Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzigwiritsa Ntchito Zipangizo Zamakono Mwanzeru

Muzigwiritsa Ntchito Zipangizo Zamakono Mwanzeru

Muzigwiritsa Ntchito Zipangizo Zamakono Mwanzeru

Katherine, yemwe ali ndi zaka zoposa 20, amagwiritsa ntchito kompyuta kuntchito kwake. Ndipo akabwerera kunyumba amafikiranso pa Intaneti, pomwe amafufuza ndi kugula zinthu komanso kutumiza mauthenga ambirimbiri. Komabe, anzake ena azaka zocheperapo amagwiritsa ntchito kwambiri Intaneti kuposa iyeyo. Iye anadandaula kuti: “N’chifukwa chiyani nthawi zonse anzangawa amandivutitsa ndi mauthenga achabechabe? Bwanji sandiimbira foni kuti tizilankhulana?”

N’ZOONA kuti kulankhulana pa foni n’kwabwino kuyerekeza ndi kutumizirana uthenga. Komabe, kulankhulana pamasom’pamaso n’kofunika kwambiri. Ngakhale kuti zipangizo zambiri zamakono zinakonzedwa kuti anthu azilankhulana mosavuta, kugwiritsa ntchito zipangizozi sikungapose kucheza pamasom’pamaso. Mfundo za m’Baibulo zotsatirazi zingakuthandizeni kuti muzigwiritsa ntchito zipangizo zamakono mwanzeru.

“Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.” (Mateyo 7:12) Kutsatira mawu a Yesu Khristu amenewa pogwiritsa ntchito foni ndi kompyuta, kungatithandize kulemekeza ena ndi kuwachitira zabwino. Mayi wina dzina lake Anne, anati: “Tsiku lina ine ndi mwamuna wanga tinapita kulesitilanti, ndipo tinakhala pafupi ndi azibambo enaake awiri. Bambo mmodzi ankangolankhula pafoni kwinaku akudya. Mnzakeyo ankatimvetsa chisoni chifukwa ankasowa wocheza naye.” Kodi inuyo mukanakhala mnzake wa bamboyu mukanamva bwanji? Kodi simukanakwiya kapena kukhumudwa? N’zoona kuti tingathe kugwiritsa ntchito foni yam’manja nthawi ina iliyonse, koma tifunikanso kumaganizira ena. Tiyenera kutsatira zimene Yesu ananena zakuti tizichitira ena zimene tingafune kuti iwowo atichitire.

“Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru, podziwombolera nthawi yoyenerera.” (Aefeso 5:15, 16) Nthawi ndi mphatso yofunika kwambiri imene Mulungu anatipatsa ndipo sitiyenera kuiwononga mwachisawawa. Zipangizo zamakono zingatithandize kuti tisamawononge nthawi yambiri. Mwachitsanzo, Intaneti ingatithandize kufufuza zinthu, kusungitsa ndalama kubanki ndiponso kugula zinthu mwachangu. Koma ingakhalenso yosathandiza ngati timathera nthawi yaitali tikufufuza zinthu zosafunikira.

Chinthu chinanso chomwe chingatiwonongere nthawi ndicho kuchita zinthu zambirimbiri nthawi imodzi. Mwachitsanzo, kugwiritsa ntchito kompyuta kwinaku tikuonera TV ndi kulankhula pa foni, kapena kutsegula mapulogalamu ambirimbiri pamene tikutumiza uthenga pa Intaneti n’kosathandiza. N’chifukwa chiyani tikutero?

Dokotala wina wa ubongo, dzina lake Jordan Grafman, anati: “Munthu amene amagwira ntchito zambirimbiri nthawi imodzi, sagwira bwino ntchitoyo poyerekeza ndi munthu amene akugwira ntchito iliyonse payokha.” N’zosatheka kuika maganizo athu pa zinthu zambiri nthawi imodzi chifukwa kuchita zimenezi kumachititsa kuti ntchitoyo isalongosoke. Ndipo magazini ya Time inanena kuti anthu akamasinthasintha maganizo awo kuchoka ku ntchito imodzi kupita ku ina, amalakwitsa zinthu zambiri. Ndipo ntchitoyo “imawatengera nthawi yaitali, mwina kuwirikiza kawiri, kusiyana ndi kumagwira ntchito imodzi nthawi imodzi.” Choncho ngati mukufuna kugwira ntchito zambiri nthawi imodzi, dziwani kuti mutha osamaliza ntchitozo.

“Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwa mtundu uliwonse, chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Chuma, kaya chikhale chochuluka bwanji, sichingatipatse moyo kapena kutithandiza kukhala osangalala. Mulungu ndi amene angatipatse zinthu zimenezi. Yesu anati: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyo 5:3) Anthu ogulitsa malonda amafuna kuti anthu aziganiza kuti angakhale osangalala ngati ali ndi katundu wambiri. Iwo amauza anthu kuti ngati sagula katundu watsopano ndiye kuti akutsalira. Koma musamakopeke ndi zimenezi. Muyenera kuchita zinthu mwanzeru. Muziganizira kaye ngati chomwe mukufuna kugulacho chili chofunikira musanawononge ndalama zanu, zomwe mwina munazipeza movutikira. Muyeneranso kukumbukira kuti zipangizo zambiri zamakono sizichedwa kutha fasho. Choncho, ngati mukufuna chipangizo chinachake, muyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikufunikiradi chipangizochi? Ndipo kodi ndikufunikiradi chipangizo chokhala ndi zinthu zambirimbiri zimene mwina sindingazigwiritse ntchito n’komwe?’

Zimadalira Mmene Mukuzigwiritsira Ntchito

Katherine, yemwe tamutchula kale uja, anakhumudwa kwambiri kompyuta yake itawonongeka. Iye anati: “Poyamba ndinakhumudwa kwambiri koma kenako ndinazolowera ndipo ndinaganiza kuti ndisagulenso ina mwachangu. Patapita mwezi umodzi, ndinaona kuti ndinkakhala ndi nthawi yambiri yochitira zinthu zina ndipo ndinkakhala ndi nthawi yambiri yowerenga. Kuntchito ndili ndi kompyuta, choncho ndimagwiritsa ntchito kompyuta imeneyi kuti ndilankhule ndi anzanga panthawi yopuma. Panopa ndimaona kuti si vuto kukhala wopanda Intaneti ndipo sindidalira kwambiri zipangizo zamakono.”

Kunena zoona, zipangizo zambiri zamakono ndi zabwino ndipo zimathandiza kuti tizichita zinthu mofulumira komanso mosakhetsa kwambiri thukuta. Choncho sikulakwa kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono ngati mukufunikiradi, koma muyenera kutero moganizira ena komanso mosamala. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Muzikonda kwambiri anthu kuposa zipangizozo. Muzipewa kuwononga nthawi ndi ndalama zambiri kugula zinthu zosafunikira kwenikweni. Muzipewanso kuonera zinthu zolaula komanso zachiwawa pa Intaneti ndi pa zinthu zina. Ndipo muzitha kukhala popanda foni kapena kompyuta. Mwachidule tingoti muzigwiritsa ntchito zipangizozi mwanzeru, ndipo muzitsatira malangizo odalirika opezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Baibulo limati: “Yehova apatsa nzeru; kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.”—Miyambo 2:6.

[Bokosi patsamba 9]

MUZIGWIRITSA NTCHITO MOYENERA ZIPANGIZO ZAMAKONO

Kodi mungagwiritse ntchito bwanji foni kapena kompyuta moganizira ena? Onani mfundo zotsatirazi.

▪ Muzipewa kuimba kapena kuyankha foni pamalo amene mungasokoneze ena. Ndiponso nthawi zina ndi bwino kuthimitsa foni yanu.

▪ Ngati zili zotheka, musalole kuti foni yanu ikudodometseni pamene mukukambirana ndi anthu zinthu zofunika.

▪ Mukamalankhula pa foni, muzimvetsera kwambiri zimene akunena.

▪ Si bwino kujambula anthu ndi foni yanu musanawapemphe chifukwa ena zingawachititse manyazi kapena angakuoneni ngati wopanda ulemu.

▪ Muzipewa kutumizira ena uthenga uliwonse womwe mwalandira poganiza kuti iwowo asangalala nawo. N’kutheka kuti anzanuwo sangaone kuti uthengawo ndi wofunika.