Kodi Pali Vuto Lililonse ndi Kukhalitsa Padzuwa?
Kodi Pali Vuto Lililonse ndi Kukhalitsa Padzuwa?
“Mpweya umene wakuta dziko lapansi ukuwonongedwa ndipo anthu ambiri padziko lonse akumakhalitsa padzuwa. Zimenezi zikuchititsa kuti anthu ambiri azidwala matenda osiyanasiyana a pakhungu, chifukwa dzuwa limakhala ndi cheza choipa.”—ANATERO DR. LEE JONG-WOOK, YEMWE ANALI MKULU WA BUNGWE LOONA ZA UMOYO PADZIKO LONSE.
TSIKU lina, Martin, yemwe ndi mzungu wochokera kumpoto kwa Ulaya, anagona pansi pa mthunzi wa ambulera mphepete mwa nyanja ku Italy. Atadzuka, anapeza kuti pamene anagonapo pafika dzuwa. Miyendo yake inali itafiira kwambiri ndipo inkapweteka. Martin anati: “Miyendo yanga inapsa kwambiri ndi dzuwa ndipo inatupa zedi, moti ndinapita kuchipatala. Patapita masiku atatu, ndinayamba kumva kupweteka kwambiri. Sindinkatha kuimirira kapena kupinda miyendo ndipo miyendoyo inakungika kwambiri moti ndinkangoganiza kuti iphulika.”
Anthu ambiri amaganiza kuti azungu okha, monga Martin, ndi amene sayenera kukhalitsa padzuwa. Komabe, ngakhale kuti khungu la anthu akuda siliwonongeka mwamsanga ndi dzuwa, iwo akhozabe kudwala khansa ya pakhungu. Ndipo sangadziwe msanga kuti ali ndi khansa mpaka itafika poipa kwambiri. Mavuto amene amabwera chifukwa chopsa ndi dzuwa ndi monga kuwonongeka kwa maso komanso kuwonongeka kwa chitetezo cha m’thupi. Zimenezi sizidziwika msanga mpaka patadutsa zaka zambiri.
Anthu amene amakhala m’mayiko otentha kwambiri ndi amene angavulale kwambiri ndi cheza choipa chochokera ku dzuwa. Choncho anthu amene amakhala kapena kupita ku mayiko amenewa, ayenera kukhala osamala kwambiri chifukwa mpweya umene umateteza dzikoli ku cheza choipa ukuwonongedwa kwambiri masiku ano. Tiyeni tione mavuto ena amene amabwera chifukwa chokhalitsa padzuwa.
Kuwonongeka kwa Maso
Pafupifupi anthu 15 miliyoni padziko lonse ndi osaona chifukwa cha ng’ala. Ng’ala ndi imene imachititsa anthu ambiri padziko lonse kukhala akhungu. Vuto limeneli limayamba ngati mbali ya diso yomwe imatithandiza kuona yaphimbika. Munthu amayamba ng’ala ngati amakhala padzuwa nthawi yaitali. Ndipo akatswiri akuti anthu 20 pa 100 aliwonse amene ali ndi ng’ala, inayamba kapena kuwonjezereka chifukwa chokhalitsa padzuwa.
N’zomvetsa chisoni kuti dera limene anthu ambiri amakhala ndi ng’ala likuphatikizapo mayiko amene akungotukuka kumene, komwe anthu ambiri ndi osauka. Choncho anthu ambiri a ku Africa, Asia, Central America, ndi South America ndi a khungu chifukwa sangathe kulipira kuchipatala kuti awapale ng’ala.
Khungu Limawonongeka
Anthu 33 pa 100 aliwonse amene amapezeka ndi khansa, khansa yake imakhala ya pakhungu. Chaka chilichonse, anthu pafupifupi 130,000 amapezeka ndi khansa ya pakhungu yoopsa kwambiri yotchedwa melanoma. Ndipo anthu 2 miliyoni mpaka 3 miliyoni amadwala mitundu ina ya khansa ya pakhungu. Akuti anthu pafupifupi 66,000 amafa ndi khansa ya pakhungu chaka chilichonse. *
Kodi dzuwa limawononga bwanji khungu lanu? Nthawi zambiri, munthu akakhala nthawi yaitali padzuwa, khungu limawauka ndipo kenako limachita matuza kapena kusendeka.
Khungu likawauka ndi dzuwa, maselo ambiri akhungu amafa ndiponso maselo ena am’kati mwa khungu amawonongeka. Ngati khungu la munthu lasintha mtundu chifukwa chokhala padzuwa, chimenechi ndi chizindikiro chakuti khungulo lawonongeka. Munthu angadwale khansa ngati DNA imene imachititsa kuti maselo a khungu azikula yawonongeka. Dzuwa limachititsanso kuti khungu lichite makwinya komanso kuti lizikhala ndi mabala mosavuta.
Chitetezo cha M’thupi Chimawonongeka
Ofufuza ena apeza kuti ngati khungu lamenyedwa ndi cheza choipa cha dzuwa nthawi yaitali, chitetezo cha m’thupi la munthuyo chimachepa kwambiri. Zimenezi zimachititsa kuti thupi lizilephera kumenyana ndi matenda. Munthu angadwale matenda osiyanasiyana ngakhale atakhala padzuwa nthawi yochepa. Anthu ambiri aona kuti dzuwa limawapangitsa kutuluka zilonda pakhungu. Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linanena kuti pali cheza china choipa chimene “chikuoneka kuti chimachepetsa chitetezo cha m’thupi ndiponso chomwe chimachititsa kuti khungu lizituluka zilonda zimene zimachititsa kuti tizilombo toyambitsa matenda tilowe m’thupi mosavuta.”
Choncho, kuti dzuwa liyambitse khansa, chimene chimachitika n’chakuti, choyamba, limawononga DNA imene imachititsa kuti maselo a khungu azikula. Ndipo kenako limachititsa kuti chitetezo cha m’thupi chichepe ndipo thupilo limalephera kulimbana ndi khansayo.
Choncho ndi nzeru kupewa kukhala nthawi yaitali padzuwa, chifukwa kupanda kusamala tikhoza kudwala kapena kufa kumene.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 10 Kuti mumve zambiri zokhudza khansa ya pakhungu, werengani Galamukani! ya June 8, 2005, masamba 3-10.
[Bokosi patsamba 11]
MMENE MUNGADZITETEZERE
▪ Musamakonde kukhala padzuwa 10 koloko m’mawa mpaka 4 koloko masana, chifukwa panthawiyi dzuwa limakhala lamphamvu kwambiri.
▪ Muzikonda kukhala pamthunzi.
▪ Muzivala zovala zosathina komanso zosatentha kwambiri.
▪ Muzivala zipewa zakhonde kuti muteteze maso, makutu, nkhope ndi khosi lanu.
▪ Muzivala magalasi abwino oteteza maso anu ku dzuwa.
▪ Muzidzola mafuta okutetezani ku dzuwa pakatha maola awiri aliwonse.
▪ Muzipewa kugwiritsa ntchito magetsi okhala ndi cheza choipa omwe angasinthe mtundu wa khungu lanu.
▪ Muziteteza kwambiri ana anu chifukwa amakhala ndi khungu lofewa kwambiri.
▪ Musamagone padzuwa.
▪ Mukatuluka matuza pakhungu amene akukukayikitsani, pitani kuchipatala.