Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mzinda wa Bucharest Ndi Wochititsa Chidwi

Mzinda wa Bucharest Ndi Wochititsa Chidwi

Mzinda wa Bucharest Ndi Wochititsa Chidwi

YOLEMBEDWA KU ROMANIA

MUKAONA mzinda wa Bucharest muli patali, chimene chimaonekera kwambiri ndi Nyumba ya Malamulo (1), imene m’nthawi ya ulamuliro wa chikomyunizimu inkatchedwa Nyumba ya Anthu Onse. Nyumba imeneyi imakopa anthu ambiri odzaona malo ndipo ndi imodzi mwa nyumba zikuluzikulu kwambiri padziko lonse.

Nyumba ya Malamulo imeneyi ndi chizindikiro cha mzinda wamakono wa Bucharest. Koma sikuti anthu onse kumeneko amaikonda nyumbayi. Iwo amafuna kuti alendo azionanso nyumba zakale zokongola zimene zili mumzindawu.

Likulu Lakale

Mzinda wa Bucharest unakhala likulu la dziko la Romania m’chaka cha 1862. Ndipo kenako unayamba kutukuka kwambiri. Kunamangidwa nyumba zambiri zokongola zomwe mapulani ake anajambulidwa ndi akatswiri a ku France. Mzindawu unkatchedwanso kuti Munda Wokongola chifukwa unali ndi mapaki, minda ya maluwa ndi zinthu zina zokongola. Mzinda wa Bucharest uli m’gulu la mizinda yoyamba padziko lonse kukhala ndi nyali za mumsewu. Mu 1935, ku Bucharest kunamangidwa Chipilala (2), m’mphepete mwa msewu wokongola wa Kiseleff. Pulani ya chipilalachi anatengera ku chipilala cha ku France chotchedwa Arc de Triomphe, chomwe chili mphepete mwa msewu wa Champs-Élysées ku Paris. Anthu a ku France akafika mu mzindawu ankaona ngati ali kwawo, n’chifukwa chake mzinda wa Bucharest anangoupatsa dzina lakuti Mzinda Waung’ono wa Paris.

Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha, panthawi ya ulamuliro wa chikomyunizimu, mzinda wa Bucharest unasintha kwambiri. Nyumba zambiri zakale zinagwetsedwa ndipo anamangapo nyumba zogona. Kuyambira mu 1960 mpaka 1961, kunamangidwa nyumba zogona zokwana 23,000. Mu 1980, ntchito yomanga Nyumba ya Malamulo inayamba. Nyumbayi inali ndi magetsi okongola kwambiri. Inalinso ndi zipinda zapansi zobisalamo kukaphulika bomba, zotalika mamita 90. Inatenga malo okwana masikweya mita 360,000 ndipo ili ndi nyumba zosanja 12 ndiponso zipinda 1,100. Nyumbayi ndi yaikulu kuwirikiza katatu poyerekeza ndi nyumba yakale yachifumu ya mu mzinda wa Versailles, ku France. Malo aakulu analambulidwa kuti amangepo nyumbayi komanso msewu wake. Msewu umenewu ndi waukulu kwambiri kuposa msewu wa ku France wotchedwa Champs-Élysées. Mzindawu unasintha kwambiri moti anthu sankatha kuzindikiranso kuti ndi mzinda womwe uja.

Koma kwa anthu ambiri a mu mzindawu, nyumbayi imawakumbutsa za mtsogoleri wankhanza, dzina lake Nicolae Ceauşescu. Mtsogoleriyu anayamba kumanga nyumbayi pofuna kuti anthu azidzamukumbukira. Iye analemba ntchito anthu okwana 700 ojambula mapulani. Anthu ena amati, iye analembanso ntchito anthu omanga pafupifupi 20,000, amene ankagwira ntchito mosinthanasinthana usana ndi usiku. Ulamuliro wake utatha mu 1989, nyumbayi inali isanamalizidwe, ngakhale kuti panthawiyi anali atawononga ndalama zopitirira madola 1 biliyoni.

Nyumba Zinanso Zochititsa Chidwi

Mumzindawu mulinso nyumba zina zakale. Anthu amachita nazo chidwi kwambiri chifukwa zimasonyeza mmene nyumba zakale za ku Bucharest zinkaonekera. Ndipo nyumba zakale (3) zimenezi zimasonyeza chikhalidwe chosiyanasiyana cha anthu akumidzi a ku Romania. Nyumbazi, zomwe ndi za anthu osauka ochokera m’madera osiyanasiyana a ku Romania, zinamangidwa pa malo enaake okongola komanso abata, ndipo zilipo zoposa 50. Nyumba zimenezi anazikonzanso n’kupanga malo okongola osungirako zinthu zakale. Nyumba iliyonse payokha ndi yochititsa chidwi, chifukwa ili ndi zinthu monga zipangizo zosiyanasiyana zapakhomo, zogulitsa, ndiponso zinthu zosonyeza mmene pakhomo pa anthu ambiri a ku Romania pankaonekera. Nyumba zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi nyumba za mumzinda wa Bucharest wamakono.

Mumzindawu, si zachilendo kuona nyumba zamakono komanso zakale zitamangidwa moyandikana (4). Mzinda wa Bucharest ndi wochititsadi chidwi chifukwa uli ndi zinthu zakale komanso zamakono.

[Zithunzi patsamba 10]

1 Nyumba ya Malamulo

2 Chipilala

3 Nyumba zakale

4 Nyumba zamakono komanso zakale zitamangidwa moyandikana

[Mawu a Chithunzi]

© Sari Gustafsson/hehkuva/age fotostock