‘Limayankha Mafunso Athu’
‘Limayankha Mafunso Athu’
▪ ‘Limayankha mafunso athu.’ Zimenezi ndi zimene achinyamata ena anena zokhudza buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri. Mtsikana wina dzina lake Jessicah, yemwe amakhala ku Texas, U.S.A anati: “Nthawi zambiri ndinkasokonekera maganizo ndipo sindinkadzidalira pochita zinthu. Koma buku limeneli landithandiza kwambiri. Ndalimbikitsidwa kudziwa kuti achinyamata ambiri amakumana ndi mavuto ngati anga akamatumikira Mulungu. Bukuli layankha pafupifupi funso lililonse limene ndinali nalo.”
Breann, yemwe amakhala ku Colorado, anati: “Buku lanu likukwaniritsa cholinga chake chothandiza achinyamata kuti azikambirana ndi makolo awo. Ndikafuna kukambirana ndi mayi anga, ndimangotulutsa bukuli n’kuyamba kuwawerengera nkhani yomwe ndikufunayo. Mnzanga winanso atawerenga bukuli, ananena kuti akufuna kuyamba kukambirana ndi makolo ake.”
Mitu yoyambirira ya bukuli ikuyankha mafunso amene achinyamata amakonda kufunsa okhudza anthu amene si anyamata kapena atsikana anzawo. Katrina, yemwe amakhala ku New Jersey, analemba kuti: “Bukuli landilimbikitsa kwambiri kuti ndisayambe chibwenzi msanga ngakhale ena atandiumiriza kuchita zimenezi. Ndiponso, kudikira kaye kumathandiza kuti munthu uchite zinthu zambiri zofunika. Ndikufuna ndikwaniritse kaye zinthu zimenezi. Ndipo nthawi ikadzakwana yoti ndikhale ndi chibwenzi, sizidzandivuta kupeza munthu woyenera ndiponso sizidzandivuta kuyendetsa chibwenzicho.”
Mukhoza kuitanitsa bukuli polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi, n’kutumiza ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena tumizani ku adiresi yoyenera yomwe ili pa tsamba 5 la magazini ino.
□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.
□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.
[Chithunzi patsamba 32]
Jessicah
[Chithunzi patsamba 32]
Breann
[Chithunzi patsamba 32]
Katrina