi. Ndipo pofuna kuonetsetsa kuti nyama zosowazi zisatheretu, boma la Mexico linakhazikitsa malo otetezera zamoyo omwe mbali yake ina kumakhala anangumi amenewa. M’nyanjayi mulinso zamoyo zina ndipo zina zimachita kubweramo. Nyama zomwe zimapezeka m’nyanjayi ndi monga anangumi, akamba am’madzi, nyama zosiyanasiyana zokhala ngati mvuu, ndiponso nsomba za mitundu yosiyanasiyana.
Kum’mwera kwa nyanjayi, asayansi apezako zamoyo zina zapansi panyanja zimene anthu ambiri sanazionepo. Chifukwa chake n’chakuti nyama zimenezi zimakhala m’phanga linalake m’nyanjamo, lotchedwa Guaymas lomwe n’lozama mamita pafupifupi 2,000. M’phanga limeneli muli akasupe a madzi otentha omwe amathandiza kuti zamoyo zosiyanasiyana zizikhalamo bwinobwino, ngakhale kuti dzuwa silifikamo. Ndipo m’phanga limeneli muli nyongolotsi zinazake zopanda kamwa ndi matumbo. Nyongolotsizi ndi zofiira ndipo zimakhala m’magulu. Zimatha kuima nji pansi panyanjapo komanso zimatha kumavinavina m’madzi otentha kapena ozizira. Pamoyo wake, nyongolotsi iliyonse imadalira tizilombo timene timakhala m’thupi lake. Ndipo tiubweya tofiira ta nyongolotsizi n’timene timathandiza kuti zizipuma.
Ngakhale kuti nyama zina m’nyanjayi zikhoza kutha, nkhani yabwino ndi yakuti sizingatheretu zonse. N’chifukwa chiyani tikutero? N’chifukwa chakuti Mlengi wa zamoyo zimenezi sangalole kuti zingowonongeka basi. Iyeyu amakonda kwambiri dziko lonseli moti posachedwapa adzachitapo kanthu. Adzaliteteza kuti anthu asapitirize kuliwononga ndipo adzalibwezeretsa mwakale monga mmene ankafunira pachiyambi. (Genesis 1:26-28; Chivumbulutso 11:18) Sitingathe n’komwe kuganizira za mmene nyanja ya Gulf of California idzakongolere panthawiyi. N’zoonadi, kuti ngakhale mawu akuti “kukongola” sangadzakhale okwanira kufotokoza maonekedwe a nyanjayi.
[Chithunzi patsamba 25]
Nangumi
[Chithunzi patsamba 25]
Nyongolotsi
[Mawu a Chithunzi patsamba 24]
Satellite view: NASA/The Visible Earth (http://visibleearth.nasa.gov/); reef: © Dirscherl Reinhard/age fotostock
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Beach: Mexico Tourism Board; whale: © Mark Jones/age fotostock; tube worms: © Woods Hole Oceanographic Institution