Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kukhulupirika M’banja N’kutani?

Kodi Kukhulupirika M’banja N’kutani?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Kukhulupirika M’banja N’kutani?

Anthu ambiri amaona kuti anthu okwatirana sayenera kugona ndi amuna kapena akazi ena. Zimenezi n’zogwirizana ndi Baibulo, limene limati: “Ukwati ukhale wolemekezeka pakati pa onse, ndi kama wa ukwati akhale wosaipitsidwa.”—Aheberi 13:4.

KOMA kodi munthu wokhulupirika m’banja amangopewa kugonana ndi amuna kapena akazi ena basi? Nanga bwanji ngati amakhumbira amuna kapena akazi ena? Bwanjinso ngati munthu amacheza kwambiri ndi akazi kapena amuna ena, kodi tinganene kuti ndi wokhulupirika?

Kodi Kukhumbira Akazi Kapena Amuna Ena N’koipa?

Baibulo limasonyeza kuti kugonana kwa mwamuna ndi mkazi okwatirana, sikoipa komanso n’kosangalatsa. (Miyambo 5:18, 19) Koma alangizi ena a zabanja amaona kuti kukhumbira akazi kapena amuna ena sikulakwa. Kodi tinganene kuti zimenezi si zoipa, malinga ngati munthu sakuchita chigololo?

Anthu amakhumbira akazi kapena amuna ena chifukwa chongofuna kusangalala basi. Khalidwe loipa limeneli ndi lotsutsana ndi malangizo amene Baibulo limapereka kwa anthu okwatirana. Mawu a Mulungu amati: “Mkazi asachite ulamuliro pa thupi lake la iye mwini, ulamulirowo ukhale ndi mwamuna wake; mwamunanso asachite ulamuliro pa thupi lake la iye mwini, koma ulamulirowo ukhale ndi mkazi wake.” (1 Akorinto 7:4) Kutsatira malangizo a m’Baibulo amenewa kumathandiza munthu kupewa khalidwe lokhumbira akazi kapena amuna ena. Anthu okwatirana akapewa khalidwe limeneli, amasangalala kwambiri.—Machitidwe 20:35; Afilipi 2:4.

Munthu akamakhumbira mkazi kapena mwamuna wina, amakhala akuganizira zinthu zoipa zimene ngati atazichita zitha kukhumudwitsa kwambiri mnzake. Kodi kukhumbira munthu wina kungachititse munthu kuchita chigololo? Yankho lachidule n’lakuti, inde. Baibulo limasonyeza kuti nthawi zambiri munthu amachita zimene amaganiza. Limati: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako cha iye mwini. Ndiye chilakolako chikatenga pathupi, chimabala tchimo.”—Yakobe 1:14, 15.

Yesu anati: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.” (Mateyo 5:28) Mukamapewa kukhumbira ena, ‘mumatchinjiriza mtima wanu’ ndipo zimenezi zimateteza banja lanu.—Miyambo 4:23.

Pewani Kucheza Molakwika ndi Akazi Kapena Amuna Ena

Kuti banja liziyenda bwino, mwamuna ndi mkazi ayenera kudzipereka ndi mtima wonse. (Nyimbo ya Solomo 8:6; Miyambo 5:15-18) Kodi zimenezi zimatanthauza chiyani? Dziwani kuti sikulakwa kucheza ndi munthu wina aliyense, koma mkazi kapena mwamuna wanu ndi amene muyenera kucheza naye kwambiri. Kukondana kwambiri ndi munthu wina yemwe simunakwatirane naye n’kusakhulupirika, ngakhale kuti simunagonane. *

Kodi zimatheka bwanji kuti munthu ayambe kukondana ndi munthu wina? Zimachitika chifukwa chakuti munthu winayo ndi wooneka bwino kapena womvetsa zinthu kwambiri kuposa mkazi kapena mwamuna wanu. Kucheza kwambiri ndi munthu ameneyo kuntchito kapena malo ena kungachititse kuti muyambe kukambirana zachinsinsi, monga mavuto a m’banja mwanu. M’kupita kwa nthawi mumayamba kudalirana kwambiri. Kucheza kwambiri ndi munthuyo pamaso m’pamaso, pa telefoni, kapena pa Intaneti, kungachititse kuti muyambe kukambirana nkhani zosayenera. Anthu okwatirana ayenera kuonetsetsa kuti nkhani zina azingokamba ndi mwamuna kapena mkazi wawo yekha basi ndipo zolankhula zawozo ziyenera kukhala ‘zachinsinsi.’—Miyambo 25:9.

Musamaganize kuti kucheza kwambiri ndi munthu wina kulibe vuto. Lemba la Yeremiya 17:9 limanena kuti ‘mtima ndi wonyenga.’ Choncho, ngati mumacheza kwambiri ndi mkazi kapena mwamuna wina, dzifunseni kuti: ‘Kodi ena akandifunsa za munthu amene ndimacheza nayeyo ndimabisa kapena kuwakalipira? Kodi mkazi kapena mwamuna wanga atamva zimene timakambirana zingamusangalatse? Kodi ndingamve bwanji ngati mkazi kapena mwamuna wanga atayamba kucheza motere ndi munthu wina?—Mateyo 7:12.

Kucheza mosayenera ndi munthu wina kungawononge ukwati wanu chifukwa chakuti mungazolowerane kwambiri ndi munthuyo mpaka kuchita chigololo. Yesu anachenjeza kuti: “Zachigololo . . . zimachokera mu mtima.” (Mateyo 15:19) Ngakhale ngati simungachite chigololo, zingakhale zovuta kwambiri kuti mkazi kapena mwamuna wanu ayambenso kukukhulupirirani. Mkazi wina, dzina lake Karen, * anati: “Nditadziwa kuti mwamuna wanga akumacheza mobisa pafoni ndi mkazi wina zinandiwawa kwambiri. N’zovuta kukhulupirira kuti iye sanachite naye chigololo. Sindikudziwa ngati ndidzamukhulupirirenso.”

Muzicheza moyenera ndi amuna kapena akazi ena, ndipo ngati mwayamba kukopeka nawo, sinthani kachezedwe kanu. Ngati mwaona kuti kucheza ndi munthu wina kungawononge ukwati wanu, chepetsani kapena siyani kucheza naye. Baibulo limati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala.”—Miyambo 22:3.

Pitirizanibe Kukhala Thupi Limodzi

Mlengi wathu amafuna kuti mwamuna ndi mkazi wake azigwirizana kwambiri. Iye anati mwamuna ndi mkazi “adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Kukhala thupi limodzi sikutanthauza kugonana kokha. Pamafunikanso kukondana kwambiri ndipo zimenezi zingatheke ngati nonse mumaganizirana, mumadalirana, komanso kulemekezana. (Miyambo 31:11; Malaki 2:14, 15; Aefeso 5:28, 33) Malangizo amenewa angathandize kuti mupewe mavuto amene amabwera chifukwa chosakhulupirika m’banja.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Komabe, m’pofunika kudziwa kuti Malemba amati banja lingathe pokhapokha ngati mkazi kapena mwamuna wachita chigololo.—Mateyo 19:9.

^ ndime 14 Maina tawasintha.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi kukhumbira munthu wina kungachititse munthu chigololo?—Yakobe 1:14, 15.

▪ Kodi kucheza kwambiri ndi mkazi kapena mwamuna wina kungawononge ukwati wanu?—Yeremiya 17:9; Mateyo 15:19.

▪ Kodi mungalimbitse bwanji ukwati wanu?—1 Akorinto 7:4; 13:8; Aefeso 5:28, 33.

[Mawu Otsindika patsamba 29]

“Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.”—Mateyo 5:28